Job 28 (BOGWICC)

1 Pali mgodi wa silivandiponso malo oyengerapo golide. 2 Chitsulo amachikumba pansi,ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa. 3 Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale,amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo,kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani. 4 Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu,kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko;iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku. 5 Nthaka, imene imatulutsa zakudya,kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto; 6 miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake,ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide. 7 Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi,palibe kamtema amene anayiona. 8 Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo,ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo. 9 Munthu amaphwanya matanthwe olimba,ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde. 10 Amabowola njira mʼmatanthwewo;ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo. 11 Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso,motero amatulutsira poyera zinthu zobisika. 12 “Koma nzeru zingapezeke kuti?Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti? 13 Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo;nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo. 14 Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’ 15 Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri,mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri. 16 Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri,kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro. 17 Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi,sungayigule ndi zokometsera zagolide. 18 Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe;mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi. 19 Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi;nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri. 20 “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti?Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti? 21 Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse,ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga. 22 Chiwonongeko ndi imfa zikuti,‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’ 23 Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko,ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala, 24 pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansindipo amaona zonse za kunsi kwa thambo. 25 Iye atapatsa mphepo mphamvu zake,nayeza kuzama kwa nyanja, 26 atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwandi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu, 27 pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake;nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe. 28 Ndipo Iye anati kwa munthu,‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezondipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ”

In Other Versions

Job 28 in the ANGEFD

Job 28 in the ANTPNG2D

Job 28 in the AS21

Job 28 in the BAGH

Job 28 in the BBPNG

Job 28 in the BBT1E

Job 28 in the BDS

Job 28 in the BEV

Job 28 in the BHAD

Job 28 in the BIB

Job 28 in the BLPT

Job 28 in the BNT

Job 28 in the BNTABOOT

Job 28 in the BNTLV

Job 28 in the BOATCB

Job 28 in the BOATCB2

Job 28 in the BOBCV

Job 28 in the BOCNT

Job 28 in the BOECS

Job 28 in the BOHCB

Job 28 in the BOHCV

Job 28 in the BOHLNT

Job 28 in the BOHNTLTAL

Job 28 in the BOICB

Job 28 in the BOILNTAP

Job 28 in the BOITCV

Job 28 in the BOKCV

Job 28 in the BOKCV2

Job 28 in the BOKHWOG

Job 28 in the BOKSSV

Job 28 in the BOLCB

Job 28 in the BOLCB2

Job 28 in the BOMCV

Job 28 in the BONAV

Job 28 in the BONCB

Job 28 in the BONLT

Job 28 in the BONUT2

Job 28 in the BOPLNT

Job 28 in the BOSCB

Job 28 in the BOSNC

Job 28 in the BOTLNT

Job 28 in the BOVCB

Job 28 in the BOYCB

Job 28 in the BPBB

Job 28 in the BPH

Job 28 in the BSB

Job 28 in the CCB

Job 28 in the CUV

Job 28 in the CUVS

Job 28 in the DBT

Job 28 in the DGDNT

Job 28 in the DHNT

Job 28 in the DNT

Job 28 in the ELBE

Job 28 in the EMTV

Job 28 in the ESV

Job 28 in the FBV

Job 28 in the FEB

Job 28 in the GGMNT

Job 28 in the GNT

Job 28 in the HARY

Job 28 in the HNT

Job 28 in the IRVA

Job 28 in the IRVB

Job 28 in the IRVG

Job 28 in the IRVH

Job 28 in the IRVK

Job 28 in the IRVM

Job 28 in the IRVM2

Job 28 in the IRVO

Job 28 in the IRVP

Job 28 in the IRVT

Job 28 in the IRVT2

Job 28 in the IRVU

Job 28 in the ISVN

Job 28 in the JSNT

Job 28 in the KAPI

Job 28 in the KBT1ETNIK

Job 28 in the KBV

Job 28 in the KJV

Job 28 in the KNFD

Job 28 in the LBA

Job 28 in the LBLA

Job 28 in the LNT

Job 28 in the LSV

Job 28 in the MAAL

Job 28 in the MBV

Job 28 in the MBV2

Job 28 in the MHNT

Job 28 in the MKNFD

Job 28 in the MNG

Job 28 in the MNT

Job 28 in the MNT2

Job 28 in the MRS1T

Job 28 in the NAA

Job 28 in the NASB

Job 28 in the NBLA

Job 28 in the NBS

Job 28 in the NBVTP

Job 28 in the NET2

Job 28 in the NIV11

Job 28 in the NNT

Job 28 in the NNT2

Job 28 in the NNT3

Job 28 in the PDDPT

Job 28 in the PFNT

Job 28 in the RMNT

Job 28 in the SBIAS

Job 28 in the SBIBS

Job 28 in the SBIBS2

Job 28 in the SBICS

Job 28 in the SBIDS

Job 28 in the SBIGS

Job 28 in the SBIHS

Job 28 in the SBIIS

Job 28 in the SBIIS2

Job 28 in the SBIIS3

Job 28 in the SBIKS

Job 28 in the SBIKS2

Job 28 in the SBIMS

Job 28 in the SBIOS

Job 28 in the SBIPS

Job 28 in the SBISS

Job 28 in the SBITS

Job 28 in the SBITS2

Job 28 in the SBITS3

Job 28 in the SBITS4

Job 28 in the SBIUS

Job 28 in the SBIVS

Job 28 in the SBT

Job 28 in the SBT1E

Job 28 in the SCHL

Job 28 in the SNT

Job 28 in the SUSU

Job 28 in the SUSU2

Job 28 in the SYNO

Job 28 in the TBIAOTANT

Job 28 in the TBT1E

Job 28 in the TBT1E2

Job 28 in the TFTIP

Job 28 in the TFTU

Job 28 in the TGNTATF3T

Job 28 in the THAI

Job 28 in the TNFD

Job 28 in the TNT

Job 28 in the TNTIK

Job 28 in the TNTIL

Job 28 in the TNTIN

Job 28 in the TNTIP

Job 28 in the TNTIZ

Job 28 in the TOMA

Job 28 in the TTENT

Job 28 in the UBG

Job 28 in the UGV

Job 28 in the UGV2

Job 28 in the UGV3

Job 28 in the VBL

Job 28 in the VDCC

Job 28 in the YALU

Job 28 in the YAPE

Job 28 in the YBVTP

Job 28 in the ZBP