1 Peter 2 (BOGWICC)
1 Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse. 2 Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu, 3 pakuti tsopano mwalawadi kuti Ambuye ndi wabwino. 4 Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali, 5 inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. 6 Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti,“Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni,wosankhika ndi wamtengowapatali.Amene akhulupirira Iyesadzachititsidwa manyazi.” 7 Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira,“Mwala umene amisiri anawukanawasanduka mwala wa maziko, 8 ndi“Mwala wopunthwitsa anthundiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.”Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo. 9 Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa. 10 Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo. 11 Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu. 12 Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere. 13 Gonjerani maulamuliro onse chifukwa cha Ambuye. Kaya ndi mfumu, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro waukulu, 14 kaya ndi mabwanamkubwa, pakuti watumidwa ndi mfumu kuti alange onse amene amachita zoyipa ndi kuyamikira onse amene amachita zabwino. 15 Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa. 16 Mukhale monga mfulu, koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo ngati chophimbira zoyipa; mukhale monga atumiki a Mulungu. 17 Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu. 18 Inu akapolo, gonjerani ambuye anu ndi kuwachitira ulemu, osati kwa iwo okha amene ndi abwino ndi omvetsa zinthu, komanso kwa amene ndi ankhanza. 19 Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo. 20 Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu. 21 Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake. 22 “Iye sanachite tchimokapena kunena bodza.” 23 Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama. 24 Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa. 25 Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.
In Other Versions
1 Peter 2 in the ANGEFD
1 Peter 2 in the ANTPNG2D
1 Peter 2 in the AS21
1 Peter 2 in the BAGH
1 Peter 2 in the BBPNG
1 Peter 2 in the BBT1E
1 Peter 2 in the BDS
1 Peter 2 in the BEV
1 Peter 2 in the BHAD
1 Peter 2 in the BIB
1 Peter 2 in the BLPT
1 Peter 2 in the BNT
1 Peter 2 in the BNTABOOT
1 Peter 2 in the BNTLV
1 Peter 2 in the BOATCB
1 Peter 2 in the BOATCB2
1 Peter 2 in the BOBCV
1 Peter 2 in the BOCNT
1 Peter 2 in the BOECS
1 Peter 2 in the BOHCB
1 Peter 2 in the BOHCV
1 Peter 2 in the BOHLNT
1 Peter 2 in the BOHNTLTAL
1 Peter 2 in the BOICB
1 Peter 2 in the BOILNTAP
1 Peter 2 in the BOITCV
1 Peter 2 in the BOKCV
1 Peter 2 in the BOKCV2
1 Peter 2 in the BOKHWOG
1 Peter 2 in the BOKSSV
1 Peter 2 in the BOLCB
1 Peter 2 in the BOLCB2
1 Peter 2 in the BOMCV
1 Peter 2 in the BONAV
1 Peter 2 in the BONCB
1 Peter 2 in the BONLT
1 Peter 2 in the BONUT2
1 Peter 2 in the BOPLNT
1 Peter 2 in the BOSCB
1 Peter 2 in the BOSNC
1 Peter 2 in the BOTLNT
1 Peter 2 in the BOVCB
1 Peter 2 in the BOYCB
1 Peter 2 in the BPBB
1 Peter 2 in the BPH
1 Peter 2 in the BSB
1 Peter 2 in the CCB
1 Peter 2 in the CUV
1 Peter 2 in the CUVS
1 Peter 2 in the DBT
1 Peter 2 in the DGDNT
1 Peter 2 in the DHNT
1 Peter 2 in the DNT
1 Peter 2 in the ELBE
1 Peter 2 in the EMTV
1 Peter 2 in the ESV
1 Peter 2 in the FBV
1 Peter 2 in the FEB
1 Peter 2 in the GGMNT
1 Peter 2 in the GNT
1 Peter 2 in the HARY
1 Peter 2 in the HNT
1 Peter 2 in the IRVA
1 Peter 2 in the IRVB
1 Peter 2 in the IRVG
1 Peter 2 in the IRVH
1 Peter 2 in the IRVK
1 Peter 2 in the IRVM
1 Peter 2 in the IRVM2
1 Peter 2 in the IRVO
1 Peter 2 in the IRVP
1 Peter 2 in the IRVT
1 Peter 2 in the IRVT2
1 Peter 2 in the IRVU
1 Peter 2 in the ISVN
1 Peter 2 in the JSNT
1 Peter 2 in the KAPI
1 Peter 2 in the KBT1ETNIK
1 Peter 2 in the KBV
1 Peter 2 in the KJV
1 Peter 2 in the KNFD
1 Peter 2 in the LBA
1 Peter 2 in the LBLA
1 Peter 2 in the LNT
1 Peter 2 in the LSV
1 Peter 2 in the MAAL
1 Peter 2 in the MBV
1 Peter 2 in the MBV2
1 Peter 2 in the MHNT
1 Peter 2 in the MKNFD
1 Peter 2 in the MNG
1 Peter 2 in the MNT
1 Peter 2 in the MNT2
1 Peter 2 in the MRS1T
1 Peter 2 in the NAA
1 Peter 2 in the NASB
1 Peter 2 in the NBLA
1 Peter 2 in the NBS
1 Peter 2 in the NBVTP
1 Peter 2 in the NET2
1 Peter 2 in the NIV11
1 Peter 2 in the NNT
1 Peter 2 in the NNT2
1 Peter 2 in the NNT3
1 Peter 2 in the PDDPT
1 Peter 2 in the PFNT
1 Peter 2 in the RMNT
1 Peter 2 in the SBIAS
1 Peter 2 in the SBIBS
1 Peter 2 in the SBIBS2
1 Peter 2 in the SBICS
1 Peter 2 in the SBIDS
1 Peter 2 in the SBIGS
1 Peter 2 in the SBIHS
1 Peter 2 in the SBIIS
1 Peter 2 in the SBIIS2
1 Peter 2 in the SBIIS3
1 Peter 2 in the SBIKS
1 Peter 2 in the SBIKS2
1 Peter 2 in the SBIMS
1 Peter 2 in the SBIOS
1 Peter 2 in the SBIPS
1 Peter 2 in the SBISS
1 Peter 2 in the SBITS
1 Peter 2 in the SBITS2
1 Peter 2 in the SBITS3
1 Peter 2 in the SBITS4
1 Peter 2 in the SBIUS
1 Peter 2 in the SBIVS
1 Peter 2 in the SBT
1 Peter 2 in the SBT1E
1 Peter 2 in the SCHL
1 Peter 2 in the SNT
1 Peter 2 in the SUSU
1 Peter 2 in the SUSU2
1 Peter 2 in the SYNO
1 Peter 2 in the TBIAOTANT
1 Peter 2 in the TBT1E
1 Peter 2 in the TBT1E2
1 Peter 2 in the TFTIP
1 Peter 2 in the TFTU
1 Peter 2 in the TGNTATF3T
1 Peter 2 in the THAI
1 Peter 2 in the TNFD
1 Peter 2 in the TNT
1 Peter 2 in the TNTIK
1 Peter 2 in the TNTIL
1 Peter 2 in the TNTIN
1 Peter 2 in the TNTIP
1 Peter 2 in the TNTIZ
1 Peter 2 in the TOMA
1 Peter 2 in the TTENT
1 Peter 2 in the UBG
1 Peter 2 in the UGV
1 Peter 2 in the UGV2
1 Peter 2 in the UGV3
1 Peter 2 in the VBL
1 Peter 2 in the VDCC
1 Peter 2 in the YALU
1 Peter 2 in the YAPE
1 Peter 2 in the YBVTP
1 Peter 2 in the ZBP