Joshua 5 (BOGWICC)

1 Mafumu onse a Aamori, a kummawa kwa Yorodani ndi mafumu onse a Akanaani a mʼmbali mwa Nyanja anamva momwe Yehova anawumitsira Yorodani pamene Aisraeli ankawoloka. Choncho anachita mantha ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraeliwo. 2 Tsono Yehova anati kwa Yoswa, “Panga mipeni ya miyala ndipo uchitenso mwambo wa mdulidwe pa Aisraeli.” 3 Choncho Yoswa anapanga mipeni ya miyala ndi kuchita mdulidwe Aisraeli ku Gibeyati Haaraloti. 4 Chifukwa chimene Yoswa anachitira izi ndi ichi: Onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto, amuna onse amene anali oyenera kumenya nkhondo anatha kufa mʼchipululu atatuluka mʼdziko la Igupto. 5 Anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto anali atachita mwambo wa mdulidwe, koma onse amene anabadwira mʼchipululu, pa ulendo wochoka ku Igupto, sanachite. 6 Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa. 7 Koma ana awo amene analowa mʼmalo mwawo ndiwo amene Yoswa anawachita mdulidwe popeza sanachite pamene anali pa ulendo wawo mʼchipululu muja. 8 Atamaliza kuchita mdulidwe uja, anthu onse anakakhala ku misasa yawo kudikira kuti zilonda zipole. 9 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Kuyambira tsopano anthu a ku Igupto sadzakunyozaninso.” Nʼchifukwa chake malowa anatchedwa Giligala mpaka lero. 10 Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. 11 Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo. 12 Atangodya chakudya cha mʼdzikomo, mana anasiya kugwa, ndipo sanapezekenso. Kuyambira nthawi imeneyo Aisraeli anayamba kudya chakudya cha mʼdziko la Kanaani. 13 Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo mwadzidzidzi anaona munthu atayima patsogolo pake ndi lupanga losolola mʼdzanja lake. Yoswa anapita pamene panali munthuyo ndipo anamufunsa kuti, “Kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?” 14 Iye anayankha kuti “Sindili mbali iliyonse. Ndabwera monga mkulu wa asilikali a Yehova.” Pomwepo Yoswa anadzigwetsa chafufumimba kupereka ulemu, ndipo anamufunsa, “Kodi mbuye wanga muli ndi uthenga wotani kwa mtumiki wanu?” 15 Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo.

In Other Versions

Joshua 5 in the ANGEFD

Joshua 5 in the ANTPNG2D

Joshua 5 in the AS21

Joshua 5 in the BAGH

Joshua 5 in the BBPNG

Joshua 5 in the BBT1E

Joshua 5 in the BDS

Joshua 5 in the BEV

Joshua 5 in the BHAD

Joshua 5 in the BIB

Joshua 5 in the BLPT

Joshua 5 in the BNT

Joshua 5 in the BNTABOOT

Joshua 5 in the BNTLV

Joshua 5 in the BOATCB

Joshua 5 in the BOATCB2

Joshua 5 in the BOBCV

Joshua 5 in the BOCNT

Joshua 5 in the BOECS

Joshua 5 in the BOHCB

Joshua 5 in the BOHCV

Joshua 5 in the BOHLNT

Joshua 5 in the BOHNTLTAL

Joshua 5 in the BOICB

Joshua 5 in the BOILNTAP

Joshua 5 in the BOITCV

Joshua 5 in the BOKCV

Joshua 5 in the BOKCV2

Joshua 5 in the BOKHWOG

Joshua 5 in the BOKSSV

Joshua 5 in the BOLCB

Joshua 5 in the BOLCB2

Joshua 5 in the BOMCV

Joshua 5 in the BONAV

Joshua 5 in the BONCB

Joshua 5 in the BONLT

Joshua 5 in the BONUT2

Joshua 5 in the BOPLNT

Joshua 5 in the BOSCB

Joshua 5 in the BOSNC

Joshua 5 in the BOTLNT

Joshua 5 in the BOVCB

Joshua 5 in the BOYCB

Joshua 5 in the BPBB

Joshua 5 in the BPH

Joshua 5 in the BSB

Joshua 5 in the CCB

Joshua 5 in the CUV

Joshua 5 in the CUVS

Joshua 5 in the DBT

Joshua 5 in the DGDNT

Joshua 5 in the DHNT

Joshua 5 in the DNT

Joshua 5 in the ELBE

Joshua 5 in the EMTV

Joshua 5 in the ESV

Joshua 5 in the FBV

Joshua 5 in the FEB

Joshua 5 in the GGMNT

Joshua 5 in the GNT

Joshua 5 in the HARY

Joshua 5 in the HNT

Joshua 5 in the IRVA

Joshua 5 in the IRVB

Joshua 5 in the IRVG

Joshua 5 in the IRVH

Joshua 5 in the IRVK

Joshua 5 in the IRVM

Joshua 5 in the IRVM2

Joshua 5 in the IRVO

Joshua 5 in the IRVP

Joshua 5 in the IRVT

Joshua 5 in the IRVT2

Joshua 5 in the IRVU

Joshua 5 in the ISVN

Joshua 5 in the JSNT

Joshua 5 in the KAPI

Joshua 5 in the KBT1ETNIK

Joshua 5 in the KBV

Joshua 5 in the KJV

Joshua 5 in the KNFD

Joshua 5 in the LBA

Joshua 5 in the LBLA

Joshua 5 in the LNT

Joshua 5 in the LSV

Joshua 5 in the MAAL

Joshua 5 in the MBV

Joshua 5 in the MBV2

Joshua 5 in the MHNT

Joshua 5 in the MKNFD

Joshua 5 in the MNG

Joshua 5 in the MNT

Joshua 5 in the MNT2

Joshua 5 in the MRS1T

Joshua 5 in the NAA

Joshua 5 in the NASB

Joshua 5 in the NBLA

Joshua 5 in the NBS

Joshua 5 in the NBVTP

Joshua 5 in the NET2

Joshua 5 in the NIV11

Joshua 5 in the NNT

Joshua 5 in the NNT2

Joshua 5 in the NNT3

Joshua 5 in the PDDPT

Joshua 5 in the PFNT

Joshua 5 in the RMNT

Joshua 5 in the SBIAS

Joshua 5 in the SBIBS

Joshua 5 in the SBIBS2

Joshua 5 in the SBICS

Joshua 5 in the SBIDS

Joshua 5 in the SBIGS

Joshua 5 in the SBIHS

Joshua 5 in the SBIIS

Joshua 5 in the SBIIS2

Joshua 5 in the SBIIS3

Joshua 5 in the SBIKS

Joshua 5 in the SBIKS2

Joshua 5 in the SBIMS

Joshua 5 in the SBIOS

Joshua 5 in the SBIPS

Joshua 5 in the SBISS

Joshua 5 in the SBITS

Joshua 5 in the SBITS2

Joshua 5 in the SBITS3

Joshua 5 in the SBITS4

Joshua 5 in the SBIUS

Joshua 5 in the SBIVS

Joshua 5 in the SBT

Joshua 5 in the SBT1E

Joshua 5 in the SCHL

Joshua 5 in the SNT

Joshua 5 in the SUSU

Joshua 5 in the SUSU2

Joshua 5 in the SYNO

Joshua 5 in the TBIAOTANT

Joshua 5 in the TBT1E

Joshua 5 in the TBT1E2

Joshua 5 in the TFTIP

Joshua 5 in the TFTU

Joshua 5 in the TGNTATF3T

Joshua 5 in the THAI

Joshua 5 in the TNFD

Joshua 5 in the TNT

Joshua 5 in the TNTIK

Joshua 5 in the TNTIL

Joshua 5 in the TNTIN

Joshua 5 in the TNTIP

Joshua 5 in the TNTIZ

Joshua 5 in the TOMA

Joshua 5 in the TTENT

Joshua 5 in the UBG

Joshua 5 in the UGV

Joshua 5 in the UGV2

Joshua 5 in the UGV3

Joshua 5 in the VBL

Joshua 5 in the VDCC

Joshua 5 in the YALU

Joshua 5 in the YAPE

Joshua 5 in the YBVTP

Joshua 5 in the ZBP