Numbers 33 (BOGWICC)
1 Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni. 2 Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa: 3 Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona, 4 pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo. 5 Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti. 6 Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu. 7 Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli. 8 Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara. 9 Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko. 10 Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira. 11 Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini. 12 Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika. 13 Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi. 14 Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa. 15 Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai 16 Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava. 17 Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti. 18 Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima. 19 Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi. 20 Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina. 21 Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa. 22 Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata. 23 Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi. 24 Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada. 25 Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti. 26 Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati. 27 Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera. 28 Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika. 29 Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona. 30 Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti. 31 Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani. 32 Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi. 33 Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata. 34 Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona. 35 Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi. 36 Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi. 37 Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu. 38 Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto. 39 Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123. 40 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera. 41 Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni. 42 Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni. 43 Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti. 44 Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu. 45 Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi. 46 Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu. 47 Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo. 48 Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. 49 Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu. 50 Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, 51 “Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani, 52 mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo. 53 Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo. 54 Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu. 55 “ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo. 56 Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’ ”