Nehemiah 5 (BOGWICC)

1 Tsono anthu ena ndi akazi awo anayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzawo. 2 Ena ankanena kuti, “Ife ndi ana athu aamuna ndi aakazi, tilipo ochuluka kwambiri. Choncho tikufuna tirigu kuti tidye ndi kukhala ndi moyo.” 3 Panali ena amene ankanena kuti, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu ya mphesa ndi nyumba zathu ngati chikole kuti tipeze tirigu chifukwa njala yakula.” 4 Panalinso ena amene ankanena kuti, “ife tinachita kukongola ndalama zoti tipereke msonkho wa minda ndi mitengo yathu ya mphesa kwa mfumu. 5 Ngakhale kuti ndife amodzi ndi abale athuwa, ndipo ngakhalenso ana athu ndi ofanana ndi ana awo, ife tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo. Ena mwa ana athu aakazi atengedwa kale ukapolo. Ife tilibe mphamvu yochitapo kanthu popeza anthu ena anatenga kale minda yathu ndi mitengo yathu ya mphesa.” 6 Nditamva madandawulo awo ndi zimene amanenazi ndinapsa mtima kwambiri. 7 Nditalingalira bwino ndinatsimikiza zoti ndichitepo kanthu ndipo kenaka ndinawadzudzula anthu olemekezeka ndi akuluakuluwo. Ndinawawuza kuti, “Zoona ndithu inu nʼkumalipiritsana chiwongoladzanja chachikulu anthu apachibale nokhanokha!” Choncho ndinayitanitsa msonkhano waukulu kuti ndiwazenge mlandu 8 ndipo ndinati, “Monga zakhaliramu ife tikutha kuwombola abale anthu amene anagulitsidwa ukapolo kwa anthu ena. Kodi tsopano inu mukugulitsanso abale anu kwa anzawo kuti ife tiwumirizidwe kuwawombola?” Iwo anakhala chete, chifukwa sanapeze mawu oti anene. 9 Kotero ndinapitiriza kunena kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi inu simungakhale ndi moyo woopa Mulungu wathu kuti tipewe kunyoza kwa adani athu, anthu a mitunda inayi? 10 Ine ndi abale anga ndiponso antchito anga tikuwakongozanso anthuwa ndalama ndi tirigu. Ndipo tiyeni tilekeretu zolandira chiwongoladzanja! 11 Abwezereni lero lomwe minda yawo, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndiponso nyumba zawo. Muwabwezerenso chiwongoladzanja cha ndalama, tirigu, vinyo ndi mafuta zimene munatenga.” 12 Iwo anayankha kuti, “Ife tidzawabwezera zimenezi popanda kupemphapo kanthu kalikonse kwa iwo. Tidzachita monga mwanena.”Pambuyo pake ndinayitanitsa ansembe ndipo pamaso pawo ndinawalumbiritsa atsogoleriwo ndi akuluakuluwo kuti adzachitadi zomwe analonjezazo. 13 Ndipo inenso ndinakutumula chovala changa ndi kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu wosasunga malonjezano ake. Amulande nyumba yake ndi katundu wake ndi kumusandutsa mʼmphawi!”Apo msonkhano wonse unati, “Ameni” natamanda Yehova. Ndipo anthu aja anachita monga analonjezera. 14 Ndiponso kuyambira nthawi imene anandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda, kuchokera chaka cha makumi awiri mpaka chaka cha 32 muulamuliro wa ufumu wa Aritasasita, ndiye kuti kwa zaka zokwana 12, ine ngakhale abale anga sitinalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. 15 Koma abwanamkubwa akale ankasautsa anthu. Iwo ankalanda anthu chakudya ndi vinyo ndi kuwalipiritsanso masekeli asiliva makumi anayi. Ngakhalenso antchito awo amavutitsa anthu kwambiri. Koma ine sindinachite zimenezo chifukwa ndimaopa Mulungu. 16 Ndiponso ndinadzipereka kugwira ntchito yomanga khoma la mzinda wa Yerusalemu popanda ngakhale kugulapo munda. Antchito anganso anasonkhana komweko kuti agwire ntchito ndipo sitinafunenso malo ena. 17 Kuwonjezera apa, ndinkadyetsa Ayuda, akuluakulu kuphatikizanso anthu amene ankabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ya anthu otizungulira okwanira 150. 18 Tsiku lililonse pamaphikidwa ngʼombe imodzi, nkhosa zabwino zisanu ndi imodzi pamodzi ndi nkhuku. Ndipo pakutha pa masiku khumi aliwonse pankakhala matumba achikopa ochuluka a vinyo wa mitundu yonse. Ngakhale zinali choncho, Ine sindinatenge chakudya choperekedwa kwa bwanamkubwa, chifukwa izi zinali zosautsa anthu. 19 Kuti zinthu zindiyendere bwino, kumbukirani Yehova Mulungu wanga pa zonse zimene ndachitira anthu awa.

In Other Versions

Nehemiah 5 in the ANGEFD

Nehemiah 5 in the ANTPNG2D

Nehemiah 5 in the AS21

Nehemiah 5 in the BAGH

Nehemiah 5 in the BBPNG

Nehemiah 5 in the BBT1E

Nehemiah 5 in the BDS

Nehemiah 5 in the BEV

Nehemiah 5 in the BHAD

Nehemiah 5 in the BIB

Nehemiah 5 in the BLPT

Nehemiah 5 in the BNT

Nehemiah 5 in the BNTABOOT

Nehemiah 5 in the BNTLV

Nehemiah 5 in the BOATCB

Nehemiah 5 in the BOATCB2

Nehemiah 5 in the BOBCV

Nehemiah 5 in the BOCNT

Nehemiah 5 in the BOECS

Nehemiah 5 in the BOHCB

Nehemiah 5 in the BOHCV

Nehemiah 5 in the BOHLNT

Nehemiah 5 in the BOHNTLTAL

Nehemiah 5 in the BOICB

Nehemiah 5 in the BOILNTAP

Nehemiah 5 in the BOITCV

Nehemiah 5 in the BOKCV

Nehemiah 5 in the BOKCV2

Nehemiah 5 in the BOKHWOG

Nehemiah 5 in the BOKSSV

Nehemiah 5 in the BOLCB

Nehemiah 5 in the BOLCB2

Nehemiah 5 in the BOMCV

Nehemiah 5 in the BONAV

Nehemiah 5 in the BONCB

Nehemiah 5 in the BONLT

Nehemiah 5 in the BONUT2

Nehemiah 5 in the BOPLNT

Nehemiah 5 in the BOSCB

Nehemiah 5 in the BOSNC

Nehemiah 5 in the BOTLNT

Nehemiah 5 in the BOVCB

Nehemiah 5 in the BOYCB

Nehemiah 5 in the BPBB

Nehemiah 5 in the BPH

Nehemiah 5 in the BSB

Nehemiah 5 in the CCB

Nehemiah 5 in the CUV

Nehemiah 5 in the CUVS

Nehemiah 5 in the DBT

Nehemiah 5 in the DGDNT

Nehemiah 5 in the DHNT

Nehemiah 5 in the DNT

Nehemiah 5 in the ELBE

Nehemiah 5 in the EMTV

Nehemiah 5 in the ESV

Nehemiah 5 in the FBV

Nehemiah 5 in the FEB

Nehemiah 5 in the GGMNT

Nehemiah 5 in the GNT

Nehemiah 5 in the HARY

Nehemiah 5 in the HNT

Nehemiah 5 in the IRVA

Nehemiah 5 in the IRVB

Nehemiah 5 in the IRVG

Nehemiah 5 in the IRVH

Nehemiah 5 in the IRVK

Nehemiah 5 in the IRVM

Nehemiah 5 in the IRVM2

Nehemiah 5 in the IRVO

Nehemiah 5 in the IRVP

Nehemiah 5 in the IRVT

Nehemiah 5 in the IRVT2

Nehemiah 5 in the IRVU

Nehemiah 5 in the ISVN

Nehemiah 5 in the JSNT

Nehemiah 5 in the KAPI

Nehemiah 5 in the KBT1ETNIK

Nehemiah 5 in the KBV

Nehemiah 5 in the KJV

Nehemiah 5 in the KNFD

Nehemiah 5 in the LBA

Nehemiah 5 in the LBLA

Nehemiah 5 in the LNT

Nehemiah 5 in the LSV

Nehemiah 5 in the MAAL

Nehemiah 5 in the MBV

Nehemiah 5 in the MBV2

Nehemiah 5 in the MHNT

Nehemiah 5 in the MKNFD

Nehemiah 5 in the MNG

Nehemiah 5 in the MNT

Nehemiah 5 in the MNT2

Nehemiah 5 in the MRS1T

Nehemiah 5 in the NAA

Nehemiah 5 in the NASB

Nehemiah 5 in the NBLA

Nehemiah 5 in the NBS

Nehemiah 5 in the NBVTP

Nehemiah 5 in the NET2

Nehemiah 5 in the NIV11

Nehemiah 5 in the NNT

Nehemiah 5 in the NNT2

Nehemiah 5 in the NNT3

Nehemiah 5 in the PDDPT

Nehemiah 5 in the PFNT

Nehemiah 5 in the RMNT

Nehemiah 5 in the SBIAS

Nehemiah 5 in the SBIBS

Nehemiah 5 in the SBIBS2

Nehemiah 5 in the SBICS

Nehemiah 5 in the SBIDS

Nehemiah 5 in the SBIGS

Nehemiah 5 in the SBIHS

Nehemiah 5 in the SBIIS

Nehemiah 5 in the SBIIS2

Nehemiah 5 in the SBIIS3

Nehemiah 5 in the SBIKS

Nehemiah 5 in the SBIKS2

Nehemiah 5 in the SBIMS

Nehemiah 5 in the SBIOS

Nehemiah 5 in the SBIPS

Nehemiah 5 in the SBISS

Nehemiah 5 in the SBITS

Nehemiah 5 in the SBITS2

Nehemiah 5 in the SBITS3

Nehemiah 5 in the SBITS4

Nehemiah 5 in the SBIUS

Nehemiah 5 in the SBIVS

Nehemiah 5 in the SBT

Nehemiah 5 in the SBT1E

Nehemiah 5 in the SCHL

Nehemiah 5 in the SNT

Nehemiah 5 in the SUSU

Nehemiah 5 in the SUSU2

Nehemiah 5 in the SYNO

Nehemiah 5 in the TBIAOTANT

Nehemiah 5 in the TBT1E

Nehemiah 5 in the TBT1E2

Nehemiah 5 in the TFTIP

Nehemiah 5 in the TFTU

Nehemiah 5 in the TGNTATF3T

Nehemiah 5 in the THAI

Nehemiah 5 in the TNFD

Nehemiah 5 in the TNT

Nehemiah 5 in the TNTIK

Nehemiah 5 in the TNTIL

Nehemiah 5 in the TNTIN

Nehemiah 5 in the TNTIP

Nehemiah 5 in the TNTIZ

Nehemiah 5 in the TOMA

Nehemiah 5 in the TTENT

Nehemiah 5 in the UBG

Nehemiah 5 in the UGV

Nehemiah 5 in the UGV2

Nehemiah 5 in the UGV3

Nehemiah 5 in the VBL

Nehemiah 5 in the VDCC

Nehemiah 5 in the YALU

Nehemiah 5 in the YAPE

Nehemiah 5 in the YBVTP

Nehemiah 5 in the ZBP