Lamentations 2 (BOGWICC)
1 Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyonindi mtambo wa mkwiyo wake!Iye wataya pansi ulemerero wa Israelikuchoka kumwamba.Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirensopopondapo mapazi ake. 2 Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo;mu mkwiyo wake anagwetsamalinga a mwana wamkazi wa Yuda.Anagwetsa pansi mochititsa manyazimaufumu ndi akalonga ake. 3 Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyolanyanga iliyonse ya Israeli.Anabweza dzanja lake lamanjapamene mdani anamuyandikira.Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsaumene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi. 4 Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani;wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani,ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira.Ukali wake ukuyaka ngati motopa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni. 5 Ambuye ali ngati mdani;wawonongeratu Israeli;wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumundipo wawononga malinga ake.Iye wachulukitsa kubuma ndi kulirakwa mwana wamkazi wa Yuda. 6 Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda;wawononga malo ake a msonkhano.Yehova wayiwalitsa Ziyonimaphwando ake oyikika ndi masabata ake.Mokwiya kwambiri, Iye ananyozamfumu ndi wansembe. 7 Ambuye wakana guwa lake la nsembendipo wasiya malo ake opatulika.Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumukwa mdani wake;adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehovangati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero. 8 Yehova anatsimikiza kugwetsamakoma a mwana wamkazi wa Ziyoni.Anawayesa ndi chingwendipo sanafune kuleka kuwagwetsa.Analiritsa malinga ndi makoma;onse anawonongeka pamodzi. 9 Zipata za Yerusalemu zalowa pansi;wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake.Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,palibenso lamulo,ndipo aneneri ake sakupezamasomphenya kuchokera kwa Yehova. 10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoniakhala chete pansi;awaza fumbi pa mitu yawondipo avala ziguduli.Anamwali a Yerusalemuaweramitsa mitu yawo pansi. 11 Maso anga atopa ndi kulira,ndazunzika mʼmoyo mwanga,mtima wanga wadzaza ndi chisonichifukwa anthu anga akuwonongeka,chifukwa ana ndi makanda akukomokamʼmisewu ya mu mzinda. 12 Anawo akufunsa amayi awo kuti,“Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?”pamene akukomoka ngati anthu olasidwamʼmisewu ya mʼmizinda,pamene miyoyo yawo ikufowokamʼmanja mwa amayi awo. 13 Ndinganene chiyani za iwe?Ndingakufanizire ndi chiyani,iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?Kodi ndingakufanizire ndi yanikuti ndikutonthoze,iwe namwali wa Ziyoni?Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja,kodi ndani angakuchiritse? 14 Masomphenya a aneneri akoanali abodza ndi achabechabe.Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolopoyika poyera mphulupulu zako.Mauthenga amene anakupatsaanali achabechabe ndi osocheretsa. 15 Onse oyenda mʼnjira yakoakukuwombera mʼmanja;akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodolaiwe mwana wamkazi wa Yerusalemu:“Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwawokongola kotheratu,chimwemwe cha dziko lonse lapansi?” 16 Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza;iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo,ndipo akuti, “Tamumeza.Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera;tili ndi moyo kuti tilione.” 17 Yehova wachita chimene anakonzeratu;wakwaniritsa mawu ake,amene anatsimikiza kale lomwe.Wakuwononga mopanda chifundo,walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako,wakweza mphamvu za adani ako. 18 Mitima ya anthuikufuwulira Ambuye.Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni,misozi yako itsike ngati mtsinjeusana ndi usiku;usadzipatse wekha mpumulo,maso ako asaleke kukhetsa misozi. 19 Dzuka, fuwula usiku,pamene alonda ayamba kulondera;khuthula mtima wako ngati madzipamaso pa Ambuye.Kweza manja ako kwa Iyechifukwa cha miyoyo ya ana ako,amene akukomoka ndi njalamʼmisewu yonse ya mu mzinda. 20 Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani:kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi?Kodi amayi adye ana awo,amene amawasamalira?Kodi ansembe ndi aneneri awapheremʼmalo opatulika a Ambuye? 21 Anyamata ndi okalamba aligone pamodzipa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda;anyamata anga ndi anamwali angaaphedwa ndi lupanga.Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu;mwawapha mopanda chifundo. 22 Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando,chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse.Pa tsiku limene Yehova wakwiyapalibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo;mdani wanga wawonongaonse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.
In Other Versions
Lamentations 2 in the ANTPNG2D
Lamentations 2 in the BNTABOOT
Lamentations 2 in the BOHNTLTAL
Lamentations 2 in the BOILNTAP
Lamentations 2 in the KBT1ETNIK
Lamentations 2 in the TBIAOTANT