Luke 10 (BOGWICC)

1 Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako. 2 Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola. 3 Pitani! Ine ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. 4 Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira. 5 “Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’ 6 Ngati mʼnyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere wanuwo udzakhala pa iyeyo; ngati mulibemo, mtendere wanuwo udzabwerera kwa inu. 7 Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina. 8 “Mukamalowa mʼmudzi, ndi kulandiridwa, idyani chilichonse akukonzerani. 9 Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 10 Koma mukalowa mʼmudzi ndipo osalandiridwa bwino, kapiteni ku misewu mʼmudzimo nʼkukanena kuti, 11 ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12 Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo. 13 “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 14 Koma adzachita chifundo polanga Turo ndi Sidoni kusiyana ndi inu. 15 Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. 16 “Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.” 17 Anthu 72 aja anabwerera ndi chimwemwe ndipo anati, “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife mʼdzina lanu.” 18 Iye anayankha kuti, “Ndinaona Satana akugwa kuchokera kumwamba ngati mphenzi. 19 Ine ndakupatsani ulamuliro woponda njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zonse za mdani; palibe chimene chidzakupwetekani. 20 Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba.” 21 Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu. 22 “Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.” 23 Kenaka anatembenukira kwa ophunzira ake nawawuza iwo okha kuti, “Ndi odala maso amene akuona zimene mukuonazi. 24 Pakuti kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuona zimene mukuonazi koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.” 25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” 26 Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?” 27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.” 28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.” 29 Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?” 30 Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. 31 Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. 32 Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. 33 Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. 34 Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. 35 Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’ 36 “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?” 37 Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.”Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.” 38 Yesu ndi ophunzira ake akuyenda, anafika pa mudzi kumene mayi wotchedwa Marita anamulandira Iye mʼnyumba mwake. 39 Mayiyu anali ndi mchemwali wake wotchedwa Mariya, amene anakhala pa mapazi a Yesu kumverera zimene Iye ankanena. 40 Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!” 41 Ambuye anati, “Marita, Marita, ukudandaula ndi kuvutika ndi zinthu zambiri, 42 koma chofunika nʼchimodzi chokha. Mariya wasankha chinthu chabwino, ndipo palibe angamulande chimenechi.”

In Other Versions

Luke 10 in the ANGEFD

Luke 10 in the ANTPNG2D

Luke 10 in the AS21

Luke 10 in the BAGH

Luke 10 in the BBPNG

Luke 10 in the BBT1E

Luke 10 in the BDS

Luke 10 in the BEV

Luke 10 in the BHAD

Luke 10 in the BIB

Luke 10 in the BLPT

Luke 10 in the BNT

Luke 10 in the BNTABOOT

Luke 10 in the BNTLV

Luke 10 in the BOATCB

Luke 10 in the BOATCB2

Luke 10 in the BOBCV

Luke 10 in the BOCNT

Luke 10 in the BOECS

Luke 10 in the BOHCB

Luke 10 in the BOHCV

Luke 10 in the BOHLNT

Luke 10 in the BOHNTLTAL

Luke 10 in the BOICB

Luke 10 in the BOILNTAP

Luke 10 in the BOITCV

Luke 10 in the BOKCV

Luke 10 in the BOKCV2

Luke 10 in the BOKHWOG

Luke 10 in the BOKSSV

Luke 10 in the BOLCB

Luke 10 in the BOLCB2

Luke 10 in the BOMCV

Luke 10 in the BONAV

Luke 10 in the BONCB

Luke 10 in the BONLT

Luke 10 in the BONUT2

Luke 10 in the BOPLNT

Luke 10 in the BOSCB

Luke 10 in the BOSNC

Luke 10 in the BOTLNT

Luke 10 in the BOVCB

Luke 10 in the BOYCB

Luke 10 in the BPBB

Luke 10 in the BPH

Luke 10 in the BSB

Luke 10 in the CCB

Luke 10 in the CUV

Luke 10 in the CUVS

Luke 10 in the DBT

Luke 10 in the DGDNT

Luke 10 in the DHNT

Luke 10 in the DNT

Luke 10 in the ELBE

Luke 10 in the EMTV

Luke 10 in the ESV

Luke 10 in the FBV

Luke 10 in the FEB

Luke 10 in the GGMNT

Luke 10 in the GNT

Luke 10 in the HARY

Luke 10 in the HNT

Luke 10 in the IRVA

Luke 10 in the IRVB

Luke 10 in the IRVG

Luke 10 in the IRVH

Luke 10 in the IRVK

Luke 10 in the IRVM

Luke 10 in the IRVM2

Luke 10 in the IRVO

Luke 10 in the IRVP

Luke 10 in the IRVT

Luke 10 in the IRVT2

Luke 10 in the IRVU

Luke 10 in the ISVN

Luke 10 in the JSNT

Luke 10 in the KAPI

Luke 10 in the KBT1ETNIK

Luke 10 in the KBV

Luke 10 in the KJV

Luke 10 in the KNFD

Luke 10 in the LBA

Luke 10 in the LBLA

Luke 10 in the LNT

Luke 10 in the LSV

Luke 10 in the MAAL

Luke 10 in the MBV

Luke 10 in the MBV2

Luke 10 in the MHNT

Luke 10 in the MKNFD

Luke 10 in the MNG

Luke 10 in the MNT

Luke 10 in the MNT2

Luke 10 in the MRS1T

Luke 10 in the NAA

Luke 10 in the NASB

Luke 10 in the NBLA

Luke 10 in the NBS

Luke 10 in the NBVTP

Luke 10 in the NET2

Luke 10 in the NIV11

Luke 10 in the NNT

Luke 10 in the NNT2

Luke 10 in the NNT3

Luke 10 in the PDDPT

Luke 10 in the PFNT

Luke 10 in the RMNT

Luke 10 in the SBIAS

Luke 10 in the SBIBS

Luke 10 in the SBIBS2

Luke 10 in the SBICS

Luke 10 in the SBIDS

Luke 10 in the SBIGS

Luke 10 in the SBIHS

Luke 10 in the SBIIS

Luke 10 in the SBIIS2

Luke 10 in the SBIIS3

Luke 10 in the SBIKS

Luke 10 in the SBIKS2

Luke 10 in the SBIMS

Luke 10 in the SBIOS

Luke 10 in the SBIPS

Luke 10 in the SBISS

Luke 10 in the SBITS

Luke 10 in the SBITS2

Luke 10 in the SBITS3

Luke 10 in the SBITS4

Luke 10 in the SBIUS

Luke 10 in the SBIVS

Luke 10 in the SBT

Luke 10 in the SBT1E

Luke 10 in the SCHL

Luke 10 in the SNT

Luke 10 in the SUSU

Luke 10 in the SUSU2

Luke 10 in the SYNO

Luke 10 in the TBIAOTANT

Luke 10 in the TBT1E

Luke 10 in the TBT1E2

Luke 10 in the TFTIP

Luke 10 in the TFTU

Luke 10 in the TGNTATF3T

Luke 10 in the THAI

Luke 10 in the TNFD

Luke 10 in the TNT

Luke 10 in the TNTIK

Luke 10 in the TNTIL

Luke 10 in the TNTIN

Luke 10 in the TNTIP

Luke 10 in the TNTIZ

Luke 10 in the TOMA

Luke 10 in the TTENT

Luke 10 in the UBG

Luke 10 in the UGV

Luke 10 in the UGV2

Luke 10 in the UGV3

Luke 10 in the VBL

Luke 10 in the VDCC

Luke 10 in the YALU

Luke 10 in the YAPE

Luke 10 in the YBVTP

Luke 10 in the ZBP