Joel 2 (BOGWICC)

1 Lizani lipenga mu Ziyoni.Chenjezani pa phiri langa loyera.Onse okhala mʼdziko anjenjemere,pakuti tsiku la Yehova likubwera,layandikira; 2 tsiku la mdima ndi chisoni,tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri,gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera,gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepongakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso. 3 Patsogolo pawo moto ukupsereza,kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu.Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni,kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu,kulibe kanthu kotsalapo. 4 Maonekedwe awo ali ngati akavalo;akuthamanga ngati akavalo ankhondo. 5 Akulumpha pamwamba pa mapirindi phokoso ngati la magaleta,ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu,ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo. 6 Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima;nkhope iliyonse imagwa. 7 Amathamanga ngati ankhondo;amakwera makoma ngati asilikali.Onse amayenda pa mizere,osaphonya njira yawo. 8 Iwo sakankhanakankhana,aliyense amayenda molunjika.Amadutsa malo otchingidwapopanda kumwazikana. 9 Amakhamukira mu mzinda,amathamanga mʼmbali mwa khoma.Amakwera nyumba ndi kulowamo;amalowera pa zenera ngati mbala. 10 Patsogolo pawo dziko limagwedezeka,thambo limanjenjemera,dzuwa ndi mwezi zimachita mdima,ndipo nyenyezi zimaleka kuwala. 11 Yehova amabangulapatsogolo pawo,gulu lake lankhondo ndi losawerengeka,ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake.Tsiku la Yehova ndi lalikulu;ndi loopsa.Ndani adzapirira pa tsikulo? 12 “Ngakhale tsopano,bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonseposala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova. 13 Ngʼambani mtima wanuosati zovala zanu.Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo,wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka,ndipo amaleka kubweretsa mavuto. 14 Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni,nʼkutisiyira madalitso,a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwakwa Yehova Mulungu wanu. 15 Lizani lipenga mu Ziyoni,lengezani tsiku losala zakudya,itanitsani msonkhano wopatulika. 16 Sonkhanitsani anthu pamodzi,muwawuze kuti adziyeretse;sonkhanitsani akuluakulu,sonkhanitsani ana,sonkhanitsani ndi oyamwa omwe.Mkwati atuluke mʼchipinda chake,mkwatibwi atuluke mokhala mwake. 17 Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova,alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova.Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu.Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka,kuti anthu a mitundu ina awalamulire.Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti,‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ” 18 Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lakendi kuchitira chisoni anthu ake. 19 Yehova adzawayankha kuti,“Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafutandipo mudzakhuta ndithu;sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzokwa anthu a mitundu ina. 20 “Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu,kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu,gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawandi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo.Ndipo mitembo yawo idzawola,fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu. 21 Iwe dziko usachite mantha;sangalala ndipo kondwera.Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu. 22 Inu nyama zakuthengo, musachite mantha,pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira.Mitengo ikubala zipatso zake;mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri. 23 Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani,kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu,pakuti wakupatsanimvula yoyambirira mwachilungamo chake.Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka,mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja. 24 Pa malo opunthira padzaza tirigu;mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta. 25 “Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe,dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono,dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka;gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu. 26 Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta,ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,amene wakuchitirani zodabwitsa;ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi. 27 Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli,kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,ndi kuti palibenso wina;ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi. 28 “Ndipo patapita nthawi,ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,nkhalamba zanu zidzalota maloto,anyamata anu adzaona masomphenya. 29 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazindidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo. 30 Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalengandi pa dziko lapansi,ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo. 31 Dzuwa lidzadetsedwandipo mwezi udzaoneka ngati magazilisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye. 32 Ndipo aliyense amene adzayitanapa dzina la Ambuye adzapulumuka;pakuti chipulumutso chidzakhala pa Phiri la Ziyonindi mu Yerusalemu,monga Yehova wanenera,pakati pa otsalaamene Yehova wawayitana.

In Other Versions

Joel 2 in the ANGEFD

Joel 2 in the ANTPNG2D

Joel 2 in the AS21

Joel 2 in the BAGH

Joel 2 in the BBPNG

Joel 2 in the BBT1E

Joel 2 in the BDS

Joel 2 in the BEV

Joel 2 in the BHAD

Joel 2 in the BIB

Joel 2 in the BLPT

Joel 2 in the BNT

Joel 2 in the BNTABOOT

Joel 2 in the BNTLV

Joel 2 in the BOATCB

Joel 2 in the BOATCB2

Joel 2 in the BOBCV

Joel 2 in the BOCNT

Joel 2 in the BOECS

Joel 2 in the BOHCB

Joel 2 in the BOHCV

Joel 2 in the BOHLNT

Joel 2 in the BOHNTLTAL

Joel 2 in the BOICB

Joel 2 in the BOILNTAP

Joel 2 in the BOITCV

Joel 2 in the BOKCV

Joel 2 in the BOKCV2

Joel 2 in the BOKHWOG

Joel 2 in the BOKSSV

Joel 2 in the BOLCB

Joel 2 in the BOLCB2

Joel 2 in the BOMCV

Joel 2 in the BONAV

Joel 2 in the BONCB

Joel 2 in the BONLT

Joel 2 in the BONUT2

Joel 2 in the BOPLNT

Joel 2 in the BOSCB

Joel 2 in the BOSNC

Joel 2 in the BOTLNT

Joel 2 in the BOVCB

Joel 2 in the BOYCB

Joel 2 in the BPBB

Joel 2 in the BPH

Joel 2 in the BSB

Joel 2 in the CCB

Joel 2 in the CUV

Joel 2 in the CUVS

Joel 2 in the DBT

Joel 2 in the DGDNT

Joel 2 in the DHNT

Joel 2 in the DNT

Joel 2 in the ELBE

Joel 2 in the EMTV

Joel 2 in the ESV

Joel 2 in the FBV

Joel 2 in the FEB

Joel 2 in the GGMNT

Joel 2 in the GNT

Joel 2 in the HARY

Joel 2 in the HNT

Joel 2 in the IRVA

Joel 2 in the IRVB

Joel 2 in the IRVG

Joel 2 in the IRVH

Joel 2 in the IRVK

Joel 2 in the IRVM

Joel 2 in the IRVM2

Joel 2 in the IRVO

Joel 2 in the IRVP

Joel 2 in the IRVT

Joel 2 in the IRVT2

Joel 2 in the IRVU

Joel 2 in the ISVN

Joel 2 in the JSNT

Joel 2 in the KAPI

Joel 2 in the KBT1ETNIK

Joel 2 in the KBV

Joel 2 in the KJV

Joel 2 in the KNFD

Joel 2 in the LBA

Joel 2 in the LBLA

Joel 2 in the LNT

Joel 2 in the LSV

Joel 2 in the MAAL

Joel 2 in the MBV

Joel 2 in the MBV2

Joel 2 in the MHNT

Joel 2 in the MKNFD

Joel 2 in the MNG

Joel 2 in the MNT

Joel 2 in the MNT2

Joel 2 in the MRS1T

Joel 2 in the NAA

Joel 2 in the NASB

Joel 2 in the NBLA

Joel 2 in the NBS

Joel 2 in the NBVTP

Joel 2 in the NET2

Joel 2 in the NIV11

Joel 2 in the NNT

Joel 2 in the NNT2

Joel 2 in the NNT3

Joel 2 in the PDDPT

Joel 2 in the PFNT

Joel 2 in the RMNT

Joel 2 in the SBIAS

Joel 2 in the SBIBS

Joel 2 in the SBIBS2

Joel 2 in the SBICS

Joel 2 in the SBIDS

Joel 2 in the SBIGS

Joel 2 in the SBIHS

Joel 2 in the SBIIS

Joel 2 in the SBIIS2

Joel 2 in the SBIIS3

Joel 2 in the SBIKS

Joel 2 in the SBIKS2

Joel 2 in the SBIMS

Joel 2 in the SBIOS

Joel 2 in the SBIPS

Joel 2 in the SBISS

Joel 2 in the SBITS

Joel 2 in the SBITS2

Joel 2 in the SBITS3

Joel 2 in the SBITS4

Joel 2 in the SBIUS

Joel 2 in the SBIVS

Joel 2 in the SBT

Joel 2 in the SBT1E

Joel 2 in the SCHL

Joel 2 in the SNT

Joel 2 in the SUSU

Joel 2 in the SUSU2

Joel 2 in the SYNO

Joel 2 in the TBIAOTANT

Joel 2 in the TBT1E

Joel 2 in the TBT1E2

Joel 2 in the TFTIP

Joel 2 in the TFTU

Joel 2 in the TGNTATF3T

Joel 2 in the THAI

Joel 2 in the TNFD

Joel 2 in the TNT

Joel 2 in the TNTIK

Joel 2 in the TNTIL

Joel 2 in the TNTIN

Joel 2 in the TNTIP

Joel 2 in the TNTIZ

Joel 2 in the TOMA

Joel 2 in the TTENT

Joel 2 in the UBG

Joel 2 in the UGV

Joel 2 in the UGV2

Joel 2 in the UGV3

Joel 2 in the VBL

Joel 2 in the VDCC

Joel 2 in the YALU

Joel 2 in the YAPE

Joel 2 in the YBVTP

Joel 2 in the ZBP