Jeremiah 44 (BOGWICC)

1 Uthenga umene Yeremiya analandira wonena za Ayuda onse amene ankakhala ku Igupto, ku mizinda ya Migidoli, Tapanesi ndi Mefisi, ndiponso ku Patirosi ndi uwu: 2 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu mwaona mavuto aakulu amene ndinawabweretsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda munthu wokhalamo. 3 Zimenezi zinachitika chifukwa cha zoyipa zomwe anachita. Iwo anaputa mkwiyo wanga pofukiza lubani ndi potumikira milungu ina imene iwo kapena inu ngakhalenso makolo anu sanayidziwe. 4 Kawirikawiri Ine ndakhala ndikutuma atumiki anga, aneneri, amene anati, ‘Musachite chinthu chonyansachi chimene Ine ndimadana nacho!’ 5 Koma iwo sanamvere kapena kulabadira; sanatembenuke kusiya zoyipa zawo kapena kuleka kufukiza lubani kwa milungu ina. 6 Nʼchifukwa chake mkwiyo wanga unayaka ngati moto kutentha mizinda ya ku Yuda ndi misewu ya mu Yerusalemu ndi kuyisandutsa bwinja mpaka lero. 7 “Ndiye tsopano Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, ‘Chifukwa chiyani mukufuna kudziwononga chotere? Kodi mukufuna kuti amuna, akazi, ana ndi makanda onse aphedwe ndi kuti mu Yuda musatsale ndi munthu mmodzi yemwe? 8 Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga popembedza mafano pofukiza lubani kwa milungu ina mʼdziko lino la Igupto mʼmene mukukhalamo. Kodi mukuchita zimenezi kuti mudziwononge nokha ndi kuti mudzisandutse chinthu choseketsa ndi chonyozeka pakati pa mitundu yonse ya dziko lapansi? 9 Kodi mwayiwala zoyipa zimene anachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi awo, ndiponso zoyipa zimene munachita inuyo ndi akazi anu mʼdziko la Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 10 Koma mpaka lero simunalape. Simunandilemekeze kapena kumvera malamulo anga amene ndinayikira inuyo ndi makolo anu. 11 “Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Ine ndatsimikiza zobweretsa mavuto pa inu ndi kuwatheratu anthu a ku Yuda. 12 Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene atsimikiza zopita ku Igupto ndi kukakhala kumeneko. Onse adzathera ku Igupto. Adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Adzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, chinthu choseketsa ndi chonyozeka. 13 Ndidzalanga Ayuda okhala ku Igupto ndi lupanga, njala ndi mliri, ngati mmene ndinalangira anthu a ku Yerusalemu. 14 Motero mwa anthu amene anapita ku Igupto palibe ndi mmodzi yemwe adzapulumuke, kapena kukhala ndi moyo, kapena kubwerera ku Yuda. Palibe amene adzabwerere kupatula othawa nkhondo.’ ” 15 Tsono amuna onse amene anadziwa kuti akazi awo ankafukiza lubani kwa milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, gulu lalikulu la anthu, pamodzi ndi anthu onse amene amakhala ku Patirosi mʼdziko la Igupto, anati kwa Yeremiya, 16 “Ife sitimvera uthenga umene watiwuza mʼdzina la Yehova! 17 Koma tidzachitadi chilichonse chimene tinanena kuti tidzachita: Tidzafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndipo tidzayipatsa nsembe yachakumwa ngati mmene tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akuluakulu mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Nthawi imeneyo ife tinali ndi chakudya chochuluka ndipo tinali pabwino, sitimapeza mavuto. 18 Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.” 19 Akazi anawonjezera kunena kuti, “Pamene tinkafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza mmene timayipangira mfumukazi yakumwambayo makeke abwino olembapo chinthunzi chake ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa?” 20 Yeremiya atamva kuyankha kumeneku anawawuza kuti, 21 “Kodi mukuganiza kuti Yehova nʼkuyiwala kuti inuyo ndi makolo anu, mafumu anu ndi akuluakulu anu, ndiponso anthu onse, munkafukiza lubani kwa mafano a mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 22 Ndiye Yehova sakanathanso kupirira ndi machitidwe anu ndi zonyansa zimene munkachita. Nʼchifukwa chake dziko lanu linasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa. Dziko lopandamo anthu monga zilili lero lino. 23 Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.” 24 Kenaka Yeremiya anawuza anthu onse, makamaka akazi kuti, “Imvani mawu a Yehova, anthu onse a ku Yuda amene muli mu Igupto. 25 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu ndi akazi anu munalonjeza ndi pakamwa panu, ndipo malonjezowo mwakwaniritsa. Inu munanena kuti, ‘Tidzachita zimene tinalonjeza, kufukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha zakumwa.’ Tsopano chitanitu zimene munalonjezazo! Kwaniritsani malumbiro anu.“Yambani, chitani zimene munalonjeza! Kwaniritsani malumbiro anu! 26 Koma imvani mawu a Yehova, inu Ayuda nonse amene mukukhala mu Igupto: Yehova akuti, ‘Ine ndikulumbira mʼdzina langa lopambana kuti palibe wochokera ku Yuda amene akukhala mu Igupto amene adzatchule dzina langa polumbira kuti, ‘Pali Ambuye Yehova wamoyo.’ 27 Pakuti ndionetsetsa kuti ndiwachitire choyipa, osati chabwino. Anthu a ku Yuda amene akukhala ku Igupto adzaphedwa pa nkhondo. Ena adzafa ndi njala mpaka onse atatheratu. 28 Amene adzapulumuke ku lupanga ndi kubwerera ku dziko la Yuda kuchokera ku Igupto adzakhala ochepa kwambiri. Choncho otsala onse a ku Yuda amene anapita kukakhala ku Igupto adzadziwa kuti mawu woona ndi ati, anga kapena awo. 29 “Ine Yehova ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano. Motero mudzadziwa kuti mawu anga akuti ndidzakulangani ndi woona. 30 Yehova akuti, ‘Ine ndidzamupereka Farao Hofira mfumu ya Igupto kwa adani ake amene akufuna kumupha, monga momwe ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, mdani wake amene ankafuna kumupha.’ ”

In Other Versions

Jeremiah 44 in the ANGEFD

Jeremiah 44 in the ANTPNG2D

Jeremiah 44 in the AS21

Jeremiah 44 in the BAGH

Jeremiah 44 in the BBPNG

Jeremiah 44 in the BBT1E

Jeremiah 44 in the BDS

Jeremiah 44 in the BEV

Jeremiah 44 in the BHAD

Jeremiah 44 in the BIB

Jeremiah 44 in the BLPT

Jeremiah 44 in the BNT

Jeremiah 44 in the BNTABOOT

Jeremiah 44 in the BNTLV

Jeremiah 44 in the BOATCB

Jeremiah 44 in the BOATCB2

Jeremiah 44 in the BOBCV

Jeremiah 44 in the BOCNT

Jeremiah 44 in the BOECS

Jeremiah 44 in the BOHCB

Jeremiah 44 in the BOHCV

Jeremiah 44 in the BOHLNT

Jeremiah 44 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 44 in the BOICB

Jeremiah 44 in the BOILNTAP

Jeremiah 44 in the BOITCV

Jeremiah 44 in the BOKCV

Jeremiah 44 in the BOKCV2

Jeremiah 44 in the BOKHWOG

Jeremiah 44 in the BOKSSV

Jeremiah 44 in the BOLCB

Jeremiah 44 in the BOLCB2

Jeremiah 44 in the BOMCV

Jeremiah 44 in the BONAV

Jeremiah 44 in the BONCB

Jeremiah 44 in the BONLT

Jeremiah 44 in the BONUT2

Jeremiah 44 in the BOPLNT

Jeremiah 44 in the BOSCB

Jeremiah 44 in the BOSNC

Jeremiah 44 in the BOTLNT

Jeremiah 44 in the BOVCB

Jeremiah 44 in the BOYCB

Jeremiah 44 in the BPBB

Jeremiah 44 in the BPH

Jeremiah 44 in the BSB

Jeremiah 44 in the CCB

Jeremiah 44 in the CUV

Jeremiah 44 in the CUVS

Jeremiah 44 in the DBT

Jeremiah 44 in the DGDNT

Jeremiah 44 in the DHNT

Jeremiah 44 in the DNT

Jeremiah 44 in the ELBE

Jeremiah 44 in the EMTV

Jeremiah 44 in the ESV

Jeremiah 44 in the FBV

Jeremiah 44 in the FEB

Jeremiah 44 in the GGMNT

Jeremiah 44 in the GNT

Jeremiah 44 in the HARY

Jeremiah 44 in the HNT

Jeremiah 44 in the IRVA

Jeremiah 44 in the IRVB

Jeremiah 44 in the IRVG

Jeremiah 44 in the IRVH

Jeremiah 44 in the IRVK

Jeremiah 44 in the IRVM

Jeremiah 44 in the IRVM2

Jeremiah 44 in the IRVO

Jeremiah 44 in the IRVP

Jeremiah 44 in the IRVT

Jeremiah 44 in the IRVT2

Jeremiah 44 in the IRVU

Jeremiah 44 in the ISVN

Jeremiah 44 in the JSNT

Jeremiah 44 in the KAPI

Jeremiah 44 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 44 in the KBV

Jeremiah 44 in the KJV

Jeremiah 44 in the KNFD

Jeremiah 44 in the LBA

Jeremiah 44 in the LBLA

Jeremiah 44 in the LNT

Jeremiah 44 in the LSV

Jeremiah 44 in the MAAL

Jeremiah 44 in the MBV

Jeremiah 44 in the MBV2

Jeremiah 44 in the MHNT

Jeremiah 44 in the MKNFD

Jeremiah 44 in the MNG

Jeremiah 44 in the MNT

Jeremiah 44 in the MNT2

Jeremiah 44 in the MRS1T

Jeremiah 44 in the NAA

Jeremiah 44 in the NASB

Jeremiah 44 in the NBLA

Jeremiah 44 in the NBS

Jeremiah 44 in the NBVTP

Jeremiah 44 in the NET2

Jeremiah 44 in the NIV11

Jeremiah 44 in the NNT

Jeremiah 44 in the NNT2

Jeremiah 44 in the NNT3

Jeremiah 44 in the PDDPT

Jeremiah 44 in the PFNT

Jeremiah 44 in the RMNT

Jeremiah 44 in the SBIAS

Jeremiah 44 in the SBIBS

Jeremiah 44 in the SBIBS2

Jeremiah 44 in the SBICS

Jeremiah 44 in the SBIDS

Jeremiah 44 in the SBIGS

Jeremiah 44 in the SBIHS

Jeremiah 44 in the SBIIS

Jeremiah 44 in the SBIIS2

Jeremiah 44 in the SBIIS3

Jeremiah 44 in the SBIKS

Jeremiah 44 in the SBIKS2

Jeremiah 44 in the SBIMS

Jeremiah 44 in the SBIOS

Jeremiah 44 in the SBIPS

Jeremiah 44 in the SBISS

Jeremiah 44 in the SBITS

Jeremiah 44 in the SBITS2

Jeremiah 44 in the SBITS3

Jeremiah 44 in the SBITS4

Jeremiah 44 in the SBIUS

Jeremiah 44 in the SBIVS

Jeremiah 44 in the SBT

Jeremiah 44 in the SBT1E

Jeremiah 44 in the SCHL

Jeremiah 44 in the SNT

Jeremiah 44 in the SUSU

Jeremiah 44 in the SUSU2

Jeremiah 44 in the SYNO

Jeremiah 44 in the TBIAOTANT

Jeremiah 44 in the TBT1E

Jeremiah 44 in the TBT1E2

Jeremiah 44 in the TFTIP

Jeremiah 44 in the TFTU

Jeremiah 44 in the TGNTATF3T

Jeremiah 44 in the THAI

Jeremiah 44 in the TNFD

Jeremiah 44 in the TNT

Jeremiah 44 in the TNTIK

Jeremiah 44 in the TNTIL

Jeremiah 44 in the TNTIN

Jeremiah 44 in the TNTIP

Jeremiah 44 in the TNTIZ

Jeremiah 44 in the TOMA

Jeremiah 44 in the TTENT

Jeremiah 44 in the UBG

Jeremiah 44 in the UGV

Jeremiah 44 in the UGV2

Jeremiah 44 in the UGV3

Jeremiah 44 in the VBL

Jeremiah 44 in the VDCC

Jeremiah 44 in the YALU

Jeremiah 44 in the YAPE

Jeremiah 44 in the YBVTP

Jeremiah 44 in the ZBP