Psalms 124 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,anene tsono Israeli, 2 akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,potiwukira anthuwo, 3 iwo atatipsera mtima,akanatimeza amoyo; 4 chigumula chikanatimiza,mtsinje ukanatikokolola, 5 madzi a mkokomoakanatikokolola. 6 Atamandike Yehova,amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo. 7 Moyo wathu wawonjoka ngati mbalameyokodwa mu msampha wa mlenje;msampha wathyoka,ndipo ife tapulumuka. 8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehovawolenga kumwamba ndi dziko lapansi.