Colossians 2 (BOGWICC)

1 Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso. 2 Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu. 3 Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso. 4 Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake. 5 Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu. 6 Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. 7 Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire. 8 Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu. 9 Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu. 10 Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse. 11 Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija. 12 Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa. 13 Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. 14 Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda. 15 Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda. 16 Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata. 17 Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu. 18 Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu. 19 Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire. 20 Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa: 21 “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?” 22 Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe. 23 Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.

In Other Versions

Colossians 2 in the ANGEFD

Colossians 2 in the ANTPNG2D

Colossians 2 in the AS21

Colossians 2 in the BAGH

Colossians 2 in the BBPNG

Colossians 2 in the BBT1E

Colossians 2 in the BDS

Colossians 2 in the BEV

Colossians 2 in the BHAD

Colossians 2 in the BIB

Colossians 2 in the BLPT

Colossians 2 in the BNT

Colossians 2 in the BNTABOOT

Colossians 2 in the BNTLV

Colossians 2 in the BOATCB

Colossians 2 in the BOATCB2

Colossians 2 in the BOBCV

Colossians 2 in the BOCNT

Colossians 2 in the BOECS

Colossians 2 in the BOHCB

Colossians 2 in the BOHCV

Colossians 2 in the BOHLNT

Colossians 2 in the BOHNTLTAL

Colossians 2 in the BOICB

Colossians 2 in the BOILNTAP

Colossians 2 in the BOITCV

Colossians 2 in the BOKCV

Colossians 2 in the BOKCV2

Colossians 2 in the BOKHWOG

Colossians 2 in the BOKSSV

Colossians 2 in the BOLCB

Colossians 2 in the BOLCB2

Colossians 2 in the BOMCV

Colossians 2 in the BONAV

Colossians 2 in the BONCB

Colossians 2 in the BONLT

Colossians 2 in the BONUT2

Colossians 2 in the BOPLNT

Colossians 2 in the BOSCB

Colossians 2 in the BOSNC

Colossians 2 in the BOTLNT

Colossians 2 in the BOVCB

Colossians 2 in the BOYCB

Colossians 2 in the BPBB

Colossians 2 in the BPH

Colossians 2 in the BSB

Colossians 2 in the CCB

Colossians 2 in the CUV

Colossians 2 in the CUVS

Colossians 2 in the DBT

Colossians 2 in the DGDNT

Colossians 2 in the DHNT

Colossians 2 in the DNT

Colossians 2 in the ELBE

Colossians 2 in the EMTV

Colossians 2 in the ESV

Colossians 2 in the FBV

Colossians 2 in the FEB

Colossians 2 in the GGMNT

Colossians 2 in the GNT

Colossians 2 in the HARY

Colossians 2 in the HNT

Colossians 2 in the IRVA

Colossians 2 in the IRVB

Colossians 2 in the IRVG

Colossians 2 in the IRVH

Colossians 2 in the IRVK

Colossians 2 in the IRVM

Colossians 2 in the IRVM2

Colossians 2 in the IRVO

Colossians 2 in the IRVP

Colossians 2 in the IRVT

Colossians 2 in the IRVT2

Colossians 2 in the IRVU

Colossians 2 in the ISVN

Colossians 2 in the JSNT

Colossians 2 in the KAPI

Colossians 2 in the KBT1ETNIK

Colossians 2 in the KBV

Colossians 2 in the KJV

Colossians 2 in the KNFD

Colossians 2 in the LBA

Colossians 2 in the LBLA

Colossians 2 in the LNT

Colossians 2 in the LSV

Colossians 2 in the MAAL

Colossians 2 in the MBV

Colossians 2 in the MBV2

Colossians 2 in the MHNT

Colossians 2 in the MKNFD

Colossians 2 in the MNG

Colossians 2 in the MNT

Colossians 2 in the MNT2

Colossians 2 in the MRS1T

Colossians 2 in the NAA

Colossians 2 in the NASB

Colossians 2 in the NBLA

Colossians 2 in the NBS

Colossians 2 in the NBVTP

Colossians 2 in the NET2

Colossians 2 in the NIV11

Colossians 2 in the NNT

Colossians 2 in the NNT2

Colossians 2 in the NNT3

Colossians 2 in the PDDPT

Colossians 2 in the PFNT

Colossians 2 in the RMNT

Colossians 2 in the SBIAS

Colossians 2 in the SBIBS

Colossians 2 in the SBIBS2

Colossians 2 in the SBICS

Colossians 2 in the SBIDS

Colossians 2 in the SBIGS

Colossians 2 in the SBIHS

Colossians 2 in the SBIIS

Colossians 2 in the SBIIS2

Colossians 2 in the SBIIS3

Colossians 2 in the SBIKS

Colossians 2 in the SBIKS2

Colossians 2 in the SBIMS

Colossians 2 in the SBIOS

Colossians 2 in the SBIPS

Colossians 2 in the SBISS

Colossians 2 in the SBITS

Colossians 2 in the SBITS2

Colossians 2 in the SBITS3

Colossians 2 in the SBITS4

Colossians 2 in the SBIUS

Colossians 2 in the SBIVS

Colossians 2 in the SBT

Colossians 2 in the SBT1E

Colossians 2 in the SCHL

Colossians 2 in the SNT

Colossians 2 in the SUSU

Colossians 2 in the SUSU2

Colossians 2 in the SYNO

Colossians 2 in the TBIAOTANT

Colossians 2 in the TBT1E

Colossians 2 in the TBT1E2

Colossians 2 in the TFTIP

Colossians 2 in the TFTU

Colossians 2 in the TGNTATF3T

Colossians 2 in the THAI

Colossians 2 in the TNFD

Colossians 2 in the TNT

Colossians 2 in the TNTIK

Colossians 2 in the TNTIL

Colossians 2 in the TNTIN

Colossians 2 in the TNTIP

Colossians 2 in the TNTIZ

Colossians 2 in the TOMA

Colossians 2 in the TTENT

Colossians 2 in the UBG

Colossians 2 in the UGV

Colossians 2 in the UGV2

Colossians 2 in the UGV3

Colossians 2 in the VBL

Colossians 2 in the VDCC

Colossians 2 in the YALU

Colossians 2 in the YAPE

Colossians 2 in the YBVTP

Colossians 2 in the ZBP