Psalms 78 (BOGWICC)

undefined Ndakatulo ya Asafu. 1 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;mvetserani mawu a pakamwa panga. 2 Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale 3 zimene tinazimva ndi kuzidziwa,zimene makolo athu anatiwuza. 4 Sitidzabisira ana awo,tidzafotokozera mʼbado wotsatirantchito zotamandika za Yehova,mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita. 5 Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobondi kukhazikitsa lamulo mu Israeli,zimene analamulira makolo athukuphunzitsa ana awo, 6 kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,ngakhale ana amene sanabadwe,ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso. 7 Choncho iwo adzakhulupirira Mulungundipo sadzayiwala ntchito zakekoma adzasunga malamulo ake. 8 Iwo asadzakhale monga makolo awo,mʼbado wosamvera ndi wowukira,umene mitima yake inali yosamvera Mulungu,umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye. 9 Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta,anathawabe pa nthawi ya nkhondo; 10 iwo sanasunge pangano la Mulungundipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake. 11 Anayiwala zimene Iye anachita,zozizwitsa zimene anawaonetsa. 12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani. 13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma. 14 Anawatsogolera ndi mtambo masanandi kuwala kwa moto usiku wonse. 15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululundi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri; 16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyalandi kuyenda madzi ngati mitsinje. 17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu. 18 Ananyoza Mulungu mwadalapomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka. 19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,“Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu? 20 Iye atamenya thanthwemadzi anatuluka,ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi.Koma iye angatipatsenso ife chakudya?Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?” 21 Yehova atawamva anakwiya kwambiri;moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo,ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli, 22 pakuti iwo sanakhulupirire Mulungukapena kudalira chipulumutso chake. 23 Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwambandi kutsekula makomo a mayiko akumwamba; 24 anagwetsa mana kuti anthu adye,anawapatsa tirigu wakumwamba. 25 Anthu anadya buledi wa angelo,Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya. 26 Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba,ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake. 27 Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi,mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 28 Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo,kuzungulira matenti awo onse. 29 Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochulukapakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka. 30 Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho,chakudya chili mʼkamwa mwawobe, 31 mkwiyo wa Mulungu unawayakira;Iye anapha amphamvu onse pakati pawo,kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli. 32 Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa;ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe. 33 Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya.Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso. 34 Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo;iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu. 35 Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo,kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo. 36 Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo,kumunamiza ndi malilime awo; 37 Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye,iwo sanakhulupirike ku pangano lake. 38 Komabe Iye anali wachifundo;anakhululukira mphulupulu zawondipo sanawawononge.Nthawi ndi nthawi Iye anabweza mkwiyo wakendipo sanawutse ukali wake wonse. 39 Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe,mphepo yopita imene sibwereranso. 40 Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululundi kumumvetsa chisoni mʼdziko lopanda kanthu! 41 Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu;ankamuputa Woyera wa Israeli. 42 Sanakumbukire mphamvu zake,tsiku limene Iye anawawombola kwa ozunza, 43 tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto,zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani. 44 Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi;Iwo sanathe kumwa madzi ochokera mʼmitsinje yawo. 45 Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga,ndiponso achule amene anawasakaza. 46 Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala,zokolola zawo kwa dzombe. 47 Iye anawononga mphesa zawo ndi matalalandiponso mitengo yawo yankhuyu ndi chisanu. 48 Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala,zoweta zawo ku zingʼaningʼani. 49 Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo,anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso.Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza. 50 Analolera kukwiya,sanawapulumutse ku imfakoma anawapereka ku mliri. 51 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu 52 Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto;anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu. 53 Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe manthakoma nyanja inamiza adani awo. 54 Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera,ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera. 55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawondipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo;Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo. 56 Koma iwo anayesa Mulungundi kuwukira Wammwambamwamba;sanasunge malamulo ake. 57 Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo,anapotoka monga uta wosakhulupirika. 58 Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano;anawutsa nsanje yake ndi mafano awo. 59 Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri;Iye anakana Israeli kwathunthu. 60 Anasiya nyumba ya ku Silo,tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu. 61 Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo,ulemerero wake mʼmanja mwa adani. 62 Anapereka anthu ake ku lupanga;anakwiya kwambiri ndi cholowa chake. 63 Moto unanyeketsa anyamata awo,ndipo anamwali awo analibe nyimbo za ukwati; 64 ansembe awo anaphedwa ndi lupanga,ndipo amayi awo amasiye sanathe kulira. 65 Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo,ngati munthu wamphamvu wofuwula chifukwa cha vinyo. 66 Iye anathamangitsa adani ake;anawachititsa manyazi ku nthawi zonse. 67 Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe,sanasankhe fuko la Efereimu; 68 Koma anasankha fuko la Yuda,phiri la Ziyoni limene analikonda. 69 Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda,dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya. 70 Anasankha Davide mtumiki wakendi kumuchotsa pakati pa makola ankhosa; 71 kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsakuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo,wa Israeli cholowa chake. 72 Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama;ndi manja aluso anawatsogolera.

In Other Versions

Psalms 78 in the ANGEFD

Psalms 78 in the ANTPNG2D

Psalms 78 in the AS21

Psalms 78 in the BAGH

Psalms 78 in the BBPNG

Psalms 78 in the BBT1E

Psalms 78 in the BDS

Psalms 78 in the BEV

Psalms 78 in the BHAD

Psalms 78 in the BIB

Psalms 78 in the BLPT

Psalms 78 in the BNT

Psalms 78 in the BNTABOOT

Psalms 78 in the BNTLV

Psalms 78 in the BOATCB

Psalms 78 in the BOATCB2

Psalms 78 in the BOBCV

Psalms 78 in the BOCNT

Psalms 78 in the BOECS

Psalms 78 in the BOHCB

Psalms 78 in the BOHCV

Psalms 78 in the BOHLNT

Psalms 78 in the BOHNTLTAL

Psalms 78 in the BOICB

Psalms 78 in the BOILNTAP

Psalms 78 in the BOITCV

Psalms 78 in the BOKCV

Psalms 78 in the BOKCV2

Psalms 78 in the BOKHWOG

Psalms 78 in the BOKSSV

Psalms 78 in the BOLCB

Psalms 78 in the BOLCB2

Psalms 78 in the BOMCV

Psalms 78 in the BONAV

Psalms 78 in the BONCB

Psalms 78 in the BONLT

Psalms 78 in the BONUT2

Psalms 78 in the BOPLNT

Psalms 78 in the BOSCB

Psalms 78 in the BOSNC

Psalms 78 in the BOTLNT

Psalms 78 in the BOVCB

Psalms 78 in the BOYCB

Psalms 78 in the BPBB

Psalms 78 in the BPH

Psalms 78 in the BSB

Psalms 78 in the CCB

Psalms 78 in the CUV

Psalms 78 in the CUVS

Psalms 78 in the DBT

Psalms 78 in the DGDNT

Psalms 78 in the DHNT

Psalms 78 in the DNT

Psalms 78 in the ELBE

Psalms 78 in the EMTV

Psalms 78 in the ESV

Psalms 78 in the FBV

Psalms 78 in the FEB

Psalms 78 in the GGMNT

Psalms 78 in the GNT

Psalms 78 in the HARY

Psalms 78 in the HNT

Psalms 78 in the IRVA

Psalms 78 in the IRVB

Psalms 78 in the IRVG

Psalms 78 in the IRVH

Psalms 78 in the IRVK

Psalms 78 in the IRVM

Psalms 78 in the IRVM2

Psalms 78 in the IRVO

Psalms 78 in the IRVP

Psalms 78 in the IRVT

Psalms 78 in the IRVT2

Psalms 78 in the IRVU

Psalms 78 in the ISVN

Psalms 78 in the JSNT

Psalms 78 in the KAPI

Psalms 78 in the KBT1ETNIK

Psalms 78 in the KBV

Psalms 78 in the KJV

Psalms 78 in the KNFD

Psalms 78 in the LBA

Psalms 78 in the LBLA

Psalms 78 in the LNT

Psalms 78 in the LSV

Psalms 78 in the MAAL

Psalms 78 in the MBV

Psalms 78 in the MBV2

Psalms 78 in the MHNT

Psalms 78 in the MKNFD

Psalms 78 in the MNG

Psalms 78 in the MNT

Psalms 78 in the MNT2

Psalms 78 in the MRS1T

Psalms 78 in the NAA

Psalms 78 in the NASB

Psalms 78 in the NBLA

Psalms 78 in the NBS

Psalms 78 in the NBVTP

Psalms 78 in the NET2

Psalms 78 in the NIV11

Psalms 78 in the NNT

Psalms 78 in the NNT2

Psalms 78 in the NNT3

Psalms 78 in the PDDPT

Psalms 78 in the PFNT

Psalms 78 in the RMNT

Psalms 78 in the SBIAS

Psalms 78 in the SBIBS

Psalms 78 in the SBIBS2

Psalms 78 in the SBICS

Psalms 78 in the SBIDS

Psalms 78 in the SBIGS

Psalms 78 in the SBIHS

Psalms 78 in the SBIIS

Psalms 78 in the SBIIS2

Psalms 78 in the SBIIS3

Psalms 78 in the SBIKS

Psalms 78 in the SBIKS2

Psalms 78 in the SBIMS

Psalms 78 in the SBIOS

Psalms 78 in the SBIPS

Psalms 78 in the SBISS

Psalms 78 in the SBITS

Psalms 78 in the SBITS2

Psalms 78 in the SBITS3

Psalms 78 in the SBITS4

Psalms 78 in the SBIUS

Psalms 78 in the SBIVS

Psalms 78 in the SBT

Psalms 78 in the SBT1E

Psalms 78 in the SCHL

Psalms 78 in the SNT

Psalms 78 in the SUSU

Psalms 78 in the SUSU2

Psalms 78 in the SYNO

Psalms 78 in the TBIAOTANT

Psalms 78 in the TBT1E

Psalms 78 in the TBT1E2

Psalms 78 in the TFTIP

Psalms 78 in the TFTU

Psalms 78 in the TGNTATF3T

Psalms 78 in the THAI

Psalms 78 in the TNFD

Psalms 78 in the TNT

Psalms 78 in the TNTIK

Psalms 78 in the TNTIL

Psalms 78 in the TNTIN

Psalms 78 in the TNTIP

Psalms 78 in the TNTIZ

Psalms 78 in the TOMA

Psalms 78 in the TTENT

Psalms 78 in the UBG

Psalms 78 in the UGV

Psalms 78 in the UGV2

Psalms 78 in the UGV3

Psalms 78 in the VBL

Psalms 78 in the VDCC

Psalms 78 in the YALU

Psalms 78 in the YAPE

Psalms 78 in the YBVTP

Psalms 78 in the ZBP