Psalms 123 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Ndikweza maso anga kwa Inu,kwa Inu amene mumakhala kumwamba. 2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo,monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake,choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu,mpaka atichitire chifundo. 3 Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo,pakuti tapirira chitonzo chachikulu. 4 Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza,chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.