1 Chronicles 29 (BOGWICC)

1 Kenaka, mfumu Davide inati kwa gulu lonse: “Mwana wanga Solomoni amene Mulungu wamusankha ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Ntchitoyi ndi yayikulu chifukwa nyumba yaufumuyi si ya munthu, koma ndi ya Yehova Mulungu. 2 Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka. 3 Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu: 4 Matani 100 agolide (golide wa ku Ofiri) ndi matani 240 a siliva woyengeka bwino wokutira makoma a nyumba, 5 zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?” 6 Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu. 7 Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo. 8 Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni. 9 Anthu anakondwa chifukwa cha kupereka mwaufulu kwa atsogoleri awo, pakuti anapereka kwa Yehova mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse. Nayenso mfumu Davide anakondwera kwambiri. 10 Davide anatamanda Yehova pamaso pa gulu lonse, ponena kuti,“Mutamandidwe Inu YehovaMulungu wa kholo lathu Israelikuchokera muyaya mpaka muyaya. 11 Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu,ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola.Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu.Wanu, Inu Yehova ndi ufumu;Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse. 12 Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu;Inu ndinu wolamulira zinthu zonse.Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu,kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse. 13 Tsopano Mulungu wathu, ife tikukuthokozanindi kutamanda dzina lanu laulemerero. 14 “Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu. 15 Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo. 16 Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu. 17 Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu. 18 Inu Yehova Mulungu wa makolo athu Abrahamu, Isake ndi Israeli, mukhazikitse chofuna ichi mʼmitima ya anthu anu kwamuyaya, ndipo mukhazikitse mtima wokhulupirika kwa Inu. 19 Ndipo mumupatse mwana wanga Solomoni mtima wodzipereka kwathunthu kwa Inu kuti asunge malamulo anu, zofuna ndi malangizo anu. Achite chilichonse pomanga nyumba yaufumu imene ine ndayipezera zofunika zonse.” 20 Kenaka mfumu Davide inati kwa gulu lonse, “Tamandani Yehova Mulungu wanu.” Kotero onse anatamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anawerama pansi ndi kugona chafufumimba pamaso pa Yehova ndi mfumu. 21 Mmawa mwake anthu anapereka nsembe zosiyanasiyana ndi nsembe zopsereza kwa Yehova; ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa zamphongo 1,000 ndi ana ankhosa 1,000, pamodzi ndi nsembe yachakumwa ndi nsembe zina zambiri zoperekera Aisraeli onse. 22 Tsiku limeneli, iwo anadya ndi kumwa mosangalala pamaso pa Yehova ndipo anavomereza Solomoni mwana wa Davide kukhala mfumu yawo kachiwiri.Anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala wolamulira wawo ndipo Zadoki anadzozedwa kukhala wansembe. 23 Ndipo Solomoni ankakhala pa mpando waufumu wa Yehova monga mfumu mʼmalo mwa Davide abambo ake. Iye analemera ndipo Aisraeli onse ankamumvera. 24 Akuluakulu onse a ankhondo ndi anthu amphamvu, pamodzinso ndi ana onse aamuna a mfumu Davide, analonjeza kumvera mfumu Solomoni. 25 Yehova anamukweza kwambiri Solomoni pamaso pa Aisraeli onse ndi kumupatsa ulemerero waufumu umene sunapatsidwepo kwa mfumu ina iliyonse ya Israeli. 26 Davide mwana wa Yese anali mfumu ya Aisraeli onse. 27 Iye analamulira Israeli kwa zaka makumi anayi; zaka zisanu ndi ziwiri ali ku Hebroni ndi zaka 33 ali ku Yerusalemu. 28 Iye anamwalira atakalamba kwambiri, atakhala ndi moyo wautali, chuma ndi ulemu. Solomoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 29 Tsono zonse zimene mfumu Davide anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mneneri Samueli, mʼbuku la mneneri Natani ndi mʼbuku la mneneri Gadi, 30 pamodzi ndi tsatanetsatane wa mbiri ya ulamuliro wake ndi mphamvu zake, ndi zonse zomwe zinamuzungulira iye ndi Israeli ndiponso mafumu a mayiko ena onse.

In Other Versions

1 Chronicles 29 in the ANGEFD

1 Chronicles 29 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 29 in the AS21

1 Chronicles 29 in the BAGH

1 Chronicles 29 in the BBPNG

1 Chronicles 29 in the BBT1E

1 Chronicles 29 in the BDS

1 Chronicles 29 in the BEV

1 Chronicles 29 in the BHAD

1 Chronicles 29 in the BIB

1 Chronicles 29 in the BLPT

1 Chronicles 29 in the BNT

1 Chronicles 29 in the BNTABOOT

1 Chronicles 29 in the BNTLV

1 Chronicles 29 in the BOATCB

1 Chronicles 29 in the BOATCB2

1 Chronicles 29 in the BOBCV

1 Chronicles 29 in the BOCNT

1 Chronicles 29 in the BOECS

1 Chronicles 29 in the BOHCB

1 Chronicles 29 in the BOHCV

1 Chronicles 29 in the BOHLNT

1 Chronicles 29 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 29 in the BOICB

1 Chronicles 29 in the BOILNTAP

1 Chronicles 29 in the BOITCV

1 Chronicles 29 in the BOKCV

1 Chronicles 29 in the BOKCV2

1 Chronicles 29 in the BOKHWOG

1 Chronicles 29 in the BOKSSV

1 Chronicles 29 in the BOLCB

1 Chronicles 29 in the BOLCB2

1 Chronicles 29 in the BOMCV

1 Chronicles 29 in the BONAV

1 Chronicles 29 in the BONCB

1 Chronicles 29 in the BONLT

1 Chronicles 29 in the BONUT2

1 Chronicles 29 in the BOPLNT

1 Chronicles 29 in the BOSCB

1 Chronicles 29 in the BOSNC

1 Chronicles 29 in the BOTLNT

1 Chronicles 29 in the BOVCB

1 Chronicles 29 in the BOYCB

1 Chronicles 29 in the BPBB

1 Chronicles 29 in the BPH

1 Chronicles 29 in the BSB

1 Chronicles 29 in the CCB

1 Chronicles 29 in the CUV

1 Chronicles 29 in the CUVS

1 Chronicles 29 in the DBT

1 Chronicles 29 in the DGDNT

1 Chronicles 29 in the DHNT

1 Chronicles 29 in the DNT

1 Chronicles 29 in the ELBE

1 Chronicles 29 in the EMTV

1 Chronicles 29 in the ESV

1 Chronicles 29 in the FBV

1 Chronicles 29 in the FEB

1 Chronicles 29 in the GGMNT

1 Chronicles 29 in the GNT

1 Chronicles 29 in the HARY

1 Chronicles 29 in the HNT

1 Chronicles 29 in the IRVA

1 Chronicles 29 in the IRVB

1 Chronicles 29 in the IRVG

1 Chronicles 29 in the IRVH

1 Chronicles 29 in the IRVK

1 Chronicles 29 in the IRVM

1 Chronicles 29 in the IRVM2

1 Chronicles 29 in the IRVO

1 Chronicles 29 in the IRVP

1 Chronicles 29 in the IRVT

1 Chronicles 29 in the IRVT2

1 Chronicles 29 in the IRVU

1 Chronicles 29 in the ISVN

1 Chronicles 29 in the JSNT

1 Chronicles 29 in the KAPI

1 Chronicles 29 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 29 in the KBV

1 Chronicles 29 in the KJV

1 Chronicles 29 in the KNFD

1 Chronicles 29 in the LBA

1 Chronicles 29 in the LBLA

1 Chronicles 29 in the LNT

1 Chronicles 29 in the LSV

1 Chronicles 29 in the MAAL

1 Chronicles 29 in the MBV

1 Chronicles 29 in the MBV2

1 Chronicles 29 in the MHNT

1 Chronicles 29 in the MKNFD

1 Chronicles 29 in the MNG

1 Chronicles 29 in the MNT

1 Chronicles 29 in the MNT2

1 Chronicles 29 in the MRS1T

1 Chronicles 29 in the NAA

1 Chronicles 29 in the NASB

1 Chronicles 29 in the NBLA

1 Chronicles 29 in the NBS

1 Chronicles 29 in the NBVTP

1 Chronicles 29 in the NET2

1 Chronicles 29 in the NIV11

1 Chronicles 29 in the NNT

1 Chronicles 29 in the NNT2

1 Chronicles 29 in the NNT3

1 Chronicles 29 in the PDDPT

1 Chronicles 29 in the PFNT

1 Chronicles 29 in the RMNT

1 Chronicles 29 in the SBIAS

1 Chronicles 29 in the SBIBS

1 Chronicles 29 in the SBIBS2

1 Chronicles 29 in the SBICS

1 Chronicles 29 in the SBIDS

1 Chronicles 29 in the SBIGS

1 Chronicles 29 in the SBIHS

1 Chronicles 29 in the SBIIS

1 Chronicles 29 in the SBIIS2

1 Chronicles 29 in the SBIIS3

1 Chronicles 29 in the SBIKS

1 Chronicles 29 in the SBIKS2

1 Chronicles 29 in the SBIMS

1 Chronicles 29 in the SBIOS

1 Chronicles 29 in the SBIPS

1 Chronicles 29 in the SBISS

1 Chronicles 29 in the SBITS

1 Chronicles 29 in the SBITS2

1 Chronicles 29 in the SBITS3

1 Chronicles 29 in the SBITS4

1 Chronicles 29 in the SBIUS

1 Chronicles 29 in the SBIVS

1 Chronicles 29 in the SBT

1 Chronicles 29 in the SBT1E

1 Chronicles 29 in the SCHL

1 Chronicles 29 in the SNT

1 Chronicles 29 in the SUSU

1 Chronicles 29 in the SUSU2

1 Chronicles 29 in the SYNO

1 Chronicles 29 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 29 in the TBT1E

1 Chronicles 29 in the TBT1E2

1 Chronicles 29 in the TFTIP

1 Chronicles 29 in the TFTU

1 Chronicles 29 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 29 in the THAI

1 Chronicles 29 in the TNFD

1 Chronicles 29 in the TNT

1 Chronicles 29 in the TNTIK

1 Chronicles 29 in the TNTIL

1 Chronicles 29 in the TNTIN

1 Chronicles 29 in the TNTIP

1 Chronicles 29 in the TNTIZ

1 Chronicles 29 in the TOMA

1 Chronicles 29 in the TTENT

1 Chronicles 29 in the UBG

1 Chronicles 29 in the UGV

1 Chronicles 29 in the UGV2

1 Chronicles 29 in the UGV3

1 Chronicles 29 in the VBL

1 Chronicles 29 in the VDCC

1 Chronicles 29 in the YALU

1 Chronicles 29 in the YAPE

1 Chronicles 29 in the YBVTP

1 Chronicles 29 in the ZBP