Matthew 7 (BOGWICC)
1 “Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe. 2 Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo. 3 “Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako? 4 Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, ‘Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako? 5 Wachiphamaso iwe! Yamba wachotsa chimtengo chili mʼdiso mwako ndipo pamenepo udzatha kuona bwino ndi kuchotsa kachitsotso kali mʼdiso mwa mʼbale wako. 6 “Musapatse agalu zinthu zopatulika; kapena musaponyere nkhumba ngale zanu. Pakuti ngati mutero, zidzaziponda ndipo pomwepo zidzakutembenukirani ndi kukudulani nthulinthuli. 7 “Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. 8 Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira. 9 “Ndani mwa inu, mwana wake akamupempha buledi amamupatsa mwala? 10 Kapena ngati mwana apempha nsomba, kodi amamupatsa njoka? 11 Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha? 12 Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa. 13 “Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. 14 Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo. 15 “Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa. 16 Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula? 17 Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa. 18 Mtengo wabwino sungabale chipatso choyipa, ndi mtengo woyipa sungabale chipatso chabwino. 19 Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto. 20 Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira. 21 “Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. 22 Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ 23 Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’ 24 “Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26 Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga. 27 Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.” 28 Yesu atamaliza kunena zonsezi, magulu a anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, 29 chifukwa anaphunzitsa ngati amene anali ndi ulamuliro osati ngati aphunzitsi amalamulo.
In Other Versions
Matthew 7 in the ANGEFD
Matthew 7 in the ANTPNG2D
Matthew 7 in the AS21
Matthew 7 in the BAGH
Matthew 7 in the BBPNG
Matthew 7 in the BBT1E
Matthew 7 in the BDS
Matthew 7 in the BEV
Matthew 7 in the BHAD
Matthew 7 in the BIB
Matthew 7 in the BLPT
Matthew 7 in the BNT
Matthew 7 in the BNTABOOT
Matthew 7 in the BNTLV
Matthew 7 in the BOATCB
Matthew 7 in the BOATCB2
Matthew 7 in the BOBCV
Matthew 7 in the BOCNT
Matthew 7 in the BOECS
Matthew 7 in the BOHCB
Matthew 7 in the BOHCV
Matthew 7 in the BOHLNT
Matthew 7 in the BOHNTLTAL
Matthew 7 in the BOICB
Matthew 7 in the BOILNTAP
Matthew 7 in the BOITCV
Matthew 7 in the BOKCV
Matthew 7 in the BOKCV2
Matthew 7 in the BOKHWOG
Matthew 7 in the BOKSSV
Matthew 7 in the BOLCB
Matthew 7 in the BOLCB2
Matthew 7 in the BOMCV
Matthew 7 in the BONAV
Matthew 7 in the BONCB
Matthew 7 in the BONLT
Matthew 7 in the BONUT2
Matthew 7 in the BOPLNT
Matthew 7 in the BOSCB
Matthew 7 in the BOSNC
Matthew 7 in the BOTLNT
Matthew 7 in the BOVCB
Matthew 7 in the BOYCB
Matthew 7 in the BPBB
Matthew 7 in the BPH
Matthew 7 in the BSB
Matthew 7 in the CCB
Matthew 7 in the CUV
Matthew 7 in the CUVS
Matthew 7 in the DBT
Matthew 7 in the DGDNT
Matthew 7 in the DHNT
Matthew 7 in the DNT
Matthew 7 in the ELBE
Matthew 7 in the EMTV
Matthew 7 in the ESV
Matthew 7 in the FBV
Matthew 7 in the FEB
Matthew 7 in the GGMNT
Matthew 7 in the GNT
Matthew 7 in the HARY
Matthew 7 in the HNT
Matthew 7 in the IRVA
Matthew 7 in the IRVB
Matthew 7 in the IRVG
Matthew 7 in the IRVH
Matthew 7 in the IRVK
Matthew 7 in the IRVM
Matthew 7 in the IRVM2
Matthew 7 in the IRVO
Matthew 7 in the IRVP
Matthew 7 in the IRVT
Matthew 7 in the IRVT2
Matthew 7 in the IRVU
Matthew 7 in the ISVN
Matthew 7 in the JSNT
Matthew 7 in the KAPI
Matthew 7 in the KBT1ETNIK
Matthew 7 in the KBV
Matthew 7 in the KJV
Matthew 7 in the KNFD
Matthew 7 in the LBA
Matthew 7 in the LBLA
Matthew 7 in the LNT
Matthew 7 in the LSV
Matthew 7 in the MAAL
Matthew 7 in the MBV
Matthew 7 in the MBV2
Matthew 7 in the MHNT
Matthew 7 in the MKNFD
Matthew 7 in the MNG
Matthew 7 in the MNT
Matthew 7 in the MNT2
Matthew 7 in the MRS1T
Matthew 7 in the NAA
Matthew 7 in the NASB
Matthew 7 in the NBLA
Matthew 7 in the NBS
Matthew 7 in the NBVTP
Matthew 7 in the NET2
Matthew 7 in the NIV11
Matthew 7 in the NNT
Matthew 7 in the NNT2
Matthew 7 in the NNT3
Matthew 7 in the PDDPT
Matthew 7 in the PFNT
Matthew 7 in the RMNT
Matthew 7 in the SBIAS
Matthew 7 in the SBIBS
Matthew 7 in the SBIBS2
Matthew 7 in the SBICS
Matthew 7 in the SBIDS
Matthew 7 in the SBIGS
Matthew 7 in the SBIHS
Matthew 7 in the SBIIS
Matthew 7 in the SBIIS2
Matthew 7 in the SBIIS3
Matthew 7 in the SBIKS
Matthew 7 in the SBIKS2
Matthew 7 in the SBIMS
Matthew 7 in the SBIOS
Matthew 7 in the SBIPS
Matthew 7 in the SBISS
Matthew 7 in the SBITS
Matthew 7 in the SBITS2
Matthew 7 in the SBITS3
Matthew 7 in the SBITS4
Matthew 7 in the SBIUS
Matthew 7 in the SBIVS
Matthew 7 in the SBT
Matthew 7 in the SBT1E
Matthew 7 in the SCHL
Matthew 7 in the SNT
Matthew 7 in the SUSU
Matthew 7 in the SUSU2
Matthew 7 in the SYNO
Matthew 7 in the TBIAOTANT
Matthew 7 in the TBT1E
Matthew 7 in the TBT1E2
Matthew 7 in the TFTIP
Matthew 7 in the TFTU
Matthew 7 in the TGNTATF3T
Matthew 7 in the THAI
Matthew 7 in the TNFD
Matthew 7 in the TNT
Matthew 7 in the TNTIK
Matthew 7 in the TNTIL
Matthew 7 in the TNTIN
Matthew 7 in the TNTIP
Matthew 7 in the TNTIZ
Matthew 7 in the TOMA
Matthew 7 in the TTENT
Matthew 7 in the UBG
Matthew 7 in the UGV
Matthew 7 in the UGV2
Matthew 7 in the UGV3
Matthew 7 in the VBL
Matthew 7 in the VDCC
Matthew 7 in the YALU
Matthew 7 in the YAPE
Matthew 7 in the YBVTP
Matthew 7 in the ZBP