Numbers 13 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.” 3 Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli. 4 Mayina awo ndi awa: kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri; 5 kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori; 6 kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune; 7 kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe; 8 kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni; 9 kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu; 10 kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi; 11 kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi; 12 kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali; 13 kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli; 14 kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi; 15 kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki. 16 Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa). 17 Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri. 18 Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri. 19 Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga? 20 Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa). 21 Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati. 22 Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto). 23 Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu. 24 Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko. 25 Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija. 26 Ndipo atabwerako anapita kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa Aisraeli onse ku Kadesi mʼchipululu cha Parani. Kumeneko anafotokozera anthu onse nawaonetsanso zipatso za mʼdzikolo. 27 Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi. 28 Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko. 29 Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.” 30 Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.” 31 Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.” 32 Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali. 33 Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.”

In Other Versions

Numbers 13 in the ANGEFD

Numbers 13 in the ANTPNG2D

Numbers 13 in the AS21

Numbers 13 in the BAGH

Numbers 13 in the BBPNG

Numbers 13 in the BBT1E

Numbers 13 in the BDS

Numbers 13 in the BEV

Numbers 13 in the BHAD

Numbers 13 in the BIB

Numbers 13 in the BLPT

Numbers 13 in the BNT

Numbers 13 in the BNTABOOT

Numbers 13 in the BNTLV

Numbers 13 in the BOATCB

Numbers 13 in the BOATCB2

Numbers 13 in the BOBCV

Numbers 13 in the BOCNT

Numbers 13 in the BOECS

Numbers 13 in the BOHCB

Numbers 13 in the BOHCV

Numbers 13 in the BOHLNT

Numbers 13 in the BOHNTLTAL

Numbers 13 in the BOICB

Numbers 13 in the BOILNTAP

Numbers 13 in the BOITCV

Numbers 13 in the BOKCV

Numbers 13 in the BOKCV2

Numbers 13 in the BOKHWOG

Numbers 13 in the BOKSSV

Numbers 13 in the BOLCB

Numbers 13 in the BOLCB2

Numbers 13 in the BOMCV

Numbers 13 in the BONAV

Numbers 13 in the BONCB

Numbers 13 in the BONLT

Numbers 13 in the BONUT2

Numbers 13 in the BOPLNT

Numbers 13 in the BOSCB

Numbers 13 in the BOSNC

Numbers 13 in the BOTLNT

Numbers 13 in the BOVCB

Numbers 13 in the BOYCB

Numbers 13 in the BPBB

Numbers 13 in the BPH

Numbers 13 in the BSB

Numbers 13 in the CCB

Numbers 13 in the CUV

Numbers 13 in the CUVS

Numbers 13 in the DBT

Numbers 13 in the DGDNT

Numbers 13 in the DHNT

Numbers 13 in the DNT

Numbers 13 in the ELBE

Numbers 13 in the EMTV

Numbers 13 in the ESV

Numbers 13 in the FBV

Numbers 13 in the FEB

Numbers 13 in the GGMNT

Numbers 13 in the GNT

Numbers 13 in the HARY

Numbers 13 in the HNT

Numbers 13 in the IRVA

Numbers 13 in the IRVB

Numbers 13 in the IRVG

Numbers 13 in the IRVH

Numbers 13 in the IRVK

Numbers 13 in the IRVM

Numbers 13 in the IRVM2

Numbers 13 in the IRVO

Numbers 13 in the IRVP

Numbers 13 in the IRVT

Numbers 13 in the IRVT2

Numbers 13 in the IRVU

Numbers 13 in the ISVN

Numbers 13 in the JSNT

Numbers 13 in the KAPI

Numbers 13 in the KBT1ETNIK

Numbers 13 in the KBV

Numbers 13 in the KJV

Numbers 13 in the KNFD

Numbers 13 in the LBA

Numbers 13 in the LBLA

Numbers 13 in the LNT

Numbers 13 in the LSV

Numbers 13 in the MAAL

Numbers 13 in the MBV

Numbers 13 in the MBV2

Numbers 13 in the MHNT

Numbers 13 in the MKNFD

Numbers 13 in the MNG

Numbers 13 in the MNT

Numbers 13 in the MNT2

Numbers 13 in the MRS1T

Numbers 13 in the NAA

Numbers 13 in the NASB

Numbers 13 in the NBLA

Numbers 13 in the NBS

Numbers 13 in the NBVTP

Numbers 13 in the NET2

Numbers 13 in the NIV11

Numbers 13 in the NNT

Numbers 13 in the NNT2

Numbers 13 in the NNT3

Numbers 13 in the PDDPT

Numbers 13 in the PFNT

Numbers 13 in the RMNT

Numbers 13 in the SBIAS

Numbers 13 in the SBIBS

Numbers 13 in the SBIBS2

Numbers 13 in the SBICS

Numbers 13 in the SBIDS

Numbers 13 in the SBIGS

Numbers 13 in the SBIHS

Numbers 13 in the SBIIS

Numbers 13 in the SBIIS2

Numbers 13 in the SBIIS3

Numbers 13 in the SBIKS

Numbers 13 in the SBIKS2

Numbers 13 in the SBIMS

Numbers 13 in the SBIOS

Numbers 13 in the SBIPS

Numbers 13 in the SBISS

Numbers 13 in the SBITS

Numbers 13 in the SBITS2

Numbers 13 in the SBITS3

Numbers 13 in the SBITS4

Numbers 13 in the SBIUS

Numbers 13 in the SBIVS

Numbers 13 in the SBT

Numbers 13 in the SBT1E

Numbers 13 in the SCHL

Numbers 13 in the SNT

Numbers 13 in the SUSU

Numbers 13 in the SUSU2

Numbers 13 in the SYNO

Numbers 13 in the TBIAOTANT

Numbers 13 in the TBT1E

Numbers 13 in the TBT1E2

Numbers 13 in the TFTIP

Numbers 13 in the TFTU

Numbers 13 in the TGNTATF3T

Numbers 13 in the THAI

Numbers 13 in the TNFD

Numbers 13 in the TNT

Numbers 13 in the TNTIK

Numbers 13 in the TNTIL

Numbers 13 in the TNTIN

Numbers 13 in the TNTIP

Numbers 13 in the TNTIZ

Numbers 13 in the TOMA

Numbers 13 in the TTENT

Numbers 13 in the UBG

Numbers 13 in the UGV

Numbers 13 in the UGV2

Numbers 13 in the UGV3

Numbers 13 in the VBL

Numbers 13 in the VDCC

Numbers 13 in the YALU

Numbers 13 in the YAPE

Numbers 13 in the YBVTP

Numbers 13 in the ZBP