Psalms 1 (BOGWICC)
1 Wodala munthuamene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza. 2 Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehovandipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku. 3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,umene umabereka zipatso zake pa nyengo yakendipo masamba ake safota.Chilichonse chimene amachita amapindula nacho. 4 Sizitero ndi anthu oyipa!Iwo ali ngati munguumene umawuluzidwa ndi mphepo. 5 Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama. 6 Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.