Job 9 (BOGWICC)

1 Ndipo Yobu anayankha kuti, 2 “Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona.Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu? 3 Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye,Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe. 4 Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka.Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka? 5 Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa,ndipo amawagubuduza ali wokwiya. 6 Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pakendipo amanjenjemeretsa mizati yake. 7 Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala;Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi. 8 Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwambandipo amayenda pa mafunde a pa nyanja. 9 Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana,nsangwe ndi kumpotosimpita. 10 Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,zodabwitsa zimene sizingawerengeke. 11 Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona;akadutsa, sindingathe kumuzindikira. 12 Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa?Ndani anganene kwa Iye kuti, ‘Mukuchita chiyani?’ 13 Mulungu sabweza mkwiyo wake;ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake. 14 “Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji?Ndingawapeze kuti mawu oti nʼkutsutsana naye? 15 Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe;ndikanangopempha chifundo kwa woweruza wanga. 16 Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera,sindikhulupirira kuti akanamva mawu angawo. 17 Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho,ndipo akanandipweteka popanda chifukwa. 18 Mulungu sakanandilola kuti ndipumensokoma akanandichulukitsira zowawa. 19 Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi!Ndipo tikanena za chiweruzo cholungama, ndani angamuzenge mlandu? 20 Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa;ndikanakhala wopanda cholakwa, pakamwa panga pakanandipeza wolakwa. 21 “Ngakhale ine ndili wosalakwa,sindidziyenereza ndekha;moyo wanga ndimawupeputsa. 22 Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti,‘Iye amawononga anthu osalakwa ndi anthu oyipa omwe.’ 23 Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi,Iye amaseka tsoka la munthu wosalakwayo. 24 Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipaIye amawatseka maso anthu oweruza dzikolo.Ngati si Iyeyo, nanga ndani? 25 “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro;masikuwo amapita ine osaonapo zabwino. 26 Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja,ngati mphungu zothamangira nyama zoti zidye. 27 Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga,ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’ 28 ndikuopabe mavuto anga onse,popeza ndikudziwa kuti simudzavomereza kuti ndine wosalakwa. 29 Popeza ndapezeka kale wolakwandivutikirenji popanda phindu? 30 Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambirindi kusamba mʼmanja mwanga ndi sopo, 31 mutha kundiponyabe pa dzala,kotero kuti ngakhale zovala zanga zomwe zidzandinyansa. 32 “Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha,sindingathe kutsutsana naye mʼbwalo la milandu. 33 Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu,kuti atibweretse ife tonse pamodzi, 34 munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa inekuti kuopsa kwake kusandichititsenso mantha! 35 Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo,koma monga zililimu, sindingathe.

In Other Versions

Job 9 in the ANGEFD

Job 9 in the ANTPNG2D

Job 9 in the AS21

Job 9 in the BAGH

Job 9 in the BBPNG

Job 9 in the BBT1E

Job 9 in the BDS

Job 9 in the BEV

Job 9 in the BHAD

Job 9 in the BIB

Job 9 in the BLPT

Job 9 in the BNT

Job 9 in the BNTABOOT

Job 9 in the BNTLV

Job 9 in the BOATCB

Job 9 in the BOATCB2

Job 9 in the BOBCV

Job 9 in the BOCNT

Job 9 in the BOECS

Job 9 in the BOHCB

Job 9 in the BOHCV

Job 9 in the BOHLNT

Job 9 in the BOHNTLTAL

Job 9 in the BOICB

Job 9 in the BOILNTAP

Job 9 in the BOITCV

Job 9 in the BOKCV

Job 9 in the BOKCV2

Job 9 in the BOKHWOG

Job 9 in the BOKSSV

Job 9 in the BOLCB

Job 9 in the BOLCB2

Job 9 in the BOMCV

Job 9 in the BONAV

Job 9 in the BONCB

Job 9 in the BONLT

Job 9 in the BONUT2

Job 9 in the BOPLNT

Job 9 in the BOSCB

Job 9 in the BOSNC

Job 9 in the BOTLNT

Job 9 in the BOVCB

Job 9 in the BOYCB

Job 9 in the BPBB

Job 9 in the BPH

Job 9 in the BSB

Job 9 in the CCB

Job 9 in the CUV

Job 9 in the CUVS

Job 9 in the DBT

Job 9 in the DGDNT

Job 9 in the DHNT

Job 9 in the DNT

Job 9 in the ELBE

Job 9 in the EMTV

Job 9 in the ESV

Job 9 in the FBV

Job 9 in the FEB

Job 9 in the GGMNT

Job 9 in the GNT

Job 9 in the HARY

Job 9 in the HNT

Job 9 in the IRVA

Job 9 in the IRVB

Job 9 in the IRVG

Job 9 in the IRVH

Job 9 in the IRVK

Job 9 in the IRVM

Job 9 in the IRVM2

Job 9 in the IRVO

Job 9 in the IRVP

Job 9 in the IRVT

Job 9 in the IRVT2

Job 9 in the IRVU

Job 9 in the ISVN

Job 9 in the JSNT

Job 9 in the KAPI

Job 9 in the KBT1ETNIK

Job 9 in the KBV

Job 9 in the KJV

Job 9 in the KNFD

Job 9 in the LBA

Job 9 in the LBLA

Job 9 in the LNT

Job 9 in the LSV

Job 9 in the MAAL

Job 9 in the MBV

Job 9 in the MBV2

Job 9 in the MHNT

Job 9 in the MKNFD

Job 9 in the MNG

Job 9 in the MNT

Job 9 in the MNT2

Job 9 in the MRS1T

Job 9 in the NAA

Job 9 in the NASB

Job 9 in the NBLA

Job 9 in the NBS

Job 9 in the NBVTP

Job 9 in the NET2

Job 9 in the NIV11

Job 9 in the NNT

Job 9 in the NNT2

Job 9 in the NNT3

Job 9 in the PDDPT

Job 9 in the PFNT

Job 9 in the RMNT

Job 9 in the SBIAS

Job 9 in the SBIBS

Job 9 in the SBIBS2

Job 9 in the SBICS

Job 9 in the SBIDS

Job 9 in the SBIGS

Job 9 in the SBIHS

Job 9 in the SBIIS

Job 9 in the SBIIS2

Job 9 in the SBIIS3

Job 9 in the SBIKS

Job 9 in the SBIKS2

Job 9 in the SBIMS

Job 9 in the SBIOS

Job 9 in the SBIPS

Job 9 in the SBISS

Job 9 in the SBITS

Job 9 in the SBITS2

Job 9 in the SBITS3

Job 9 in the SBITS4

Job 9 in the SBIUS

Job 9 in the SBIVS

Job 9 in the SBT

Job 9 in the SBT1E

Job 9 in the SCHL

Job 9 in the SNT

Job 9 in the SUSU

Job 9 in the SUSU2

Job 9 in the SYNO

Job 9 in the TBIAOTANT

Job 9 in the TBT1E

Job 9 in the TBT1E2

Job 9 in the TFTIP

Job 9 in the TFTU

Job 9 in the TGNTATF3T

Job 9 in the THAI

Job 9 in the TNFD

Job 9 in the TNT

Job 9 in the TNTIK

Job 9 in the TNTIL

Job 9 in the TNTIN

Job 9 in the TNTIP

Job 9 in the TNTIZ

Job 9 in the TOMA

Job 9 in the TTENT

Job 9 in the UBG

Job 9 in the UGV

Job 9 in the UGV2

Job 9 in the UGV3

Job 9 in the VBL

Job 9 in the VDCC

Job 9 in the YALU

Job 9 in the YAPE

Job 9 in the YBVTP

Job 9 in the ZBP