Zechariah 14 (BOGWICC)

1 Taonani tsiku la Yehova likubwera pamene zinthu zimene adani ako anakulanda azidzagawana iwe ukuona. 2 Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu; mzindawu udzalandidwa, nyumba zidzaphwasulidwa, ndipo akazi adzagwiriridwa. Theka la anthu a mu mzindamu lidzapita ku ukapolo, koma ena onse otsala mu mzindamu sadzachotsedwa. 3 Pamenepo Yehova adzabwera kudzamenyana ndi mitundu ya anthu imeneyi, ngati mmene amachitira pa nthawi ya nkhondo. 4 Tsiku limenelo adzayimirira pa Phiri la Olivi, kummawa kwa Yerusalemu, ndipo Phiri la Olivilo lidzagawikana pawiri kuyambira kummawa mpaka kumadzulo, kupanga chigwa chachikulu, kuchititsa kuti theka la phiri lisunthire kumpoto ndi linalo kummwera. 5 Inu mudzathawa podzera mʼchigwa chapakati pa phirilo, pakuti chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa monga munachitira pa tsiku la chivomerezi nthawi ya Uziya mfumu ya Yuda. Kenaka Yehova Mulungu wanga adzabwera, pamodzi ndi oyera ake onse. 6 Tsiku limenelo sipadzakhala kuwala, kuzizira kapena chisanu. 7 Lidzakhala tsiku lapaderadera, silidzakhala usana kapena usiku; tsiku limeneli akulidziwa ndi Yehova yekha. Ikadzafika nthawi ya madzulo, kudzakhala kukuwalabe. 8 Tsiku limenelo madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu, theka lidzapita ku nyanja ya kummawa ndipo theka lina ku nyanja ya kumadzulo, nthawi yachilimwe ndi nthawi yozizira yomwe. 9 Ndipo Yehova adzakhala mfumu pa dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo padzakhala Ambuye mmodzi yekha, ndipo dzina lidzakhala limodzi lomwelo. 10 Dziko lonse, kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kummwera kwa Yerusalemu, lidzakhala ngati Araba. Koma Yerusalemu adzakwezedwa ndipo adzakhala pamalo pakepo, kuyambira ku Chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene ali ku Chipata Choyamba, ku Chipata Chapangodya, ndipo kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku malo opsinyira mphesa za mfumu. 11 Mʼmenemo mudzakhala anthu; sadzawonongedwanso. Yerusalemu adzakhala pa mtendere. 12 Mliri umene Yehova adzakanthire nawo mitundu yonse ya anthu imene inkamenyana ndi Yerusalemu ndi uwu: Matupi awo adzawola iwo eni akuyenda, maso awo adzawola ali mʼmalo mwake, ndipo malilime awo adzawola ali mʼkamwa mwawo. 13 Pa tsiku limenelo Yehova adzasokoneza anthu akuluakulu. Munthu aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndi kuyamba kumenyana okhaokha. 14 Yuda nayenso adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Chuma chonse cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi; golide, siliva ndi zovala zochuluka kwambiri. 15 Mliri womwewo udzapha akavalo ndi nyulu, ngamira ndi abulu, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku misasako. 16 Kenaka opulumuka ochokera mwa mitundu yonse ya anthu amene anathira nkhondo Yerusalemu, azidzapita chaka ndi chaka kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, ndiponso kukachita Chikondwerero cha Misasa. 17 Ngati mitundu ina ya anthu pa dziko lapansi sidzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, idzakhala wopanda mvula. 18 Ndipo ngati anthu a ku Igupto sadzapita ndi kukakhala nawo kumeneko, adzakhala wopanda mvula. Yehova adzabweretsa pa iwo mliri umene analangira mitundu ina ya anthu imene sinapite ku Chikondwerero cha Misasa. 19 Chimenechi chidzakhala chilango cha Igupto ndiponso mitundu ina yonse imene sidzapita ku Chikondwerero cha Misasa. 20 Pa tsiku limenelo pa maberu a akavalo padzalembedwa mawu oti WOPATULIKIRA YEHOVA, ndipo miphika ya mʼNyumba ya Yehova idzakhala yopatulika ngati mbale za ku guwa. 21 Mʼphika uliwonse ku Yerusalemu ndi ku Yuda udzakhala wopatulikira Yehova Wamphamvuzonse, ndipo onse amene adzabwera kudzapereka nsembe adzatenga miphika ina ndi kuphikiramo. Ndipo nthawi imeneyo simudzakhalanso Akanaani mʼNyumba ya Yehova Wamphamvuzonse.

In Other Versions

Zechariah 14 in the ANGEFD

Zechariah 14 in the ANTPNG2D

Zechariah 14 in the AS21

Zechariah 14 in the BAGH

Zechariah 14 in the BBPNG

Zechariah 14 in the BBT1E

Zechariah 14 in the BDS

Zechariah 14 in the BEV

Zechariah 14 in the BHAD

Zechariah 14 in the BIB

Zechariah 14 in the BLPT

Zechariah 14 in the BNT

Zechariah 14 in the BNTABOOT

Zechariah 14 in the BNTLV

Zechariah 14 in the BOATCB

Zechariah 14 in the BOATCB2

Zechariah 14 in the BOBCV

Zechariah 14 in the BOCNT

Zechariah 14 in the BOECS

Zechariah 14 in the BOHCB

Zechariah 14 in the BOHCV

Zechariah 14 in the BOHLNT

Zechariah 14 in the BOHNTLTAL

Zechariah 14 in the BOICB

Zechariah 14 in the BOILNTAP

Zechariah 14 in the BOITCV

Zechariah 14 in the BOKCV

Zechariah 14 in the BOKCV2

Zechariah 14 in the BOKHWOG

Zechariah 14 in the BOKSSV

Zechariah 14 in the BOLCB

Zechariah 14 in the BOLCB2

Zechariah 14 in the BOMCV

Zechariah 14 in the BONAV

Zechariah 14 in the BONCB

Zechariah 14 in the BONLT

Zechariah 14 in the BONUT2

Zechariah 14 in the BOPLNT

Zechariah 14 in the BOSCB

Zechariah 14 in the BOSNC

Zechariah 14 in the BOTLNT

Zechariah 14 in the BOVCB

Zechariah 14 in the BOYCB

Zechariah 14 in the BPBB

Zechariah 14 in the BPH

Zechariah 14 in the BSB

Zechariah 14 in the CCB

Zechariah 14 in the CUV

Zechariah 14 in the CUVS

Zechariah 14 in the DBT

Zechariah 14 in the DGDNT

Zechariah 14 in the DHNT

Zechariah 14 in the DNT

Zechariah 14 in the ELBE

Zechariah 14 in the EMTV

Zechariah 14 in the ESV

Zechariah 14 in the FBV

Zechariah 14 in the FEB

Zechariah 14 in the GGMNT

Zechariah 14 in the GNT

Zechariah 14 in the HARY

Zechariah 14 in the HNT

Zechariah 14 in the IRVA

Zechariah 14 in the IRVB

Zechariah 14 in the IRVG

Zechariah 14 in the IRVH

Zechariah 14 in the IRVK

Zechariah 14 in the IRVM

Zechariah 14 in the IRVM2

Zechariah 14 in the IRVO

Zechariah 14 in the IRVP

Zechariah 14 in the IRVT

Zechariah 14 in the IRVT2

Zechariah 14 in the IRVU

Zechariah 14 in the ISVN

Zechariah 14 in the JSNT

Zechariah 14 in the KAPI

Zechariah 14 in the KBT1ETNIK

Zechariah 14 in the KBV

Zechariah 14 in the KJV

Zechariah 14 in the KNFD

Zechariah 14 in the LBA

Zechariah 14 in the LBLA

Zechariah 14 in the LNT

Zechariah 14 in the LSV

Zechariah 14 in the MAAL

Zechariah 14 in the MBV

Zechariah 14 in the MBV2

Zechariah 14 in the MHNT

Zechariah 14 in the MKNFD

Zechariah 14 in the MNG

Zechariah 14 in the MNT

Zechariah 14 in the MNT2

Zechariah 14 in the MRS1T

Zechariah 14 in the NAA

Zechariah 14 in the NASB

Zechariah 14 in the NBLA

Zechariah 14 in the NBS

Zechariah 14 in the NBVTP

Zechariah 14 in the NET2

Zechariah 14 in the NIV11

Zechariah 14 in the NNT

Zechariah 14 in the NNT2

Zechariah 14 in the NNT3

Zechariah 14 in the PDDPT

Zechariah 14 in the PFNT

Zechariah 14 in the RMNT

Zechariah 14 in the SBIAS

Zechariah 14 in the SBIBS

Zechariah 14 in the SBIBS2

Zechariah 14 in the SBICS

Zechariah 14 in the SBIDS

Zechariah 14 in the SBIGS

Zechariah 14 in the SBIHS

Zechariah 14 in the SBIIS

Zechariah 14 in the SBIIS2

Zechariah 14 in the SBIIS3

Zechariah 14 in the SBIKS

Zechariah 14 in the SBIKS2

Zechariah 14 in the SBIMS

Zechariah 14 in the SBIOS

Zechariah 14 in the SBIPS

Zechariah 14 in the SBISS

Zechariah 14 in the SBITS

Zechariah 14 in the SBITS2

Zechariah 14 in the SBITS3

Zechariah 14 in the SBITS4

Zechariah 14 in the SBIUS

Zechariah 14 in the SBIVS

Zechariah 14 in the SBT

Zechariah 14 in the SBT1E

Zechariah 14 in the SCHL

Zechariah 14 in the SNT

Zechariah 14 in the SUSU

Zechariah 14 in the SUSU2

Zechariah 14 in the SYNO

Zechariah 14 in the TBIAOTANT

Zechariah 14 in the TBT1E

Zechariah 14 in the TBT1E2

Zechariah 14 in the TFTIP

Zechariah 14 in the TFTU

Zechariah 14 in the TGNTATF3T

Zechariah 14 in the THAI

Zechariah 14 in the TNFD

Zechariah 14 in the TNT

Zechariah 14 in the TNTIK

Zechariah 14 in the TNTIL

Zechariah 14 in the TNTIN

Zechariah 14 in the TNTIP

Zechariah 14 in the TNTIZ

Zechariah 14 in the TOMA

Zechariah 14 in the TTENT

Zechariah 14 in the UBG

Zechariah 14 in the UGV

Zechariah 14 in the UGV2

Zechariah 14 in the UGV3

Zechariah 14 in the VBL

Zechariah 14 in the VDCC

Zechariah 14 in the YALU

Zechariah 14 in the YAPE

Zechariah 14 in the YBVTP

Zechariah 14 in the ZBP