Jeremiah 5 (BOGWICC)

1 “Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu,mudzionere nokha,funafunani mʼmabwalo ake.Ngati mungapeze munthu mmodziamene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi,ndipo ndidzakhululukira mzinda uno. 2 Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’komabe akungolumbira mwachinyengo.” 3 Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona?Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka;munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro.Anawumitsa mitima yawo ngati mwalandipo anakaniratu kulapa. 4 Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe;anthu ochita zopusa.Sadziwa njira ya Yehova,sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna. 5 Tsono ndidzapita kwa atsogolerindi kukayankhula nawo;ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova,amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.”Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehovandipo anadula msinga zawo. 6 Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha,mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga,kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawokuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamopakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulundipo abwerera mʼmbuyo kwambiri. 7 Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita?Ana anu andisiya Inendipo amapembedza milungu imene si milungu konse.Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa,komabe iwo anachita chigololonamasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere. 8 Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa,aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake. 9 Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?”akutero Yehova.“Kodi nʼkuleka kuwulipsiramtundu woterewu? 10 “Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga,koma musakayiwononge kotheratu.Sadzani nthambi zakepakuti anthu amenewa si a Yehova. 11 Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yudaonse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.” 12 Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti,“Yehova sangachite zimenezi!Choyipa sichidzatigwera;sitidzaona nkhondo kapena njala. 13 Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo;ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova.Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.” 14 Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti,“Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa,tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwakondipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu. 15 Inu Aisraeli,” Yehova akuti,“Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali,ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo,mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa,zimene akunena inu simungazimvetse. 16 Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri;onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha. 17 Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu,adzapha ana anu aamuna ndi aakazi;adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu,adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu.Ndi malupanga awo adzagwetsamizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira. 18 “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova. 19 Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.” 20 “Lengeza izi kwa ana a Yakobondipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti, 21 Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,inu amene maso muli nawo koma simupenya,amene makutu muli nawo koma simumva. 22 Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”Akutero Yehova.“Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo. 23 Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;andifulatira ndipo andisiyiratu. 24 Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’ 25 Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;ndipo machimo anu akumanitsani zabwino. 26 “Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipaamene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalamendiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo. 27 Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengongati zikwere zodzaza ndi mbalame.Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera. 28 Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,sateteza ufulu wa anthu osauka. 29 Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?Kodi ndisawulipsiremtundu woterewu?Akutero Yehova. 30 “Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambirichachitika mʼdzikomo: 31 Aneneri akunenera zabodza,ndipo ansembe akuvomerezana nawo,ndipo anthu anga akukonda zimenezi.Koma mudzatani potsiriza?

In Other Versions

Jeremiah 5 in the ANGEFD

Jeremiah 5 in the ANTPNG2D

Jeremiah 5 in the AS21

Jeremiah 5 in the BAGH

Jeremiah 5 in the BBPNG

Jeremiah 5 in the BBT1E

Jeremiah 5 in the BDS

Jeremiah 5 in the BEV

Jeremiah 5 in the BHAD

Jeremiah 5 in the BIB

Jeremiah 5 in the BLPT

Jeremiah 5 in the BNT

Jeremiah 5 in the BNTABOOT

Jeremiah 5 in the BNTLV

Jeremiah 5 in the BOATCB

Jeremiah 5 in the BOATCB2

Jeremiah 5 in the BOBCV

Jeremiah 5 in the BOCNT

Jeremiah 5 in the BOECS

Jeremiah 5 in the BOHCB

Jeremiah 5 in the BOHCV

Jeremiah 5 in the BOHLNT

Jeremiah 5 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 5 in the BOICB

Jeremiah 5 in the BOILNTAP

Jeremiah 5 in the BOITCV

Jeremiah 5 in the BOKCV

Jeremiah 5 in the BOKCV2

Jeremiah 5 in the BOKHWOG

Jeremiah 5 in the BOKSSV

Jeremiah 5 in the BOLCB

Jeremiah 5 in the BOLCB2

Jeremiah 5 in the BOMCV

Jeremiah 5 in the BONAV

Jeremiah 5 in the BONCB

Jeremiah 5 in the BONLT

Jeremiah 5 in the BONUT2

Jeremiah 5 in the BOPLNT

Jeremiah 5 in the BOSCB

Jeremiah 5 in the BOSNC

Jeremiah 5 in the BOTLNT

Jeremiah 5 in the BOVCB

Jeremiah 5 in the BOYCB

Jeremiah 5 in the BPBB

Jeremiah 5 in the BPH

Jeremiah 5 in the BSB

Jeremiah 5 in the CCB

Jeremiah 5 in the CUV

Jeremiah 5 in the CUVS

Jeremiah 5 in the DBT

Jeremiah 5 in the DGDNT

Jeremiah 5 in the DHNT

Jeremiah 5 in the DNT

Jeremiah 5 in the ELBE

Jeremiah 5 in the EMTV

Jeremiah 5 in the ESV

Jeremiah 5 in the FBV

Jeremiah 5 in the FEB

Jeremiah 5 in the GGMNT

Jeremiah 5 in the GNT

Jeremiah 5 in the HARY

Jeremiah 5 in the HNT

Jeremiah 5 in the IRVA

Jeremiah 5 in the IRVB

Jeremiah 5 in the IRVG

Jeremiah 5 in the IRVH

Jeremiah 5 in the IRVK

Jeremiah 5 in the IRVM

Jeremiah 5 in the IRVM2

Jeremiah 5 in the IRVO

Jeremiah 5 in the IRVP

Jeremiah 5 in the IRVT

Jeremiah 5 in the IRVT2

Jeremiah 5 in the IRVU

Jeremiah 5 in the ISVN

Jeremiah 5 in the JSNT

Jeremiah 5 in the KAPI

Jeremiah 5 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 5 in the KBV

Jeremiah 5 in the KJV

Jeremiah 5 in the KNFD

Jeremiah 5 in the LBA

Jeremiah 5 in the LBLA

Jeremiah 5 in the LNT

Jeremiah 5 in the LSV

Jeremiah 5 in the MAAL

Jeremiah 5 in the MBV

Jeremiah 5 in the MBV2

Jeremiah 5 in the MHNT

Jeremiah 5 in the MKNFD

Jeremiah 5 in the MNG

Jeremiah 5 in the MNT

Jeremiah 5 in the MNT2

Jeremiah 5 in the MRS1T

Jeremiah 5 in the NAA

Jeremiah 5 in the NASB

Jeremiah 5 in the NBLA

Jeremiah 5 in the NBS

Jeremiah 5 in the NBVTP

Jeremiah 5 in the NET2

Jeremiah 5 in the NIV11

Jeremiah 5 in the NNT

Jeremiah 5 in the NNT2

Jeremiah 5 in the NNT3

Jeremiah 5 in the PDDPT

Jeremiah 5 in the PFNT

Jeremiah 5 in the RMNT

Jeremiah 5 in the SBIAS

Jeremiah 5 in the SBIBS

Jeremiah 5 in the SBIBS2

Jeremiah 5 in the SBICS

Jeremiah 5 in the SBIDS

Jeremiah 5 in the SBIGS

Jeremiah 5 in the SBIHS

Jeremiah 5 in the SBIIS

Jeremiah 5 in the SBIIS2

Jeremiah 5 in the SBIIS3

Jeremiah 5 in the SBIKS

Jeremiah 5 in the SBIKS2

Jeremiah 5 in the SBIMS

Jeremiah 5 in the SBIOS

Jeremiah 5 in the SBIPS

Jeremiah 5 in the SBISS

Jeremiah 5 in the SBITS

Jeremiah 5 in the SBITS2

Jeremiah 5 in the SBITS3

Jeremiah 5 in the SBITS4

Jeremiah 5 in the SBIUS

Jeremiah 5 in the SBIVS

Jeremiah 5 in the SBT

Jeremiah 5 in the SBT1E

Jeremiah 5 in the SCHL

Jeremiah 5 in the SNT

Jeremiah 5 in the SUSU

Jeremiah 5 in the SUSU2

Jeremiah 5 in the SYNO

Jeremiah 5 in the TBIAOTANT

Jeremiah 5 in the TBT1E

Jeremiah 5 in the TBT1E2

Jeremiah 5 in the TFTIP

Jeremiah 5 in the TFTU

Jeremiah 5 in the TGNTATF3T

Jeremiah 5 in the THAI

Jeremiah 5 in the TNFD

Jeremiah 5 in the TNT

Jeremiah 5 in the TNTIK

Jeremiah 5 in the TNTIL

Jeremiah 5 in the TNTIN

Jeremiah 5 in the TNTIP

Jeremiah 5 in the TNTIZ

Jeremiah 5 in the TOMA

Jeremiah 5 in the TTENT

Jeremiah 5 in the UBG

Jeremiah 5 in the UGV

Jeremiah 5 in the UGV2

Jeremiah 5 in the UGV3

Jeremiah 5 in the VBL

Jeremiah 5 in the VDCC

Jeremiah 5 in the YALU

Jeremiah 5 in the YAPE

Jeremiah 5 in the YBVTP

Jeremiah 5 in the ZBP