Leviticus 20 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala. 3 Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera. 4 Ngati anthu a mʼderalo achita ngati sakumuona munthuyo pamene akupereka mwana wake kwa Moleki ndi kusamupha, 5 Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.” 6 “ ‘Ngati munthu adzapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena kwa owombeza, nadziyipitsa powatsatira iwowo, Ine ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anthu anzake. 7 “ ‘Chifukwa chake dzipatuleni ndi kukhala woyera popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 8 Ndipo sungani malangizo anga ndi kuwatsata. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani. 9 “ ‘Munthu aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. Magazi ake adzakhala pamutu pake chifukwa iye watemberera abambo kapena amayi ake. 10 “ ‘Ngati munthu wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. 11 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa abambo ake, wachititsa manyazi abambo ake. Munthuyo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. Magazi awo adzakhala pa mitu pake. 12 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa mwana wake, awiriwo ayenera kuphedwa. Iwo achita chinthu chonyansa kwambiri. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo. 13 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mwamuna mnzake ngati akugonana ndi mkazi, ndiye kuti onsewo achita chinthu cha manyazi. Choncho aphedwe. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo. 14 “ ‘Ngati munthu akwatira mkazi, nakwatiranso amayi ake, chimenecho ndi chinthu choyipa kwambiri. Mwamunayo pamodzi ndi akaziwo ayenera kutenthedwa pa moto kuti chinthu choyipa chotere chisapezekenso pakati panu. 15 “ ‘Ngati mwamuna agonana ndi nyama, iye ayenera kuphedwa, ndipo muyeneranso kupha nyamayo. 16 “ ‘Ngati mkazi agonana ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Mkaziyo ndi nyamayo ayenera kuphedwa, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo. 17 “ ‘Ngati munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake, kapena mwana wamkazi wa amayi ake, ndipo iwo nʼkugonana, ndiye kuti achita chinthu chochititsa manyazi. Onse awiri ayenera kuchotsedwa pa gulu la abale awo. Tsono popeza munthuyo wachititsa manyazi mlongo wake, adzayenera kulandira chilango. 18 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi pa nthawi yake yosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, ndipo mkaziyo wadzivulanso. Onse awiri achotsedwe pakati pa anthu anzawo. 19 “ ‘Musagonane ndi mchemwali wa amayi anu kapena abambo anu, pakuti kutero ndi kuchititsa manyazi mʼbale wanu. Nonse mudzalipira mlandu wanu. 20 “ ‘Ngati munthu agonana ndi azakhali ake, munthuyo wachititsa manyazi a malume ake. Onse adzalipira mlandu wawo. Onsewo adzafa wopanda mwana. 21 “ ‘Munthu akakwatira mkazi wa mchimwene wake ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wachititsa manyazi mʼbale wakeyo. Onse awiriwo adzakhala wopanda mwana. 22 “ ‘Nʼchifukwa chake muzisunga malangizo anga onse ndi malamulo anga ndipo muwatsatire kuti ku dziko limene Ine ndikupita nanu kuti mukakhalemo lisakakusanzeni. 23 Musatsanzire miyambo ya mitundu ya anthu imene ndi kuyipirikitsa inu mukufika. Chifukwa iwo anachita zinthu zonsezi, ndipo Ine ndinanyansidwa nawo. 24 Koma Ine ndinakuwuzani kuti, ‘Mudzatenga dziko lawo. Ine ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale cholowa chanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu. 25 “ ‘Chifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoyeretsedwa ndi nyama zodetsedwa ndiponso pakati pa mbalame zoyeretsedwa ndi mbalame zodetsedwa. Musadzidetse pakudya nyama iliyonse kapena mbalame, kapena chilichonse chimene chimakwawa pansi, chimene Ine ndachipatula kuti chikhale chodetsedwa kwa inu. 26 Muzikhala woyera pamaso panga chifukwa Ine Yehova, ndine woyera ndipo ndakupatulani pakati pa anthu a mitundu yonse kuti mukhale anthu anga. 27 “ ‘Mwamuna kapena mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena wanyanga pakati panu ayenera kuphedwa. Muwagende ndi miyala, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.’ ”

In Other Versions

Leviticus 20 in the ANGEFD

Leviticus 20 in the ANTPNG2D

Leviticus 20 in the AS21

Leviticus 20 in the BAGH

Leviticus 20 in the BBPNG

Leviticus 20 in the BBT1E

Leviticus 20 in the BDS

Leviticus 20 in the BEV

Leviticus 20 in the BHAD

Leviticus 20 in the BIB

Leviticus 20 in the BLPT

Leviticus 20 in the BNT

Leviticus 20 in the BNTABOOT

Leviticus 20 in the BNTLV

Leviticus 20 in the BOATCB

Leviticus 20 in the BOATCB2

Leviticus 20 in the BOBCV

Leviticus 20 in the BOCNT

Leviticus 20 in the BOECS

Leviticus 20 in the BOHCB

Leviticus 20 in the BOHCV

Leviticus 20 in the BOHLNT

Leviticus 20 in the BOHNTLTAL

Leviticus 20 in the BOICB

Leviticus 20 in the BOILNTAP

Leviticus 20 in the BOITCV

Leviticus 20 in the BOKCV

Leviticus 20 in the BOKCV2

Leviticus 20 in the BOKHWOG

Leviticus 20 in the BOKSSV

Leviticus 20 in the BOLCB

Leviticus 20 in the BOLCB2

Leviticus 20 in the BOMCV

Leviticus 20 in the BONAV

Leviticus 20 in the BONCB

Leviticus 20 in the BONLT

Leviticus 20 in the BONUT2

Leviticus 20 in the BOPLNT

Leviticus 20 in the BOSCB

Leviticus 20 in the BOSNC

Leviticus 20 in the BOTLNT

Leviticus 20 in the BOVCB

Leviticus 20 in the BOYCB

Leviticus 20 in the BPBB

Leviticus 20 in the BPH

Leviticus 20 in the BSB

Leviticus 20 in the CCB

Leviticus 20 in the CUV

Leviticus 20 in the CUVS

Leviticus 20 in the DBT

Leviticus 20 in the DGDNT

Leviticus 20 in the DHNT

Leviticus 20 in the DNT

Leviticus 20 in the ELBE

Leviticus 20 in the EMTV

Leviticus 20 in the ESV

Leviticus 20 in the FBV

Leviticus 20 in the FEB

Leviticus 20 in the GGMNT

Leviticus 20 in the GNT

Leviticus 20 in the HARY

Leviticus 20 in the HNT

Leviticus 20 in the IRVA

Leviticus 20 in the IRVB

Leviticus 20 in the IRVG

Leviticus 20 in the IRVH

Leviticus 20 in the IRVK

Leviticus 20 in the IRVM

Leviticus 20 in the IRVM2

Leviticus 20 in the IRVO

Leviticus 20 in the IRVP

Leviticus 20 in the IRVT

Leviticus 20 in the IRVT2

Leviticus 20 in the IRVU

Leviticus 20 in the ISVN

Leviticus 20 in the JSNT

Leviticus 20 in the KAPI

Leviticus 20 in the KBT1ETNIK

Leviticus 20 in the KBV

Leviticus 20 in the KJV

Leviticus 20 in the KNFD

Leviticus 20 in the LBA

Leviticus 20 in the LBLA

Leviticus 20 in the LNT

Leviticus 20 in the LSV

Leviticus 20 in the MAAL

Leviticus 20 in the MBV

Leviticus 20 in the MBV2

Leviticus 20 in the MHNT

Leviticus 20 in the MKNFD

Leviticus 20 in the MNG

Leviticus 20 in the MNT

Leviticus 20 in the MNT2

Leviticus 20 in the MRS1T

Leviticus 20 in the NAA

Leviticus 20 in the NASB

Leviticus 20 in the NBLA

Leviticus 20 in the NBS

Leviticus 20 in the NBVTP

Leviticus 20 in the NET2

Leviticus 20 in the NIV11

Leviticus 20 in the NNT

Leviticus 20 in the NNT2

Leviticus 20 in the NNT3

Leviticus 20 in the PDDPT

Leviticus 20 in the PFNT

Leviticus 20 in the RMNT

Leviticus 20 in the SBIAS

Leviticus 20 in the SBIBS

Leviticus 20 in the SBIBS2

Leviticus 20 in the SBICS

Leviticus 20 in the SBIDS

Leviticus 20 in the SBIGS

Leviticus 20 in the SBIHS

Leviticus 20 in the SBIIS

Leviticus 20 in the SBIIS2

Leviticus 20 in the SBIIS3

Leviticus 20 in the SBIKS

Leviticus 20 in the SBIKS2

Leviticus 20 in the SBIMS

Leviticus 20 in the SBIOS

Leviticus 20 in the SBIPS

Leviticus 20 in the SBISS

Leviticus 20 in the SBITS

Leviticus 20 in the SBITS2

Leviticus 20 in the SBITS3

Leviticus 20 in the SBITS4

Leviticus 20 in the SBIUS

Leviticus 20 in the SBIVS

Leviticus 20 in the SBT

Leviticus 20 in the SBT1E

Leviticus 20 in the SCHL

Leviticus 20 in the SNT

Leviticus 20 in the SUSU

Leviticus 20 in the SUSU2

Leviticus 20 in the SYNO

Leviticus 20 in the TBIAOTANT

Leviticus 20 in the TBT1E

Leviticus 20 in the TBT1E2

Leviticus 20 in the TFTIP

Leviticus 20 in the TFTU

Leviticus 20 in the TGNTATF3T

Leviticus 20 in the THAI

Leviticus 20 in the TNFD

Leviticus 20 in the TNT

Leviticus 20 in the TNTIK

Leviticus 20 in the TNTIL

Leviticus 20 in the TNTIN

Leviticus 20 in the TNTIP

Leviticus 20 in the TNTIZ

Leviticus 20 in the TOMA

Leviticus 20 in the TTENT

Leviticus 20 in the UBG

Leviticus 20 in the UGV

Leviticus 20 in the UGV2

Leviticus 20 in the UGV3

Leviticus 20 in the VBL

Leviticus 20 in the VDCC

Leviticus 20 in the YALU

Leviticus 20 in the YAPE

Leviticus 20 in the YBVTP

Leviticus 20 in the ZBP