Matthew 23 (BOGWICC)

1 Pamenepo Yesu anati kwa magulu a anthu ndi ophunzira ake: 2 “Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi amakhala pa mpando wa Mose. 3 Choncho muziwamvera ndi kuchita chilichonse chimene akuwuzani. Koma musachite zimene amachita, popeza sachita zimene amaphunzitsa. 4 Amamanga akatundu olemera nawayika pa mapewa a anthu, koma iwo eni safuna kuwanyamula. 5 “Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo. 6 Amakonda malo aulemu pa maphwando ndi malo ofunika kwambiri mʼmasunagoge. 7 Amakondwera ndi kupatsidwa moni mʼmisika ndi kutchulidwa kuti ‘Aphunzitsi.’ 8 “Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale. 9 Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba. 10 Komanso musamatchedwenso ‘Mtsogoleri,’ pakuti muli naye Mtsogoleri mmodzi amene ndi Khristu. 11 Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani. 12 Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa. 13 “Tsoka kwa inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumatseka pa khomo la kumwamba kuti anthu asalowemo. Eni akenu simulowamo komanso simulola kuti ena amene akufuna kulowa kuti alowe. 14 Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumawadyera akazi amasiye chuma chawo, kwinaku nʼkumanamizira kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa. 15 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumayenda maulendo ambiri pa mtunda ndi pa nyanja kuti mutembenuze munthu mmodzi, ndipo akatembenuka, mumamusandutsa kukhala mwana wa gehena kawiri kuposa inu. 16 “Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu! Mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula Nyumba ya Mulungu, zilibe kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula ndalama zagolide za mʼNyumbayo, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’ 17 Inu akhungu opusa! Chopambana nʼchiyani: ndalama zagolide, kapena Nyumba imene imayeretsa golideyo? 18 Ndiponso mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula guwa lansembe, sizitanthauza kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula mphatso ya paguwa lansembe, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’ 19 Inu anthu akhungu! Chopambana nʼchiyani: mphatso, kapena guwa limene limayeretsa mphatsoyo? 20 Chifukwa chake, iye amene alumbira kutchula guwa alumbira pa ilo ndi pa chilichonse chili pamenepo. 21 Ndipo iye wolumbira potchula Nyumba ya Mulungu alumbira pa Nyumbayo ndi pa Iye amene amakhala mʼmenemo. 22 Ndipo iye wolumbira kutchula kumwamba alumbira kutchula mpando waufumu wa Mulungu ndi pa Iye wokhalapo. 23 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo. 24 Atsogoleri akhungu inu! Mumachotsa kantchentche mu chakumwa chanu koma mumameza ngamira. 25 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkatimo mwadzaza ndi dyera ndi kusadziretsa. 26 Afarisi akhungu! Poyamba tsukani mʼkati mwa chikho ndi mbale, ndipo kunja kwake kudzakhalanso koyera. 27 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Muli ngati ziliza pa manda zowala kunja zimene zimaoneka zokongola koma mʼkatimo mwadzaza mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zina zonse. 28 Chimodzimodzinso, kunja mumaoneka kwa anthu kuti ndinu olungama koma mʼkatimo ndinu odzaza ndi chinyengo ndi zoyipa zina. 29 “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumamanga ziliza za aneneri ndi kukongoletsa manda a olungama. 30 Ndipo mumati, ‘Ngati tikanakhala mʼmasiku a makolo athu sitikanakhetsa nawo magazi a aneneri.’ 31 Potero mukutsimikiza kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri. 32 Dzazani inu muyeso wa uchimo wa makolo anu! 33 “Njoka inu! Ana amamba! Mudzachithawa bwanji chilango cha gehena? 34 Choncho ndi kutumizirani aneneri ndi anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena a iwo mudzawapha ndi kuwapachika; ena mudzawakwapula mʼmasunagoge anu ndi kuwafunafuna kuchokera mudzi wina kufikira wina. 35 Ndipo magazi onse a olungama amene anakhetsedwa pansi pano, kuyambira magazi a Abele, olungama kufikira Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, adzakhala pa inu. 36 Zoonadi, ndikuwuzani kuti zonsezi zidzafika pa mʼbado uno. 37 “Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune. 38 Taona, nyumba yako yasiyidwa ya bwinja. 39 Chifukwa chake ndikuwuza kuti simudzandionanso kufikira pamene mudzati, ‘Wodala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye.’ ”

In Other Versions

Matthew 23 in the ANGEFD

Matthew 23 in the ANTPNG2D

Matthew 23 in the AS21

Matthew 23 in the BAGH

Matthew 23 in the BBPNG

Matthew 23 in the BBT1E

Matthew 23 in the BDS

Matthew 23 in the BEV

Matthew 23 in the BHAD

Matthew 23 in the BIB

Matthew 23 in the BLPT

Matthew 23 in the BNT

Matthew 23 in the BNTABOOT

Matthew 23 in the BNTLV

Matthew 23 in the BOATCB

Matthew 23 in the BOATCB2

Matthew 23 in the BOBCV

Matthew 23 in the BOCNT

Matthew 23 in the BOECS

Matthew 23 in the BOHCB

Matthew 23 in the BOHCV

Matthew 23 in the BOHLNT

Matthew 23 in the BOHNTLTAL

Matthew 23 in the BOICB

Matthew 23 in the BOILNTAP

Matthew 23 in the BOITCV

Matthew 23 in the BOKCV

Matthew 23 in the BOKCV2

Matthew 23 in the BOKHWOG

Matthew 23 in the BOKSSV

Matthew 23 in the BOLCB

Matthew 23 in the BOLCB2

Matthew 23 in the BOMCV

Matthew 23 in the BONAV

Matthew 23 in the BONCB

Matthew 23 in the BONLT

Matthew 23 in the BONUT2

Matthew 23 in the BOPLNT

Matthew 23 in the BOSCB

Matthew 23 in the BOSNC

Matthew 23 in the BOTLNT

Matthew 23 in the BOVCB

Matthew 23 in the BOYCB

Matthew 23 in the BPBB

Matthew 23 in the BPH

Matthew 23 in the BSB

Matthew 23 in the CCB

Matthew 23 in the CUV

Matthew 23 in the CUVS

Matthew 23 in the DBT

Matthew 23 in the DGDNT

Matthew 23 in the DHNT

Matthew 23 in the DNT

Matthew 23 in the ELBE

Matthew 23 in the EMTV

Matthew 23 in the ESV

Matthew 23 in the FBV

Matthew 23 in the FEB

Matthew 23 in the GGMNT

Matthew 23 in the GNT

Matthew 23 in the HARY

Matthew 23 in the HNT

Matthew 23 in the IRVA

Matthew 23 in the IRVB

Matthew 23 in the IRVG

Matthew 23 in the IRVH

Matthew 23 in the IRVK

Matthew 23 in the IRVM

Matthew 23 in the IRVM2

Matthew 23 in the IRVO

Matthew 23 in the IRVP

Matthew 23 in the IRVT

Matthew 23 in the IRVT2

Matthew 23 in the IRVU

Matthew 23 in the ISVN

Matthew 23 in the JSNT

Matthew 23 in the KAPI

Matthew 23 in the KBT1ETNIK

Matthew 23 in the KBV

Matthew 23 in the KJV

Matthew 23 in the KNFD

Matthew 23 in the LBA

Matthew 23 in the LBLA

Matthew 23 in the LNT

Matthew 23 in the LSV

Matthew 23 in the MAAL

Matthew 23 in the MBV

Matthew 23 in the MBV2

Matthew 23 in the MHNT

Matthew 23 in the MKNFD

Matthew 23 in the MNG

Matthew 23 in the MNT

Matthew 23 in the MNT2

Matthew 23 in the MRS1T

Matthew 23 in the NAA

Matthew 23 in the NASB

Matthew 23 in the NBLA

Matthew 23 in the NBS

Matthew 23 in the NBVTP

Matthew 23 in the NET2

Matthew 23 in the NIV11

Matthew 23 in the NNT

Matthew 23 in the NNT2

Matthew 23 in the NNT3

Matthew 23 in the PDDPT

Matthew 23 in the PFNT

Matthew 23 in the RMNT

Matthew 23 in the SBIAS

Matthew 23 in the SBIBS

Matthew 23 in the SBIBS2

Matthew 23 in the SBICS

Matthew 23 in the SBIDS

Matthew 23 in the SBIGS

Matthew 23 in the SBIHS

Matthew 23 in the SBIIS

Matthew 23 in the SBIIS2

Matthew 23 in the SBIIS3

Matthew 23 in the SBIKS

Matthew 23 in the SBIKS2

Matthew 23 in the SBIMS

Matthew 23 in the SBIOS

Matthew 23 in the SBIPS

Matthew 23 in the SBISS

Matthew 23 in the SBITS

Matthew 23 in the SBITS2

Matthew 23 in the SBITS3

Matthew 23 in the SBITS4

Matthew 23 in the SBIUS

Matthew 23 in the SBIVS

Matthew 23 in the SBT

Matthew 23 in the SBT1E

Matthew 23 in the SCHL

Matthew 23 in the SNT

Matthew 23 in the SUSU

Matthew 23 in the SUSU2

Matthew 23 in the SYNO

Matthew 23 in the TBIAOTANT

Matthew 23 in the TBT1E

Matthew 23 in the TBT1E2

Matthew 23 in the TFTIP

Matthew 23 in the TFTU

Matthew 23 in the TGNTATF3T

Matthew 23 in the THAI

Matthew 23 in the TNFD

Matthew 23 in the TNT

Matthew 23 in the TNTIK

Matthew 23 in the TNTIL

Matthew 23 in the TNTIN

Matthew 23 in the TNTIP

Matthew 23 in the TNTIZ

Matthew 23 in the TOMA

Matthew 23 in the TTENT

Matthew 23 in the UBG

Matthew 23 in the UGV

Matthew 23 in the UGV2

Matthew 23 in the UGV3

Matthew 23 in the VBL

Matthew 23 in the VDCC

Matthew 23 in the YALU

Matthew 23 in the YAPE

Matthew 23 in the YBVTP

Matthew 23 in the ZBP