2 Samuel 16 (BOGWICC)

1 Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo. 2 Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?”Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.” 3 Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?”Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ” 4 Ndipo mfumu inati kwa Ziba, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako tsopano.”Ziba anati, “Ine modzichepetsa ndikukugwandirani, mbuye wanga mfumu, kuti ndipeze chisomo pamaso panu.” 5 Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera. 6 Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake. 7 Potukwana, Simeiyo amati, “Choka iwe, choka iwe, munthu wopha anthu, munthu wachabechabe iwe! 8 Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!” 9 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.” 10 Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’ ” 11 Tsono Davide anati kwa Abisai ndi akuluakulu ake onse, “Mwana wanga wobereka ndekha akufuna kundipha. Nanji tsono munthu wa fuko la Benjamini uyu! Musiyeni; mulekeni atukwane pakuti Yehova wachita kumuwuza kuti atero. 12 Mwina Yehova adzaona mazunzo anga ndipo adzandibwezera zabwino chifukwa cha kutukwanidwa kumene ndikulandira lero.” 13 Kotero Davide ndi anthu ake anapitirira kuyenda mu msewu pamene Simei amayenda mʼmbali mwa phiri moyangʼanana naye akutukwana ndi kuponya miyala pamene amayenda nʼkumamutsiranso dothi. 14 Mfumu ndi anthu ake onse anafika kumene amapita atatopa kwambiri. Ndipo kumeneko anapumula. 15 Pa nthawi imeneyi Abisalomu ndi Aisraeli ena onse anabwera ku Yerusalemu, Ahitofele anali naye. 16 Tsono Husai Mwariki bwenzi la Davide anapita kwa Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu! Ikhale ndi moyo wautali mfumu!” 17 Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?” 18 Husai anati kwa Abisalomu, “Ayi, ndidzakhala wake wa amene Yehova wamusankha, wosankhidwa ndi anthu awa ndi anthu onse a Israeli, ndipo ndidzakhala wake nthawi zonse. 19 Kodi ndidzatumikiranso yani? Kodi sinditumikira mwana wa mfumu? Monga momwe ndinatumikira abambo anu, kotero ndidzatumikiranso inu.” 20 Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?” 21 Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.” 22 Choncho anamangira tenti Abisalomu pa denga la nyumba ndipo iye anagona ndi azikazi a abambo ake Aisraeli onse akuona. 23 Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele.

In Other Versions

2 Samuel 16 in the ANGEFD

2 Samuel 16 in the ANTPNG2D

2 Samuel 16 in the AS21

2 Samuel 16 in the BAGH

2 Samuel 16 in the BBPNG

2 Samuel 16 in the BBT1E

2 Samuel 16 in the BDS

2 Samuel 16 in the BEV

2 Samuel 16 in the BHAD

2 Samuel 16 in the BIB

2 Samuel 16 in the BLPT

2 Samuel 16 in the BNT

2 Samuel 16 in the BNTABOOT

2 Samuel 16 in the BNTLV

2 Samuel 16 in the BOATCB

2 Samuel 16 in the BOATCB2

2 Samuel 16 in the BOBCV

2 Samuel 16 in the BOCNT

2 Samuel 16 in the BOECS

2 Samuel 16 in the BOHCB

2 Samuel 16 in the BOHCV

2 Samuel 16 in the BOHLNT

2 Samuel 16 in the BOHNTLTAL

2 Samuel 16 in the BOICB

2 Samuel 16 in the BOILNTAP

2 Samuel 16 in the BOITCV

2 Samuel 16 in the BOKCV

2 Samuel 16 in the BOKCV2

2 Samuel 16 in the BOKHWOG

2 Samuel 16 in the BOKSSV

2 Samuel 16 in the BOLCB

2 Samuel 16 in the BOLCB2

2 Samuel 16 in the BOMCV

2 Samuel 16 in the BONAV

2 Samuel 16 in the BONCB

2 Samuel 16 in the BONLT

2 Samuel 16 in the BONUT2

2 Samuel 16 in the BOPLNT

2 Samuel 16 in the BOSCB

2 Samuel 16 in the BOSNC

2 Samuel 16 in the BOTLNT

2 Samuel 16 in the BOVCB

2 Samuel 16 in the BOYCB

2 Samuel 16 in the BPBB

2 Samuel 16 in the BPH

2 Samuel 16 in the BSB

2 Samuel 16 in the CCB

2 Samuel 16 in the CUV

2 Samuel 16 in the CUVS

2 Samuel 16 in the DBT

2 Samuel 16 in the DGDNT

2 Samuel 16 in the DHNT

2 Samuel 16 in the DNT

2 Samuel 16 in the ELBE

2 Samuel 16 in the EMTV

2 Samuel 16 in the ESV

2 Samuel 16 in the FBV

2 Samuel 16 in the FEB

2 Samuel 16 in the GGMNT

2 Samuel 16 in the GNT

2 Samuel 16 in the HARY

2 Samuel 16 in the HNT

2 Samuel 16 in the IRVA

2 Samuel 16 in the IRVB

2 Samuel 16 in the IRVG

2 Samuel 16 in the IRVH

2 Samuel 16 in the IRVK

2 Samuel 16 in the IRVM

2 Samuel 16 in the IRVM2

2 Samuel 16 in the IRVO

2 Samuel 16 in the IRVP

2 Samuel 16 in the IRVT

2 Samuel 16 in the IRVT2

2 Samuel 16 in the IRVU

2 Samuel 16 in the ISVN

2 Samuel 16 in the JSNT

2 Samuel 16 in the KAPI

2 Samuel 16 in the KBT1ETNIK

2 Samuel 16 in the KBV

2 Samuel 16 in the KJV

2 Samuel 16 in the KNFD

2 Samuel 16 in the LBA

2 Samuel 16 in the LBLA

2 Samuel 16 in the LNT

2 Samuel 16 in the LSV

2 Samuel 16 in the MAAL

2 Samuel 16 in the MBV

2 Samuel 16 in the MBV2

2 Samuel 16 in the MHNT

2 Samuel 16 in the MKNFD

2 Samuel 16 in the MNG

2 Samuel 16 in the MNT

2 Samuel 16 in the MNT2

2 Samuel 16 in the MRS1T

2 Samuel 16 in the NAA

2 Samuel 16 in the NASB

2 Samuel 16 in the NBLA

2 Samuel 16 in the NBS

2 Samuel 16 in the NBVTP

2 Samuel 16 in the NET2

2 Samuel 16 in the NIV11

2 Samuel 16 in the NNT

2 Samuel 16 in the NNT2

2 Samuel 16 in the NNT3

2 Samuel 16 in the PDDPT

2 Samuel 16 in the PFNT

2 Samuel 16 in the RMNT

2 Samuel 16 in the SBIAS

2 Samuel 16 in the SBIBS

2 Samuel 16 in the SBIBS2

2 Samuel 16 in the SBICS

2 Samuel 16 in the SBIDS

2 Samuel 16 in the SBIGS

2 Samuel 16 in the SBIHS

2 Samuel 16 in the SBIIS

2 Samuel 16 in the SBIIS2

2 Samuel 16 in the SBIIS3

2 Samuel 16 in the SBIKS

2 Samuel 16 in the SBIKS2

2 Samuel 16 in the SBIMS

2 Samuel 16 in the SBIOS

2 Samuel 16 in the SBIPS

2 Samuel 16 in the SBISS

2 Samuel 16 in the SBITS

2 Samuel 16 in the SBITS2

2 Samuel 16 in the SBITS3

2 Samuel 16 in the SBITS4

2 Samuel 16 in the SBIUS

2 Samuel 16 in the SBIVS

2 Samuel 16 in the SBT

2 Samuel 16 in the SBT1E

2 Samuel 16 in the SCHL

2 Samuel 16 in the SNT

2 Samuel 16 in the SUSU

2 Samuel 16 in the SUSU2

2 Samuel 16 in the SYNO

2 Samuel 16 in the TBIAOTANT

2 Samuel 16 in the TBT1E

2 Samuel 16 in the TBT1E2

2 Samuel 16 in the TFTIP

2 Samuel 16 in the TFTU

2 Samuel 16 in the TGNTATF3T

2 Samuel 16 in the THAI

2 Samuel 16 in the TNFD

2 Samuel 16 in the TNT

2 Samuel 16 in the TNTIK

2 Samuel 16 in the TNTIL

2 Samuel 16 in the TNTIN

2 Samuel 16 in the TNTIP

2 Samuel 16 in the TNTIZ

2 Samuel 16 in the TOMA

2 Samuel 16 in the TTENT

2 Samuel 16 in the UBG

2 Samuel 16 in the UGV

2 Samuel 16 in the UGV2

2 Samuel 16 in the UGV3

2 Samuel 16 in the VBL

2 Samuel 16 in the VDCC

2 Samuel 16 in the YALU

2 Samuel 16 in the YAPE

2 Samuel 16 in the YBVTP

2 Samuel 16 in the ZBP