Proverbs 11 (BOGWICC)

1 Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa,koma amakondwera ndi muyeso woyenera. 2 Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi,koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru. 3 Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera,koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo. 4 Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu,koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa. 5 Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo,koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo. 6 Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa,koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe. 7 Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso.Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka. 8 Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa. 9 Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake,koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu. 10 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera,ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe. 11 Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima,koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa. 12 Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru,koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete. 13 Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi;koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake. 14 Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa;koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso. 15 Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto,koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere. 16 Mkazi wodekha amalandira ulemu,koma amuna ankhanza amangopata chuma. 17 Munthu wachifundo amadzipindulira zabwinokoma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto. 18 Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu,koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni. 19 Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo,koma wothamangira zoyipa adzafa. 20 Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhotakoma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro. 21 Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa,koma anthu olungama adzapulumuka. 22 Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba,ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa. 23 Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha,koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu. 24 Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe;wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe. 25 Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera;iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa. 26 Anthu amatemberera womana anzake chakudya,koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho. 27 Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo,koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza. 28 Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota,koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira. 29 Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto,ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru. 30 Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo,ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo. 31 Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi,kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!

In Other Versions

Proverbs 11 in the ANGEFD

Proverbs 11 in the ANTPNG2D

Proverbs 11 in the AS21

Proverbs 11 in the BAGH

Proverbs 11 in the BBPNG

Proverbs 11 in the BBT1E

Proverbs 11 in the BDS

Proverbs 11 in the BEV

Proverbs 11 in the BHAD

Proverbs 11 in the BIB

Proverbs 11 in the BLPT

Proverbs 11 in the BNT

Proverbs 11 in the BNTABOOT

Proverbs 11 in the BNTLV

Proverbs 11 in the BOATCB

Proverbs 11 in the BOATCB2

Proverbs 11 in the BOBCV

Proverbs 11 in the BOCNT

Proverbs 11 in the BOECS

Proverbs 11 in the BOHCB

Proverbs 11 in the BOHCV

Proverbs 11 in the BOHLNT

Proverbs 11 in the BOHNTLTAL

Proverbs 11 in the BOICB

Proverbs 11 in the BOILNTAP

Proverbs 11 in the BOITCV

Proverbs 11 in the BOKCV

Proverbs 11 in the BOKCV2

Proverbs 11 in the BOKHWOG

Proverbs 11 in the BOKSSV

Proverbs 11 in the BOLCB

Proverbs 11 in the BOLCB2

Proverbs 11 in the BOMCV

Proverbs 11 in the BONAV

Proverbs 11 in the BONCB

Proverbs 11 in the BONLT

Proverbs 11 in the BONUT2

Proverbs 11 in the BOPLNT

Proverbs 11 in the BOSCB

Proverbs 11 in the BOSNC

Proverbs 11 in the BOTLNT

Proverbs 11 in the BOVCB

Proverbs 11 in the BOYCB

Proverbs 11 in the BPBB

Proverbs 11 in the BPH

Proverbs 11 in the BSB

Proverbs 11 in the CCB

Proverbs 11 in the CUV

Proverbs 11 in the CUVS

Proverbs 11 in the DBT

Proverbs 11 in the DGDNT

Proverbs 11 in the DHNT

Proverbs 11 in the DNT

Proverbs 11 in the ELBE

Proverbs 11 in the EMTV

Proverbs 11 in the ESV

Proverbs 11 in the FBV

Proverbs 11 in the FEB

Proverbs 11 in the GGMNT

Proverbs 11 in the GNT

Proverbs 11 in the HARY

Proverbs 11 in the HNT

Proverbs 11 in the IRVA

Proverbs 11 in the IRVB

Proverbs 11 in the IRVG

Proverbs 11 in the IRVH

Proverbs 11 in the IRVK

Proverbs 11 in the IRVM

Proverbs 11 in the IRVM2

Proverbs 11 in the IRVO

Proverbs 11 in the IRVP

Proverbs 11 in the IRVT

Proverbs 11 in the IRVT2

Proverbs 11 in the IRVU

Proverbs 11 in the ISVN

Proverbs 11 in the JSNT

Proverbs 11 in the KAPI

Proverbs 11 in the KBT1ETNIK

Proverbs 11 in the KBV

Proverbs 11 in the KJV

Proverbs 11 in the KNFD

Proverbs 11 in the LBA

Proverbs 11 in the LBLA

Proverbs 11 in the LNT

Proverbs 11 in the LSV

Proverbs 11 in the MAAL

Proverbs 11 in the MBV

Proverbs 11 in the MBV2

Proverbs 11 in the MHNT

Proverbs 11 in the MKNFD

Proverbs 11 in the MNG

Proverbs 11 in the MNT

Proverbs 11 in the MNT2

Proverbs 11 in the MRS1T

Proverbs 11 in the NAA

Proverbs 11 in the NASB

Proverbs 11 in the NBLA

Proverbs 11 in the NBS

Proverbs 11 in the NBVTP

Proverbs 11 in the NET2

Proverbs 11 in the NIV11

Proverbs 11 in the NNT

Proverbs 11 in the NNT2

Proverbs 11 in the NNT3

Proverbs 11 in the PDDPT

Proverbs 11 in the PFNT

Proverbs 11 in the RMNT

Proverbs 11 in the SBIAS

Proverbs 11 in the SBIBS

Proverbs 11 in the SBIBS2

Proverbs 11 in the SBICS

Proverbs 11 in the SBIDS

Proverbs 11 in the SBIGS

Proverbs 11 in the SBIHS

Proverbs 11 in the SBIIS

Proverbs 11 in the SBIIS2

Proverbs 11 in the SBIIS3

Proverbs 11 in the SBIKS

Proverbs 11 in the SBIKS2

Proverbs 11 in the SBIMS

Proverbs 11 in the SBIOS

Proverbs 11 in the SBIPS

Proverbs 11 in the SBISS

Proverbs 11 in the SBITS

Proverbs 11 in the SBITS2

Proverbs 11 in the SBITS3

Proverbs 11 in the SBITS4

Proverbs 11 in the SBIUS

Proverbs 11 in the SBIVS

Proverbs 11 in the SBT

Proverbs 11 in the SBT1E

Proverbs 11 in the SCHL

Proverbs 11 in the SNT

Proverbs 11 in the SUSU

Proverbs 11 in the SUSU2

Proverbs 11 in the SYNO

Proverbs 11 in the TBIAOTANT

Proverbs 11 in the TBT1E

Proverbs 11 in the TBT1E2

Proverbs 11 in the TFTIP

Proverbs 11 in the TFTU

Proverbs 11 in the TGNTATF3T

Proverbs 11 in the THAI

Proverbs 11 in the TNFD

Proverbs 11 in the TNT

Proverbs 11 in the TNTIK

Proverbs 11 in the TNTIL

Proverbs 11 in the TNTIN

Proverbs 11 in the TNTIP

Proverbs 11 in the TNTIZ

Proverbs 11 in the TOMA

Proverbs 11 in the TTENT

Proverbs 11 in the UBG

Proverbs 11 in the UGV

Proverbs 11 in the UGV2

Proverbs 11 in the UGV3

Proverbs 11 in the VBL

Proverbs 11 in the VDCC

Proverbs 11 in the YALU

Proverbs 11 in the YAPE

Proverbs 11 in the YBVTP

Proverbs 11 in the ZBP