Proverbs 6 (BOGWICC)

1 Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole,ngati walonjeza kumulipirira mlendo, 2 ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena,wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako. 3 Tsono popeza iwe mwana wangawadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse:pita msanga ukamupemphe mnansi wako;kuti akumasule! 4 Usagone tulo,usawodzere. 5 Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje,ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka. 6 Pita kwa nyerere, mlesi iwe;kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu! 7 Zilibe mfumu,zilibe woyangʼanira kapena wolamulira, 8 komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwendipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola. 9 Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe?Kodi tulo tako tidzatha liti? 10 Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼonondingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule, 11 umphawi udzakugwira ngati mbalandipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba. 12 Munthu wachabechabe, munthu woyipa,amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa, 13 amatsinzinira maso ake,namakwakwaza mapazi akendi kulozaloza ndi zala zake, 14 amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengondipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu. 15 Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa;adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa. 16 Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo,zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa: 17 maso onyada,pakamwa pabodza,manja akupha munthu wosalakwa, 18 mtima wokonzekera kuchita zoyipa,mapazi othamangira msanga ku zoyipa, 19 mboni yonama yoyankhula mabodzakomanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale. 20 Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako. 21 Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse,uzimangirire mʼkhosi mwako. 22 Ukamayenda, zidzakulozera njira;ukugona, zidzakulondera;ukudzuka, zidzakuyankhula. 23 Paja malamulo awa ali ngati nyale,malangizowa ali ngati kuwunika,ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwomoyo weniweni, 24 kukupulumutsa kwa mkazi wadama,zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere. 25 Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake,asakukope ndi zikope zake, 26 paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledindipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse. 27 Kodi munthu angathe kutenga motozovala zake osapsa? 28 Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amotomapazi ake osapserera? 29 Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina.Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa. 30 Paja anthu sayinyoza mbala ikabachifukwa chakuti ili ndi njala. 31 Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri,ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake. 32 Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru.Wochita zimenezi amangodziwononga yekha. 33 Adzalandira mabala ndi mʼnyozo,ndipo manyazi ake sadzamuchokera. 34 Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa,ndipo sadzachita chifundo pobwezera. 35 Iye savomera dipo lililonse;sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani.

In Other Versions

Proverbs 6 in the ANGEFD

Proverbs 6 in the ANTPNG2D

Proverbs 6 in the AS21

Proverbs 6 in the BAGH

Proverbs 6 in the BBPNG

Proverbs 6 in the BBT1E

Proverbs 6 in the BDS

Proverbs 6 in the BEV

Proverbs 6 in the BHAD

Proverbs 6 in the BIB

Proverbs 6 in the BLPT

Proverbs 6 in the BNT

Proverbs 6 in the BNTABOOT

Proverbs 6 in the BNTLV

Proverbs 6 in the BOATCB

Proverbs 6 in the BOATCB2

Proverbs 6 in the BOBCV

Proverbs 6 in the BOCNT

Proverbs 6 in the BOECS

Proverbs 6 in the BOHCB

Proverbs 6 in the BOHCV

Proverbs 6 in the BOHLNT

Proverbs 6 in the BOHNTLTAL

Proverbs 6 in the BOICB

Proverbs 6 in the BOILNTAP

Proverbs 6 in the BOITCV

Proverbs 6 in the BOKCV

Proverbs 6 in the BOKCV2

Proverbs 6 in the BOKHWOG

Proverbs 6 in the BOKSSV

Proverbs 6 in the BOLCB

Proverbs 6 in the BOLCB2

Proverbs 6 in the BOMCV

Proverbs 6 in the BONAV

Proverbs 6 in the BONCB

Proverbs 6 in the BONLT

Proverbs 6 in the BONUT2

Proverbs 6 in the BOPLNT

Proverbs 6 in the BOSCB

Proverbs 6 in the BOSNC

Proverbs 6 in the BOTLNT

Proverbs 6 in the BOVCB

Proverbs 6 in the BOYCB

Proverbs 6 in the BPBB

Proverbs 6 in the BPH

Proverbs 6 in the BSB

Proverbs 6 in the CCB

Proverbs 6 in the CUV

Proverbs 6 in the CUVS

Proverbs 6 in the DBT

Proverbs 6 in the DGDNT

Proverbs 6 in the DHNT

Proverbs 6 in the DNT

Proverbs 6 in the ELBE

Proverbs 6 in the EMTV

Proverbs 6 in the ESV

Proverbs 6 in the FBV

Proverbs 6 in the FEB

Proverbs 6 in the GGMNT

Proverbs 6 in the GNT

Proverbs 6 in the HARY

Proverbs 6 in the HNT

Proverbs 6 in the IRVA

Proverbs 6 in the IRVB

Proverbs 6 in the IRVG

Proverbs 6 in the IRVH

Proverbs 6 in the IRVK

Proverbs 6 in the IRVM

Proverbs 6 in the IRVM2

Proverbs 6 in the IRVO

Proverbs 6 in the IRVP

Proverbs 6 in the IRVT

Proverbs 6 in the IRVT2

Proverbs 6 in the IRVU

Proverbs 6 in the ISVN

Proverbs 6 in the JSNT

Proverbs 6 in the KAPI

Proverbs 6 in the KBT1ETNIK

Proverbs 6 in the KBV

Proverbs 6 in the KJV

Proverbs 6 in the KNFD

Proverbs 6 in the LBA

Proverbs 6 in the LBLA

Proverbs 6 in the LNT

Proverbs 6 in the LSV

Proverbs 6 in the MAAL

Proverbs 6 in the MBV

Proverbs 6 in the MBV2

Proverbs 6 in the MHNT

Proverbs 6 in the MKNFD

Proverbs 6 in the MNG

Proverbs 6 in the MNT

Proverbs 6 in the MNT2

Proverbs 6 in the MRS1T

Proverbs 6 in the NAA

Proverbs 6 in the NASB

Proverbs 6 in the NBLA

Proverbs 6 in the NBS

Proverbs 6 in the NBVTP

Proverbs 6 in the NET2

Proverbs 6 in the NIV11

Proverbs 6 in the NNT

Proverbs 6 in the NNT2

Proverbs 6 in the NNT3

Proverbs 6 in the PDDPT

Proverbs 6 in the PFNT

Proverbs 6 in the RMNT

Proverbs 6 in the SBIAS

Proverbs 6 in the SBIBS

Proverbs 6 in the SBIBS2

Proverbs 6 in the SBICS

Proverbs 6 in the SBIDS

Proverbs 6 in the SBIGS

Proverbs 6 in the SBIHS

Proverbs 6 in the SBIIS

Proverbs 6 in the SBIIS2

Proverbs 6 in the SBIIS3

Proverbs 6 in the SBIKS

Proverbs 6 in the SBIKS2

Proverbs 6 in the SBIMS

Proverbs 6 in the SBIOS

Proverbs 6 in the SBIPS

Proverbs 6 in the SBISS

Proverbs 6 in the SBITS

Proverbs 6 in the SBITS2

Proverbs 6 in the SBITS3

Proverbs 6 in the SBITS4

Proverbs 6 in the SBIUS

Proverbs 6 in the SBIVS

Proverbs 6 in the SBT

Proverbs 6 in the SBT1E

Proverbs 6 in the SCHL

Proverbs 6 in the SNT

Proverbs 6 in the SUSU

Proverbs 6 in the SUSU2

Proverbs 6 in the SYNO

Proverbs 6 in the TBIAOTANT

Proverbs 6 in the TBT1E

Proverbs 6 in the TBT1E2

Proverbs 6 in the TFTIP

Proverbs 6 in the TFTU

Proverbs 6 in the TGNTATF3T

Proverbs 6 in the THAI

Proverbs 6 in the TNFD

Proverbs 6 in the TNT

Proverbs 6 in the TNTIK

Proverbs 6 in the TNTIL

Proverbs 6 in the TNTIN

Proverbs 6 in the TNTIP

Proverbs 6 in the TNTIZ

Proverbs 6 in the TOMA

Proverbs 6 in the TTENT

Proverbs 6 in the UBG

Proverbs 6 in the UGV

Proverbs 6 in the UGV2

Proverbs 6 in the UGV3

Proverbs 6 in the VBL

Proverbs 6 in the VDCC

Proverbs 6 in the YALU

Proverbs 6 in the YAPE

Proverbs 6 in the YBVTP

Proverbs 6 in the ZBP