Malachi 3 (BOGWICC)
1 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga amene adzakonza njira pamaso panga. Kenaka mwadzidzidzi Ambuye amene mukumufunafuna adzafika ku Nyumba yake. Mthenga wapangano amene mukumuyembekezera adzabwera.” 2 Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa. 3 Iye adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri woyenga ndi woyeretsa siliva. Iye adzayeretsa Alevi ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva. Pamenepo Yehova adzakhala ndi anthu amene azidzabweretsa zopereka mwachilungamo, 4 ndipo Yehova adzalandira zopereka za Yuda ndi Yerusalemu, ngati masiku akale, masiku amakedzana. 5 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.” 6 “Ine ndine Yehova, ndipo sindisintha. Choncho inu zidzukulu za Yakobo, simunawonongedwe. 7 Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’ 8 “Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’“Pa zakhumi ndi pa zopereka. 9 Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. 10 Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo. 11 Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 12 “Motero anthu amitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 13 Yehova akuti, “Mwayankhula mawu owawa onena za Ine.“Komabe inu mukufunsa kuti, ‘Kodi tanena chiyani chotsutsana nanu?’ 14 “Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkosapindulitsa. Kodi timapindulanji pochita zofuna zake, ndi kumayenda ngati anamfedwa pamaso pa Yehova Wamphamvuzonse? 15 Koma tsono ife timati anthu odzikuza ndiye odalitsika. Kunena zoona anthu oyipa ndiye amapeza bwino, ngakhale amene amanyoza Mulungu amapulumuka.’ ” 16 Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake. 17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, tsiku limene Ine ndidzachita izi, adzakhala angaanga. Ndidzawaleka osawalanga monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira. 18 Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu olungama ndi oyipa, pakati pa amene amatumikira Mulungu ndi amene satumikira Mulungu.”
In Other Versions
Malachi 3 in the ANGEFD
Malachi 3 in the ANTPNG2D
Malachi 3 in the AS21
Malachi 3 in the BAGH
Malachi 3 in the BBPNG
Malachi 3 in the BBT1E
Malachi 3 in the BDS
Malachi 3 in the BEV
Malachi 3 in the BHAD
Malachi 3 in the BIB
Malachi 3 in the BLPT
Malachi 3 in the BNT
Malachi 3 in the BNTABOOT
Malachi 3 in the BNTLV
Malachi 3 in the BOATCB
Malachi 3 in the BOATCB2
Malachi 3 in the BOBCV
Malachi 3 in the BOCNT
Malachi 3 in the BOECS
Malachi 3 in the BOHCB
Malachi 3 in the BOHCV
Malachi 3 in the BOHLNT
Malachi 3 in the BOHNTLTAL
Malachi 3 in the BOICB
Malachi 3 in the BOILNTAP
Malachi 3 in the BOITCV
Malachi 3 in the BOKCV
Malachi 3 in the BOKCV2
Malachi 3 in the BOKHWOG
Malachi 3 in the BOKSSV
Malachi 3 in the BOLCB
Malachi 3 in the BOLCB2
Malachi 3 in the BOMCV
Malachi 3 in the BONAV
Malachi 3 in the BONCB
Malachi 3 in the BONLT
Malachi 3 in the BONUT2
Malachi 3 in the BOPLNT
Malachi 3 in the BOSCB
Malachi 3 in the BOSNC
Malachi 3 in the BOTLNT
Malachi 3 in the BOVCB
Malachi 3 in the BOYCB
Malachi 3 in the BPBB
Malachi 3 in the BPH
Malachi 3 in the BSB
Malachi 3 in the CCB
Malachi 3 in the CUV
Malachi 3 in the CUVS
Malachi 3 in the DBT
Malachi 3 in the DGDNT
Malachi 3 in the DHNT
Malachi 3 in the DNT
Malachi 3 in the ELBE
Malachi 3 in the EMTV
Malachi 3 in the ESV
Malachi 3 in the FBV
Malachi 3 in the FEB
Malachi 3 in the GGMNT
Malachi 3 in the GNT
Malachi 3 in the HARY
Malachi 3 in the HNT
Malachi 3 in the IRVA
Malachi 3 in the IRVB
Malachi 3 in the IRVG
Malachi 3 in the IRVH
Malachi 3 in the IRVK
Malachi 3 in the IRVM
Malachi 3 in the IRVM2
Malachi 3 in the IRVO
Malachi 3 in the IRVP
Malachi 3 in the IRVT
Malachi 3 in the IRVT2
Malachi 3 in the IRVU
Malachi 3 in the ISVN
Malachi 3 in the JSNT
Malachi 3 in the KAPI
Malachi 3 in the KBT1ETNIK
Malachi 3 in the KBV
Malachi 3 in the KJV
Malachi 3 in the KNFD
Malachi 3 in the LBA
Malachi 3 in the LBLA
Malachi 3 in the LNT
Malachi 3 in the LSV
Malachi 3 in the MAAL
Malachi 3 in the MBV
Malachi 3 in the MBV2
Malachi 3 in the MHNT
Malachi 3 in the MKNFD
Malachi 3 in the MNG
Malachi 3 in the MNT
Malachi 3 in the MNT2
Malachi 3 in the MRS1T
Malachi 3 in the NAA
Malachi 3 in the NASB
Malachi 3 in the NBLA
Malachi 3 in the NBS
Malachi 3 in the NBVTP
Malachi 3 in the NET2
Malachi 3 in the NIV11
Malachi 3 in the NNT
Malachi 3 in the NNT2
Malachi 3 in the NNT3
Malachi 3 in the PDDPT
Malachi 3 in the PFNT
Malachi 3 in the RMNT
Malachi 3 in the SBIAS
Malachi 3 in the SBIBS
Malachi 3 in the SBIBS2
Malachi 3 in the SBICS
Malachi 3 in the SBIDS
Malachi 3 in the SBIGS
Malachi 3 in the SBIHS
Malachi 3 in the SBIIS
Malachi 3 in the SBIIS2
Malachi 3 in the SBIIS3
Malachi 3 in the SBIKS
Malachi 3 in the SBIKS2
Malachi 3 in the SBIMS
Malachi 3 in the SBIOS
Malachi 3 in the SBIPS
Malachi 3 in the SBISS
Malachi 3 in the SBITS
Malachi 3 in the SBITS2
Malachi 3 in the SBITS3
Malachi 3 in the SBITS4
Malachi 3 in the SBIUS
Malachi 3 in the SBIVS
Malachi 3 in the SBT
Malachi 3 in the SBT1E
Malachi 3 in the SCHL
Malachi 3 in the SNT
Malachi 3 in the SUSU
Malachi 3 in the SUSU2
Malachi 3 in the SYNO
Malachi 3 in the TBIAOTANT
Malachi 3 in the TBT1E
Malachi 3 in the TBT1E2
Malachi 3 in the TFTIP
Malachi 3 in the TFTU
Malachi 3 in the TGNTATF3T
Malachi 3 in the THAI
Malachi 3 in the TNFD
Malachi 3 in the TNT
Malachi 3 in the TNTIK
Malachi 3 in the TNTIL
Malachi 3 in the TNTIN
Malachi 3 in the TNTIP
Malachi 3 in the TNTIZ
Malachi 3 in the TOMA
Malachi 3 in the TTENT
Malachi 3 in the UBG
Malachi 3 in the UGV
Malachi 3 in the UGV2
Malachi 3 in the UGV3
Malachi 3 in the VBL
Malachi 3 in the VDCC
Malachi 3 in the YALU
Malachi 3 in the YAPE
Malachi 3 in the YBVTP
Malachi 3 in the ZBP