John 3 (BOGWICC)

1 Ndipo panali Mfarisi wotchedwa Nekodimo, wa mʼgulu lolamulira la Ayuda. 2 Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.” 3 Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.” 4 Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?” 5 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. 6 Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. 7 Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ 8 Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.” 9 Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?” 10 Yesu anati, “Iwe mphunzitsi wa Israeli, kodi sukuzindikira zimenezi? 11 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu. 12 Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba? 13 Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu. 14 Tsono monga Mose anapachika njoka mʼchipululu, moteronso Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa, 15 kuti aliyense amene akhulupirira Iye akhale ndi moyo wosatha. 16 “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. 18 Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. 19 Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. 20 Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. 21 Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.” 22 Zitatha izi, Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼmadera a ku midzi ya ku Yudeya, kumene Iye anakhala kanthawi akubatiza. 23 Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa. 24 (Apa nʼkuti Yohane asanatsekeredwe mʼndende). 25 Mkangano unabuka pakati pa ophunzira ena a Yohane ndi Ayuda ena pa zamwambo wodziyeretsa wa Ayuda. 26 Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.” 27 Atamva zimenezi, Yohane anayankha kuti, “Munthu amalandira chokhacho chapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba. 28 Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’ 29 Mwini wake wa mkwatibwi ndi mkwati. Ndipo bwenzi lamkwati limadikira ndi kumvetsera iye, ndipo amakondwa akamva mawu a mkwatiyo. Ine changa ndi chimwemwe ndipo ndine wosangalala kwambiri. 30 Nʼkoyenera kuti Iyeyo akule, ine ndichepe. 31 “Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse. 32 Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake. 33 Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona. 34 Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire. 35 Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake. 36 Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”

In Other Versions

John 3 in the ANGEFD

John 3 in the ANTPNG2D

John 3 in the AS21

John 3 in the BAGH

John 3 in the BBPNG

John 3 in the BBT1E

John 3 in the BDS

John 3 in the BEV

John 3 in the BHAD

John 3 in the BIB

John 3 in the BLPT

John 3 in the BNT

John 3 in the BNTABOOT

John 3 in the BNTLV

John 3 in the BOATCB

John 3 in the BOATCB2

John 3 in the BOBCV

John 3 in the BOCNT

John 3 in the BOECS

John 3 in the BOHCB

John 3 in the BOHCV

John 3 in the BOHLNT

John 3 in the BOHNTLTAL

John 3 in the BOICB

John 3 in the BOILNTAP

John 3 in the BOITCV

John 3 in the BOKCV

John 3 in the BOKCV2

John 3 in the BOKHWOG

John 3 in the BOKSSV

John 3 in the BOLCB

John 3 in the BOLCB2

John 3 in the BOMCV

John 3 in the BONAV

John 3 in the BONCB

John 3 in the BONLT

John 3 in the BONUT2

John 3 in the BOPLNT

John 3 in the BOSCB

John 3 in the BOSNC

John 3 in the BOTLNT

John 3 in the BOVCB

John 3 in the BOYCB

John 3 in the BPBB

John 3 in the BPH

John 3 in the BSB

John 3 in the CCB

John 3 in the CUV

John 3 in the CUVS

John 3 in the DBT

John 3 in the DGDNT

John 3 in the DHNT

John 3 in the DNT

John 3 in the ELBE

John 3 in the EMTV

John 3 in the ESV

John 3 in the FBV

John 3 in the FEB

John 3 in the GGMNT

John 3 in the GNT

John 3 in the HARY

John 3 in the HNT

John 3 in the IRVA

John 3 in the IRVB

John 3 in the IRVG

John 3 in the IRVH

John 3 in the IRVK

John 3 in the IRVM

John 3 in the IRVM2

John 3 in the IRVO

John 3 in the IRVP

John 3 in the IRVT

John 3 in the IRVT2

John 3 in the IRVU

John 3 in the ISVN

John 3 in the JSNT

John 3 in the KAPI

John 3 in the KBT1ETNIK

John 3 in the KBV

John 3 in the KJV

John 3 in the KNFD

John 3 in the LBA

John 3 in the LBLA

John 3 in the LNT

John 3 in the LSV

John 3 in the MAAL

John 3 in the MBV

John 3 in the MBV2

John 3 in the MHNT

John 3 in the MKNFD

John 3 in the MNG

John 3 in the MNT

John 3 in the MNT2

John 3 in the MRS1T

John 3 in the NAA

John 3 in the NASB

John 3 in the NBLA

John 3 in the NBS

John 3 in the NBVTP

John 3 in the NET2

John 3 in the NIV11

John 3 in the NNT

John 3 in the NNT2

John 3 in the NNT3

John 3 in the PDDPT

John 3 in the PFNT

John 3 in the RMNT

John 3 in the SBIAS

John 3 in the SBIBS

John 3 in the SBIBS2

John 3 in the SBICS

John 3 in the SBIDS

John 3 in the SBIGS

John 3 in the SBIHS

John 3 in the SBIIS

John 3 in the SBIIS2

John 3 in the SBIIS3

John 3 in the SBIKS

John 3 in the SBIKS2

John 3 in the SBIMS

John 3 in the SBIOS

John 3 in the SBIPS

John 3 in the SBISS

John 3 in the SBITS

John 3 in the SBITS2

John 3 in the SBITS3

John 3 in the SBITS4

John 3 in the SBIUS

John 3 in the SBIVS

John 3 in the SBT

John 3 in the SBT1E

John 3 in the SCHL

John 3 in the SNT

John 3 in the SUSU

John 3 in the SUSU2

John 3 in the SYNO

John 3 in the TBIAOTANT

John 3 in the TBT1E

John 3 in the TBT1E2

John 3 in the TFTIP

John 3 in the TFTU

John 3 in the TGNTATF3T

John 3 in the THAI

John 3 in the TNFD

John 3 in the TNT

John 3 in the TNTIK

John 3 in the TNTIL

John 3 in the TNTIN

John 3 in the TNTIP

John 3 in the TNTIZ

John 3 in the TOMA

John 3 in the TTENT

John 3 in the UBG

John 3 in the UGV

John 3 in the UGV2

John 3 in the UGV3

John 3 in the VBL

John 3 in the VDCC

John 3 in the YALU

John 3 in the YAPE

John 3 in the YBVTP

John 3 in the ZBP