Numbers 10 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Sula malipenga awiri a siliva, ndipo uziwagwiritsa ntchito posonkhanitsa anthu pamodzi ndiponso powasamutsa mʼmisasa. 3 Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano. 4 Akaliza limodzi lokha, atsogoleri, akulu a mafuko a Aisraeli, asonkhane kwa iwe. 5 Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka. 6 Akaliza lipenga lochenjeza lachiwiri, misasa yakummwera iyambe kusamuka. Kuliza kwa lipenga lochenjeza kudzakhala chizindikiro choyamba ulendo. 7 Pofuna kusonkhanitsa anthu, muziliza malipenga, koma mosiyana ndi mmene malipenga ochenjeza amalizidwira. 8 “Ana a Aaroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipengawo. Zimenezi zikhale zokhazikika kwa inu ndi ku mibado yanu yonse. 9 Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu. 10 Komanso pa nthawi yanu ya chisangalalo, pa maphwando anu oyikika ndi maphwando a mwezi watsopano, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu za chiyanjano, ndipo zidzakhala chikumbutso chanu pamaso pa Mulungu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” 11 Pa chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la 20, mtambo unachoka pamwamba pa chihema cha umboni. 12 Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani. 13 Kameneka kanali koyamba kuti Aisraeli anyamuke monga momwe Yehova analamulira Mose. 14 Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu. 15 Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanieli mwana wa Zuwara, 16 Eliabu mwana wa Heloni ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Zebuloni. 17 Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka. 18 Kenaka magulu a msasa wa fuko la Rubeni ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Elizuri mwana wa Sedeuri. 19 Mtsogoleri wa fuko la Simeoni anali Selumieli mwana wa Zurisadai, 20 ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi. 21 Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike. 22 Magulu a msasa wa Aefereimu anatsatira potsatira mbendera yawo. Elisama mwana wa Amihudi ndiye anali mtsogoleri wawo. 23 Gamalieli mwana wa Pedazuri ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Manase. 24 Abidani mwana wa Gideoni ndiye anali mtsogoleri wa mtundu wa Benjamini. 25 Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai. 26 Pagieli mwana wa Okirani ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Aseri, 27 ndipo mtsogoleri wa mtundu wa Nafutali anali Ahira mwana wa Enani. 28 Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu. 29 Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.” 30 Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.” 31 Ndipo Mose anati, “Pepa usatisiye popeza ukudziwa kumene tingamange misasa mʼchipululu muno ndipo udzakhala maso athu. 32 Iweyo ukapita nafe, tidzagawana nawe zinthu zabwino zomwe Yehova adzatipatsa.” 33 Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo. 34 Mtambo wa Yehova unkawaphimba masana pamene ankasamuka pa misasa yawo. 35 Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti,“Dzukani, Inu Yehova!Adani anu abalalike;Odana nanu athawe pamaso panu. 36 “Pamene likupumula, ankanena kuti,“Bwererani, Inu Yehova,ku chinamtindi cha Aisraeli.”

In Other Versions

Numbers 10 in the ANGEFD

Numbers 10 in the ANTPNG2D

Numbers 10 in the AS21

Numbers 10 in the BAGH

Numbers 10 in the BBPNG

Numbers 10 in the BBT1E

Numbers 10 in the BDS

Numbers 10 in the BEV

Numbers 10 in the BHAD

Numbers 10 in the BIB

Numbers 10 in the BLPT

Numbers 10 in the BNT

Numbers 10 in the BNTABOOT

Numbers 10 in the BNTLV

Numbers 10 in the BOATCB

Numbers 10 in the BOATCB2

Numbers 10 in the BOBCV

Numbers 10 in the BOCNT

Numbers 10 in the BOECS

Numbers 10 in the BOHCB

Numbers 10 in the BOHCV

Numbers 10 in the BOHLNT

Numbers 10 in the BOHNTLTAL

Numbers 10 in the BOICB

Numbers 10 in the BOILNTAP

Numbers 10 in the BOITCV

Numbers 10 in the BOKCV

Numbers 10 in the BOKCV2

Numbers 10 in the BOKHWOG

Numbers 10 in the BOKSSV

Numbers 10 in the BOLCB

Numbers 10 in the BOLCB2

Numbers 10 in the BOMCV

Numbers 10 in the BONAV

Numbers 10 in the BONCB

Numbers 10 in the BONLT

Numbers 10 in the BONUT2

Numbers 10 in the BOPLNT

Numbers 10 in the BOSCB

Numbers 10 in the BOSNC

Numbers 10 in the BOTLNT

Numbers 10 in the BOVCB

Numbers 10 in the BOYCB

Numbers 10 in the BPBB

Numbers 10 in the BPH

Numbers 10 in the BSB

Numbers 10 in the CCB

Numbers 10 in the CUV

Numbers 10 in the CUVS

Numbers 10 in the DBT

Numbers 10 in the DGDNT

Numbers 10 in the DHNT

Numbers 10 in the DNT

Numbers 10 in the ELBE

Numbers 10 in the EMTV

Numbers 10 in the ESV

Numbers 10 in the FBV

Numbers 10 in the FEB

Numbers 10 in the GGMNT

Numbers 10 in the GNT

Numbers 10 in the HARY

Numbers 10 in the HNT

Numbers 10 in the IRVA

Numbers 10 in the IRVB

Numbers 10 in the IRVG

Numbers 10 in the IRVH

Numbers 10 in the IRVK

Numbers 10 in the IRVM

Numbers 10 in the IRVM2

Numbers 10 in the IRVO

Numbers 10 in the IRVP

Numbers 10 in the IRVT

Numbers 10 in the IRVT2

Numbers 10 in the IRVU

Numbers 10 in the ISVN

Numbers 10 in the JSNT

Numbers 10 in the KAPI

Numbers 10 in the KBT1ETNIK

Numbers 10 in the KBV

Numbers 10 in the KJV

Numbers 10 in the KNFD

Numbers 10 in the LBA

Numbers 10 in the LBLA

Numbers 10 in the LNT

Numbers 10 in the LSV

Numbers 10 in the MAAL

Numbers 10 in the MBV

Numbers 10 in the MBV2

Numbers 10 in the MHNT

Numbers 10 in the MKNFD

Numbers 10 in the MNG

Numbers 10 in the MNT

Numbers 10 in the MNT2

Numbers 10 in the MRS1T

Numbers 10 in the NAA

Numbers 10 in the NASB

Numbers 10 in the NBLA

Numbers 10 in the NBS

Numbers 10 in the NBVTP

Numbers 10 in the NET2

Numbers 10 in the NIV11

Numbers 10 in the NNT

Numbers 10 in the NNT2

Numbers 10 in the NNT3

Numbers 10 in the PDDPT

Numbers 10 in the PFNT

Numbers 10 in the RMNT

Numbers 10 in the SBIAS

Numbers 10 in the SBIBS

Numbers 10 in the SBIBS2

Numbers 10 in the SBICS

Numbers 10 in the SBIDS

Numbers 10 in the SBIGS

Numbers 10 in the SBIHS

Numbers 10 in the SBIIS

Numbers 10 in the SBIIS2

Numbers 10 in the SBIIS3

Numbers 10 in the SBIKS

Numbers 10 in the SBIKS2

Numbers 10 in the SBIMS

Numbers 10 in the SBIOS

Numbers 10 in the SBIPS

Numbers 10 in the SBISS

Numbers 10 in the SBITS

Numbers 10 in the SBITS2

Numbers 10 in the SBITS3

Numbers 10 in the SBITS4

Numbers 10 in the SBIUS

Numbers 10 in the SBIVS

Numbers 10 in the SBT

Numbers 10 in the SBT1E

Numbers 10 in the SCHL

Numbers 10 in the SNT

Numbers 10 in the SUSU

Numbers 10 in the SUSU2

Numbers 10 in the SYNO

Numbers 10 in the TBIAOTANT

Numbers 10 in the TBT1E

Numbers 10 in the TBT1E2

Numbers 10 in the TFTIP

Numbers 10 in the TFTU

Numbers 10 in the TGNTATF3T

Numbers 10 in the THAI

Numbers 10 in the TNFD

Numbers 10 in the TNT

Numbers 10 in the TNTIK

Numbers 10 in the TNTIL

Numbers 10 in the TNTIN

Numbers 10 in the TNTIP

Numbers 10 in the TNTIZ

Numbers 10 in the TOMA

Numbers 10 in the TTENT

Numbers 10 in the UBG

Numbers 10 in the UGV

Numbers 10 in the UGV2

Numbers 10 in the UGV3

Numbers 10 in the VBL

Numbers 10 in the VDCC

Numbers 10 in the YALU

Numbers 10 in the YAPE

Numbers 10 in the YBVTP

Numbers 10 in the ZBP