1 Samuel 13 (BOGWICC)

1 Sauli analowa ufumu ali ndi zaka makumi atatu, ndipo analamulira Israeli kwa zaka 42. 2 Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo. 3 Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli. 4 Choncho Aisraeli onse anamva kuti Sauli wakantha mkulu wa ankhondo Wachifilisiti ndi kuti Afilisti anayipidwa nawo Aisraeli. Ndiye anthu anayitanidwa kuti abwere kwa Sauli ku Giligala. 5 Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni. 6 Pamene Aisraeli anaona kuti anali pamavuto akulu, poti anali atapanikizidwa kwambiri, anabisala mʼmapanga, mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼmakwalala ndi mʼzitsime. 7 Ahebri ena anawoloka Yorodani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi.Koma Sauli anakhalabe ku Giligala ndipo ankhondo onse amene anali naye anali njenjenje ndi mantha. 8 Saulo anadikirira masiku asanu ndi awiri, monga mwa nthawi imene ananena Samueli. Koma Samueli sanabwere ku Giligala, ndipo anthu anayamba kumuthawa Sauli uja. 9 Kotero iye anati, “Bwera nayoni nsembe yopsereza ndi nsembe ya chiyanjano.” Ndipo Sauli anapereka nsembe yopsereza. 10 Atangomaliza kupereka nsembe, anangoona Samueli watulukira ndipo Sauli anapita kukamulonjera. 11 Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?”Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi, 12 ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, chonsecho sindinapemphe Yehova kuti andikomere mtima.’ Motero ndinakakamizika kupereka nsembe yopsereza.” 13 Samueli anati, “Mwachita zopusa. Simunatsate zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muchite. Mukanazitsata, Yehova akanawukhazikitsa ufumu wanu mu Israeli mpaka kalekale. 14 Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Yehova wapeza munthu wapamtima pake ndipo wamusankha kukhala mtsogoleri wa anthu ake chifukwa inu simunasunge malamulo a Yehova.” 15 Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600. 16 Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi asilikali amene anali naye aja amakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti anamanga misasa yawo ku Mikimasi. 17 Ankhondo a Afilisti anatuluka mʼmisasa yawo mʼmagulu atatu. Gulu lina linapita ku Ofiri ku dziko la Suwala. 18 Gulu lina linalunjika ku Beti-Horoni, ndipo gulu lachitatu linalunjika ku malire oyangʼanana ndi chigwa cha Zeboimu cha ku chipululu. 19 Nthawi imeneyo nʼkuti mulibe osula zitsulo mʼdziko lonse la Israeli, pakuti Afilisti anati, “Tisawalole Aheberi kudzipangira okha malupanga kapena mikondo!” 20 Kotero Aisraeli onse amapita kwa Afilisti kukanoletsa mapulawo, makasu, nkhwangwa ndi zikwakwa zawo. 21 Mtengo wonolera mapulawo ndi makasu unali zigawo ziwiri za sekeli, mtengo wonolera zisonga ndi nkhwangwa unali gawo limodzi la Sekeli. 22 Motero tsiku la nkhondolo panalibe lupanga kapena mkondo mʼdzanja la aliyense amene anatsatira Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi Yonatani, iwo okha ndiwo anali ndi zida. 23 Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi.

In Other Versions

1 Samuel 13 in the ANGEFD

1 Samuel 13 in the ANTPNG2D

1 Samuel 13 in the AS21

1 Samuel 13 in the BAGH

1 Samuel 13 in the BBPNG

1 Samuel 13 in the BBT1E

1 Samuel 13 in the BDS

1 Samuel 13 in the BEV

1 Samuel 13 in the BHAD

1 Samuel 13 in the BIB

1 Samuel 13 in the BLPT

1 Samuel 13 in the BNT

1 Samuel 13 in the BNTABOOT

1 Samuel 13 in the BNTLV

1 Samuel 13 in the BOATCB

1 Samuel 13 in the BOATCB2

1 Samuel 13 in the BOBCV

1 Samuel 13 in the BOCNT

1 Samuel 13 in the BOECS

1 Samuel 13 in the BOHCB

1 Samuel 13 in the BOHCV

1 Samuel 13 in the BOHLNT

1 Samuel 13 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 13 in the BOICB

1 Samuel 13 in the BOILNTAP

1 Samuel 13 in the BOITCV

1 Samuel 13 in the BOKCV

1 Samuel 13 in the BOKCV2

1 Samuel 13 in the BOKHWOG

1 Samuel 13 in the BOKSSV

1 Samuel 13 in the BOLCB

1 Samuel 13 in the BOLCB2

1 Samuel 13 in the BOMCV

1 Samuel 13 in the BONAV

1 Samuel 13 in the BONCB

1 Samuel 13 in the BONLT

1 Samuel 13 in the BONUT2

1 Samuel 13 in the BOPLNT

1 Samuel 13 in the BOSCB

1 Samuel 13 in the BOSNC

1 Samuel 13 in the BOTLNT

1 Samuel 13 in the BOVCB

1 Samuel 13 in the BOYCB

1 Samuel 13 in the BPBB

1 Samuel 13 in the BPH

1 Samuel 13 in the BSB

1 Samuel 13 in the CCB

1 Samuel 13 in the CUV

1 Samuel 13 in the CUVS

1 Samuel 13 in the DBT

1 Samuel 13 in the DGDNT

1 Samuel 13 in the DHNT

1 Samuel 13 in the DNT

1 Samuel 13 in the ELBE

1 Samuel 13 in the EMTV

1 Samuel 13 in the ESV

1 Samuel 13 in the FBV

1 Samuel 13 in the FEB

1 Samuel 13 in the GGMNT

1 Samuel 13 in the GNT

1 Samuel 13 in the HARY

1 Samuel 13 in the HNT

1 Samuel 13 in the IRVA

1 Samuel 13 in the IRVB

1 Samuel 13 in the IRVG

1 Samuel 13 in the IRVH

1 Samuel 13 in the IRVK

1 Samuel 13 in the IRVM

1 Samuel 13 in the IRVM2

1 Samuel 13 in the IRVO

1 Samuel 13 in the IRVP

1 Samuel 13 in the IRVT

1 Samuel 13 in the IRVT2

1 Samuel 13 in the IRVU

1 Samuel 13 in the ISVN

1 Samuel 13 in the JSNT

1 Samuel 13 in the KAPI

1 Samuel 13 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 13 in the KBV

1 Samuel 13 in the KJV

1 Samuel 13 in the KNFD

1 Samuel 13 in the LBA

1 Samuel 13 in the LBLA

1 Samuel 13 in the LNT

1 Samuel 13 in the LSV

1 Samuel 13 in the MAAL

1 Samuel 13 in the MBV

1 Samuel 13 in the MBV2

1 Samuel 13 in the MHNT

1 Samuel 13 in the MKNFD

1 Samuel 13 in the MNG

1 Samuel 13 in the MNT

1 Samuel 13 in the MNT2

1 Samuel 13 in the MRS1T

1 Samuel 13 in the NAA

1 Samuel 13 in the NASB

1 Samuel 13 in the NBLA

1 Samuel 13 in the NBS

1 Samuel 13 in the NBVTP

1 Samuel 13 in the NET2

1 Samuel 13 in the NIV11

1 Samuel 13 in the NNT

1 Samuel 13 in the NNT2

1 Samuel 13 in the NNT3

1 Samuel 13 in the PDDPT

1 Samuel 13 in the PFNT

1 Samuel 13 in the RMNT

1 Samuel 13 in the SBIAS

1 Samuel 13 in the SBIBS

1 Samuel 13 in the SBIBS2

1 Samuel 13 in the SBICS

1 Samuel 13 in the SBIDS

1 Samuel 13 in the SBIGS

1 Samuel 13 in the SBIHS

1 Samuel 13 in the SBIIS

1 Samuel 13 in the SBIIS2

1 Samuel 13 in the SBIIS3

1 Samuel 13 in the SBIKS

1 Samuel 13 in the SBIKS2

1 Samuel 13 in the SBIMS

1 Samuel 13 in the SBIOS

1 Samuel 13 in the SBIPS

1 Samuel 13 in the SBISS

1 Samuel 13 in the SBITS

1 Samuel 13 in the SBITS2

1 Samuel 13 in the SBITS3

1 Samuel 13 in the SBITS4

1 Samuel 13 in the SBIUS

1 Samuel 13 in the SBIVS

1 Samuel 13 in the SBT

1 Samuel 13 in the SBT1E

1 Samuel 13 in the SCHL

1 Samuel 13 in the SNT

1 Samuel 13 in the SUSU

1 Samuel 13 in the SUSU2

1 Samuel 13 in the SYNO

1 Samuel 13 in the TBIAOTANT

1 Samuel 13 in the TBT1E

1 Samuel 13 in the TBT1E2

1 Samuel 13 in the TFTIP

1 Samuel 13 in the TFTU

1 Samuel 13 in the TGNTATF3T

1 Samuel 13 in the THAI

1 Samuel 13 in the TNFD

1 Samuel 13 in the TNT

1 Samuel 13 in the TNTIK

1 Samuel 13 in the TNTIL

1 Samuel 13 in the TNTIN

1 Samuel 13 in the TNTIP

1 Samuel 13 in the TNTIZ

1 Samuel 13 in the TOMA

1 Samuel 13 in the TTENT

1 Samuel 13 in the UBG

1 Samuel 13 in the UGV

1 Samuel 13 in the UGV2

1 Samuel 13 in the UGV3

1 Samuel 13 in the VBL

1 Samuel 13 in the VDCC

1 Samuel 13 in the YALU

1 Samuel 13 in the YAPE

1 Samuel 13 in the YBVTP

1 Samuel 13 in the ZBP