Psalms 110 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,“Khala ku dzanja langa lamanjampaka nditasandutsa adani akokukhala chopondapo mapazi ako.” 2 Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;udzalamulira pakati pa adani ako. 3 Ankhondo ako adzakhala odziperekapa tsiku lako la nkhondo.Atavala chiyero chaulemerero,kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,udzalandira mame a unyamata wako. 4 Yehova walumbirandipo sadzasintha maganizo ake:“Ndiwe wansembe mpaka muyayamonga mwa unsembe wa Melikizedeki.” 5 Ambuye ali kudzanja lako lamanja;Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake. 6 Adzaweruza anthu a mitundu ina,adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi. 7 Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira;choncho adzaweramutsa mutu wake.