1 Timothy 6 (BOGWICC)

1 Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu. 2 Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo.Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu. 3 Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu, 4 ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa, 5 ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma. 6 Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. 7 Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. 8 Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. 9 Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko. 10 Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri. 11 Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa. 12 Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. 13 Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni. 14 Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera. 15 Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye. 16 Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni. 17 Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. 18 Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo. 19 Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni. 20 Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru. 21 Anthu ena chifukwa chovomereza nzeru zotere, asochera nʼkutaya chikhulupiriro chawo.Chisomo chikhale nawe.

In Other Versions

1 Timothy 6 in the ANGEFD

1 Timothy 6 in the ANTPNG2D

1 Timothy 6 in the AS21

1 Timothy 6 in the BAGH

1 Timothy 6 in the BBPNG

1 Timothy 6 in the BBT1E

1 Timothy 6 in the BDS

1 Timothy 6 in the BEV

1 Timothy 6 in the BHAD

1 Timothy 6 in the BIB

1 Timothy 6 in the BLPT

1 Timothy 6 in the BNT

1 Timothy 6 in the BNTABOOT

1 Timothy 6 in the BNTLV

1 Timothy 6 in the BOATCB

1 Timothy 6 in the BOATCB2

1 Timothy 6 in the BOBCV

1 Timothy 6 in the BOCNT

1 Timothy 6 in the BOECS

1 Timothy 6 in the BOHCB

1 Timothy 6 in the BOHCV

1 Timothy 6 in the BOHLNT

1 Timothy 6 in the BOHNTLTAL

1 Timothy 6 in the BOICB

1 Timothy 6 in the BOILNTAP

1 Timothy 6 in the BOITCV

1 Timothy 6 in the BOKCV

1 Timothy 6 in the BOKCV2

1 Timothy 6 in the BOKHWOG

1 Timothy 6 in the BOKSSV

1 Timothy 6 in the BOLCB

1 Timothy 6 in the BOLCB2

1 Timothy 6 in the BOMCV

1 Timothy 6 in the BONAV

1 Timothy 6 in the BONCB

1 Timothy 6 in the BONLT

1 Timothy 6 in the BONUT2

1 Timothy 6 in the BOPLNT

1 Timothy 6 in the BOSCB

1 Timothy 6 in the BOSNC

1 Timothy 6 in the BOTLNT

1 Timothy 6 in the BOVCB

1 Timothy 6 in the BOYCB

1 Timothy 6 in the BPBB

1 Timothy 6 in the BPH

1 Timothy 6 in the BSB

1 Timothy 6 in the CCB

1 Timothy 6 in the CUV

1 Timothy 6 in the CUVS

1 Timothy 6 in the DBT

1 Timothy 6 in the DGDNT

1 Timothy 6 in the DHNT

1 Timothy 6 in the DNT

1 Timothy 6 in the ELBE

1 Timothy 6 in the EMTV

1 Timothy 6 in the ESV

1 Timothy 6 in the FBV

1 Timothy 6 in the FEB

1 Timothy 6 in the GGMNT

1 Timothy 6 in the GNT

1 Timothy 6 in the HARY

1 Timothy 6 in the HNT

1 Timothy 6 in the IRVA

1 Timothy 6 in the IRVB

1 Timothy 6 in the IRVG

1 Timothy 6 in the IRVH

1 Timothy 6 in the IRVK

1 Timothy 6 in the IRVM

1 Timothy 6 in the IRVM2

1 Timothy 6 in the IRVO

1 Timothy 6 in the IRVP

1 Timothy 6 in the IRVT

1 Timothy 6 in the IRVT2

1 Timothy 6 in the IRVU

1 Timothy 6 in the ISVN

1 Timothy 6 in the JSNT

1 Timothy 6 in the KAPI

1 Timothy 6 in the KBT1ETNIK

1 Timothy 6 in the KBV

1 Timothy 6 in the KJV

1 Timothy 6 in the KNFD

1 Timothy 6 in the LBA

1 Timothy 6 in the LBLA

1 Timothy 6 in the LNT

1 Timothy 6 in the LSV

1 Timothy 6 in the MAAL

1 Timothy 6 in the MBV

1 Timothy 6 in the MBV2

1 Timothy 6 in the MHNT

1 Timothy 6 in the MKNFD

1 Timothy 6 in the MNG

1 Timothy 6 in the MNT

1 Timothy 6 in the MNT2

1 Timothy 6 in the MRS1T

1 Timothy 6 in the NAA

1 Timothy 6 in the NASB

1 Timothy 6 in the NBLA

1 Timothy 6 in the NBS

1 Timothy 6 in the NBVTP

1 Timothy 6 in the NET2

1 Timothy 6 in the NIV11

1 Timothy 6 in the NNT

1 Timothy 6 in the NNT2

1 Timothy 6 in the NNT3

1 Timothy 6 in the PDDPT

1 Timothy 6 in the PFNT

1 Timothy 6 in the RMNT

1 Timothy 6 in the SBIAS

1 Timothy 6 in the SBIBS

1 Timothy 6 in the SBIBS2

1 Timothy 6 in the SBICS

1 Timothy 6 in the SBIDS

1 Timothy 6 in the SBIGS

1 Timothy 6 in the SBIHS

1 Timothy 6 in the SBIIS

1 Timothy 6 in the SBIIS2

1 Timothy 6 in the SBIIS3

1 Timothy 6 in the SBIKS

1 Timothy 6 in the SBIKS2

1 Timothy 6 in the SBIMS

1 Timothy 6 in the SBIOS

1 Timothy 6 in the SBIPS

1 Timothy 6 in the SBISS

1 Timothy 6 in the SBITS

1 Timothy 6 in the SBITS2

1 Timothy 6 in the SBITS3

1 Timothy 6 in the SBITS4

1 Timothy 6 in the SBIUS

1 Timothy 6 in the SBIVS

1 Timothy 6 in the SBT

1 Timothy 6 in the SBT1E

1 Timothy 6 in the SCHL

1 Timothy 6 in the SNT

1 Timothy 6 in the SUSU

1 Timothy 6 in the SUSU2

1 Timothy 6 in the SYNO

1 Timothy 6 in the TBIAOTANT

1 Timothy 6 in the TBT1E

1 Timothy 6 in the TBT1E2

1 Timothy 6 in the TFTIP

1 Timothy 6 in the TFTU

1 Timothy 6 in the TGNTATF3T

1 Timothy 6 in the THAI

1 Timothy 6 in the TNFD

1 Timothy 6 in the TNT

1 Timothy 6 in the TNTIK

1 Timothy 6 in the TNTIL

1 Timothy 6 in the TNTIN

1 Timothy 6 in the TNTIP

1 Timothy 6 in the TNTIZ

1 Timothy 6 in the TOMA

1 Timothy 6 in the TTENT

1 Timothy 6 in the UBG

1 Timothy 6 in the UGV

1 Timothy 6 in the UGV2

1 Timothy 6 in the UGV3

1 Timothy 6 in the VBL

1 Timothy 6 in the VDCC

1 Timothy 6 in the YALU

1 Timothy 6 in the YAPE

1 Timothy 6 in the YBVTP

1 Timothy 6 in the ZBP