Psalms 93 (BOGWICC)
1 Yehova akulamulira, wavala ulemerero;Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe. 2 Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;Inu ndinu wamuyaya. 3 Nyanja zakweza Inu Yehova,nyanja zakweza mawu ake;nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo. 4 Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,Yehova mmwamba ndi wamphamvu. 5 Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;chiyero chimakongoletsa nyumba yanumpaka muyaya.