Luke 11 (BOGWICC)

1 Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.” 2 Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti: “ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe, ufumu wanu ubwere. 3 Mutipatse chakudya chathu chalero, 4 mutikhululukire machimo athu, monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ” 5 Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, 6 chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’ 7 “Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ 8 Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna. 9 “Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. 10 Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira. 11 “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? 12 Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? 13 Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!” 14 Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa. 15 Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.” 16 Ena anamuyesa pomufunsa chizindikiro chochokera kumwamba. 17 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka. 18 Ngati Satana adziwukira yekha, ufumu wake ungalimbe bwanji? Ine ndikunena izi chifukwa inu mukuti Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu. 19 Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu. 20 Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu. 21 “Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa. 22 Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake. 23 “Munthu amene sali mbali yanga ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ameneyo ndi womwaza. 24 “Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’ 25 Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza. 26 Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa iwowo ndipo imakalowa ndi kukhala mʼmenemo. Ndipo makhalidwe otsiriza a munthuyo amakhala oyipa kuposa oyamba aja.” 27 Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!” 28 Koma Yesu anayankha kuti, “Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.” 29 Pamene gulu la anthu limachuluka, Yesu anati, “Uno ndi mʼbado oyipa. Umafuna kuona chizindikiro chodabwitsa. Koma sadzachiona kupatula chizindikiro chija cha Yona. 30 Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu ku Ninive, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mʼbado uno. 31 Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi anthu a mʼbado uno ndipo idzawatsutsa, chifukwa iyo inachokera kumapeto a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Solomoni. 32 Anthu a ku Ninive adzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi mʼbado uno ndipo adzawutsutsa, pakuti anatembenuka mtima ndi ulaliki wa Yona. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Yona. 33 “Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika. 34 Diso lanu ndi nyale ya thupi lanu. Pamene maso anu ali bwino, thupi lanu lonse limadzaza ndi kuwunika. Koma ngati ali oyipa, thupi lanunso ndi lodzaza ndi mdima. 35 Onetsetsani tsono, kuti kuwunika kuli mwa inu si mdima. 36 Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.” 37 Yesu atamaliza kuyankhula, Mfarisi wina anamuyitana kuti akadye naye. Tsono Yesu analowa mʼnyumba ndi kukhala podyera. 38 Mfarisiyo anadabwa atazindikira kuti Yesu anayamba kudya wosatsata mwambo wawo wakasambidwe ka mʼmanja. 39 Kenaka Ambuye anamuwuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkati mwanu ndi modzaza ndi kudzikonda ndi zoyipa. 40 Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja? 41 Koma popereka kwa osauka, perekani chimene chili mʼkati ndipo chilichonse chidzakhala choyera. 42 “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi. 43 “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malonje mʼmalo a pa msika. 44 “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa muli ngati manda osawaka, amene anthu amangoyendapo, osawadziwa.” 45 Mmodzi mwa akatswiri a Malamulo anamuyankha Iye nati, “Aphunzitsi, pamene mukunena zinthu izi, mukutinyoza ifenso?” 46 Yesu anayankha kuti, “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize. 47 “Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha. 48 Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo. 49 Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’ 50 Choncho mʼbado uwu udzasenza magazi a aneneri onse amene anakhetsedwa kuyambira pachiyambi cha dziko, 51 kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi. 52 “Tsoka kwa inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mwachotsa kiyi wachidziwitso inu eni akenu musanalowemo, ndipo mwatsekerezanso iwo amene amalowa.” 53 Pamene Yesu anachokamo, Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo anayamba kumamutsutsa koopsa ndi kumupanikiza ndi mafunso, 54 pofuna kumukola muchina chilichonse chimene Iye angayankhule.

In Other Versions

Luke 11 in the ANGEFD

Luke 11 in the ANTPNG2D

Luke 11 in the AS21

Luke 11 in the BAGH

Luke 11 in the BBPNG

Luke 11 in the BBT1E

Luke 11 in the BDS

Luke 11 in the BEV

Luke 11 in the BHAD

Luke 11 in the BIB

Luke 11 in the BLPT

Luke 11 in the BNT

Luke 11 in the BNTABOOT

Luke 11 in the BNTLV

Luke 11 in the BOATCB

Luke 11 in the BOATCB2

Luke 11 in the BOBCV

Luke 11 in the BOCNT

Luke 11 in the BOECS

Luke 11 in the BOHCB

Luke 11 in the BOHCV

Luke 11 in the BOHLNT

Luke 11 in the BOHNTLTAL

Luke 11 in the BOICB

Luke 11 in the BOILNTAP

Luke 11 in the BOITCV

Luke 11 in the BOKCV

Luke 11 in the BOKCV2

Luke 11 in the BOKHWOG

Luke 11 in the BOKSSV

Luke 11 in the BOLCB

Luke 11 in the BOLCB2

Luke 11 in the BOMCV

Luke 11 in the BONAV

Luke 11 in the BONCB

Luke 11 in the BONLT

Luke 11 in the BONUT2

Luke 11 in the BOPLNT

Luke 11 in the BOSCB

Luke 11 in the BOSNC

Luke 11 in the BOTLNT

Luke 11 in the BOVCB

Luke 11 in the BOYCB

Luke 11 in the BPBB

Luke 11 in the BPH

Luke 11 in the BSB

Luke 11 in the CCB

Luke 11 in the CUV

Luke 11 in the CUVS

Luke 11 in the DBT

Luke 11 in the DGDNT

Luke 11 in the DHNT

Luke 11 in the DNT

Luke 11 in the ELBE

Luke 11 in the EMTV

Luke 11 in the ESV

Luke 11 in the FBV

Luke 11 in the FEB

Luke 11 in the GGMNT

Luke 11 in the GNT

Luke 11 in the HARY

Luke 11 in the HNT

Luke 11 in the IRVA

Luke 11 in the IRVB

Luke 11 in the IRVG

Luke 11 in the IRVH

Luke 11 in the IRVK

Luke 11 in the IRVM

Luke 11 in the IRVM2

Luke 11 in the IRVO

Luke 11 in the IRVP

Luke 11 in the IRVT

Luke 11 in the IRVT2

Luke 11 in the IRVU

Luke 11 in the ISVN

Luke 11 in the JSNT

Luke 11 in the KAPI

Luke 11 in the KBT1ETNIK

Luke 11 in the KBV

Luke 11 in the KJV

Luke 11 in the KNFD

Luke 11 in the LBA

Luke 11 in the LBLA

Luke 11 in the LNT

Luke 11 in the LSV

Luke 11 in the MAAL

Luke 11 in the MBV

Luke 11 in the MBV2

Luke 11 in the MHNT

Luke 11 in the MKNFD

Luke 11 in the MNG

Luke 11 in the MNT

Luke 11 in the MNT2

Luke 11 in the MRS1T

Luke 11 in the NAA

Luke 11 in the NASB

Luke 11 in the NBLA

Luke 11 in the NBS

Luke 11 in the NBVTP

Luke 11 in the NET2

Luke 11 in the NIV11

Luke 11 in the NNT

Luke 11 in the NNT2

Luke 11 in the NNT3

Luke 11 in the PDDPT

Luke 11 in the PFNT

Luke 11 in the RMNT

Luke 11 in the SBIAS

Luke 11 in the SBIBS

Luke 11 in the SBIBS2

Luke 11 in the SBICS

Luke 11 in the SBIDS

Luke 11 in the SBIGS

Luke 11 in the SBIHS

Luke 11 in the SBIIS

Luke 11 in the SBIIS2

Luke 11 in the SBIIS3

Luke 11 in the SBIKS

Luke 11 in the SBIKS2

Luke 11 in the SBIMS

Luke 11 in the SBIOS

Luke 11 in the SBIPS

Luke 11 in the SBISS

Luke 11 in the SBITS

Luke 11 in the SBITS2

Luke 11 in the SBITS3

Luke 11 in the SBITS4

Luke 11 in the SBIUS

Luke 11 in the SBIVS

Luke 11 in the SBT

Luke 11 in the SBT1E

Luke 11 in the SCHL

Luke 11 in the SNT

Luke 11 in the SUSU

Luke 11 in the SUSU2

Luke 11 in the SYNO

Luke 11 in the TBIAOTANT

Luke 11 in the TBT1E

Luke 11 in the TBT1E2

Luke 11 in the TFTIP

Luke 11 in the TFTU

Luke 11 in the TGNTATF3T

Luke 11 in the THAI

Luke 11 in the TNFD

Luke 11 in the TNT

Luke 11 in the TNTIK

Luke 11 in the TNTIL

Luke 11 in the TNTIN

Luke 11 in the TNTIP

Luke 11 in the TNTIZ

Luke 11 in the TOMA

Luke 11 in the TTENT

Luke 11 in the UBG

Luke 11 in the UGV

Luke 11 in the UGV2

Luke 11 in the UGV3

Luke 11 in the VBL

Luke 11 in the VDCC

Luke 11 in the YALU

Luke 11 in the YAPE

Luke 11 in the YBVTP

Luke 11 in the ZBP