Deuteronomy 11 (BOGWICC)

1 Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndipo nthawi zonse muzitsata zimene Iyeyo anakulamulani, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo ake. 2 Lero kumbukirani kuti si ana anu amene anaona ndi kulawa chilango cha Yehova Mulungu wanu: ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, mkono wake wotambasuka; 3 zizindikiro zozizwitsa zimene anazionetsa ndi zinthu zimene anazichita mʼkati mwa Igupto, Farao mfumu ya Igupto ndi kwa dziko lake lonse; 4 zimene Iye anachita kwa gulu lankhondo la Aigupto, kwa akavalo ndi magaleta awo, mmene Iye anawamizira ndi madzi a mu Nyanja Yofiira pamene amakuthamangitsani, ndi mmene Yehova anawagonjetsera kufikira lero. 5 Si ana anu amene anaona zimene Iye anakuchitirani mʼchipululu kufikira pamene munafika pa malo anu, 6 ndi zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu mwana wa Rubeni, pamene nthaka inatsekula pakamwa pake pakati pa Aisraeli onse ndi kuwameza pamodzi ndi katundu wawo, matenti awo ndi chilichonse chawo. 7 Koma ndinuyo amene munaona ntchito zonse zikuluzikulu zimenezi Yehova anakuchitirani. 8 Tsono muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lero kuti mukhale ndi mphamvu ndi kuti mupite kukalanda mʼdziko limene mwakhala pangʼono kulowamo mukawoloka Yorodani, 9 ndiponso kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu ndi zidzukulu zawo, lomwe ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi. 10 Dziko limene mukukalanda ndi kulowamo silokhala ngati dziko la ku Igupto kumene mukuchokera ayi, kuja mumadzala mbewu ndi kumathirira ndi mapazi anu ngati ku dimba. 11 Koma dziko limene mukalande mukawoloka Yorodani ndi dziko la mapiri ndi zigwa, dziko limene limalandira mvula kuchokera kumwamba. 12 Ili ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu amalisamalira. Maso a Yehova Mulungu wanu amaliyangʼanira nthawi zonse kuchokera ku mayambiriro a chaka mpaka kumapeto kwake. 13 Choncho mukasunga mokhulupirika malamulo amene ndikukupatsani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iyeyo ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, 14 pamenepo ndidzatumiza mvula mʼdziko mwanu pa nthawi yake mʼnyengo ya dzinja ndi chilimwe, kuti mudzakolole tirigu wambiri ndi kuti mudzakhale ndi vinyo watsopano ndi mafuta. 15 Ndidzakupatsani udzu mʼminda mwanu woti muzidzadyetsera ngʼombe zanu ndipo inuyo mudzadya ndi kukhuta. 16 Dzisamalireni nokha, kuopa kuti mungakopeke mtima ndi kubwerera mʼmbuyo kuyamba kutumikira milungu ina ndi kumayigwadira. 17 Mukatero Yehova Mulungu wanu adzakukwiyirani kwambiri, nadzaletsa thambo kuti lisabweretsenso mvula ndipo dziko silidzapereka zokolola. Choncho mudzawonongeka msanga mʼdziko limene Yehova akukupatsani. 18 Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu. 19 Mawuwa muziphunzitsa ana anu, muzikamba za iwo pamene mukhala pansi mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mugona ndi pamene mukudzuka. 20 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu, 21 kuti inu ndi ana anu mukhale mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu mpaka kalekale monga umakhalira mlengalenga pamwamba pa dziko. 22 Mukatsatira mosamalitsa malamulo amene ndikukupatsaniwa, kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira zake zonse ndi kumugwiritsitsa Iye 23 Yehova adzapirikitsa mitundu ina yonseyi inu musanafike ndipo mudzagonjetsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inu. 24 Malo aliwonse amene mudzaponda adzakhala anu: dziko lanu lidzachokera ku chipululu mpaka ku Lebanoni, ndi ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku nyanja ya kumadzulo. 25 Palibe munthu amene adzalimbana nanu. Monga analonjezera, Yehova adzachititsa kuti anthu onse mʼdziko limene mukupitalo adzachite nanu mantha ndi kukuopani. 26 Taonani, lero ndikuyika dalitso ndi temberero pakati panu, 27 dalitso ngati mumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero. 28 Temberero ngati simumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu ndi kupatuka pa njira imene ndikulamulirani lero potsata milungu ina imene simunayidziwe. 29 Yehova Mulungu wanu akakakufikitsani mʼdziko mukukalandalo kuti mulowemo mukanene za madalitso pa Phiri la Gerizimu, ndi za matemberero pa Phiri la Ebala. 30 Monga mudziwa, mapiriwa ali kutsidya kwa Yorodani, kumadzulo kolowera dzuwa, kufupi ndi mitengo ya thundu ya More, mʼdziko la Akanaani aja okhala ku Araba moyangʼanana ndi Giligala. 31 Mwatsala pangʼono kuwoloka Yorodani kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukadzalitenga dzikolo ndi kukhalamo, 32 mudzaonetsetse kuti mukumvera malangizo ndi malamulo amene ndikukuwuzani lero.

In Other Versions

Deuteronomy 11 in the ANGEFD

Deuteronomy 11 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 11 in the AS21

Deuteronomy 11 in the BAGH

Deuteronomy 11 in the BBPNG

Deuteronomy 11 in the BBT1E

Deuteronomy 11 in the BDS

Deuteronomy 11 in the BEV

Deuteronomy 11 in the BHAD

Deuteronomy 11 in the BIB

Deuteronomy 11 in the BLPT

Deuteronomy 11 in the BNT

Deuteronomy 11 in the BNTABOOT

Deuteronomy 11 in the BNTLV

Deuteronomy 11 in the BOATCB

Deuteronomy 11 in the BOATCB2

Deuteronomy 11 in the BOBCV

Deuteronomy 11 in the BOCNT

Deuteronomy 11 in the BOECS

Deuteronomy 11 in the BOHCB

Deuteronomy 11 in the BOHCV

Deuteronomy 11 in the BOHLNT

Deuteronomy 11 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 11 in the BOICB

Deuteronomy 11 in the BOILNTAP

Deuteronomy 11 in the BOITCV

Deuteronomy 11 in the BOKCV

Deuteronomy 11 in the BOKCV2

Deuteronomy 11 in the BOKHWOG

Deuteronomy 11 in the BOKSSV

Deuteronomy 11 in the BOLCB

Deuteronomy 11 in the BOLCB2

Deuteronomy 11 in the BOMCV

Deuteronomy 11 in the BONAV

Deuteronomy 11 in the BONCB

Deuteronomy 11 in the BONLT

Deuteronomy 11 in the BONUT2

Deuteronomy 11 in the BOPLNT

Deuteronomy 11 in the BOSCB

Deuteronomy 11 in the BOSNC

Deuteronomy 11 in the BOTLNT

Deuteronomy 11 in the BOVCB

Deuteronomy 11 in the BOYCB

Deuteronomy 11 in the BPBB

Deuteronomy 11 in the BPH

Deuteronomy 11 in the BSB

Deuteronomy 11 in the CCB

Deuteronomy 11 in the CUV

Deuteronomy 11 in the CUVS

Deuteronomy 11 in the DBT

Deuteronomy 11 in the DGDNT

Deuteronomy 11 in the DHNT

Deuteronomy 11 in the DNT

Deuteronomy 11 in the ELBE

Deuteronomy 11 in the EMTV

Deuteronomy 11 in the ESV

Deuteronomy 11 in the FBV

Deuteronomy 11 in the FEB

Deuteronomy 11 in the GGMNT

Deuteronomy 11 in the GNT

Deuteronomy 11 in the HARY

Deuteronomy 11 in the HNT

Deuteronomy 11 in the IRVA

Deuteronomy 11 in the IRVB

Deuteronomy 11 in the IRVG

Deuteronomy 11 in the IRVH

Deuteronomy 11 in the IRVK

Deuteronomy 11 in the IRVM

Deuteronomy 11 in the IRVM2

Deuteronomy 11 in the IRVO

Deuteronomy 11 in the IRVP

Deuteronomy 11 in the IRVT

Deuteronomy 11 in the IRVT2

Deuteronomy 11 in the IRVU

Deuteronomy 11 in the ISVN

Deuteronomy 11 in the JSNT

Deuteronomy 11 in the KAPI

Deuteronomy 11 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 11 in the KBV

Deuteronomy 11 in the KJV

Deuteronomy 11 in the KNFD

Deuteronomy 11 in the LBA

Deuteronomy 11 in the LBLA

Deuteronomy 11 in the LNT

Deuteronomy 11 in the LSV

Deuteronomy 11 in the MAAL

Deuteronomy 11 in the MBV

Deuteronomy 11 in the MBV2

Deuteronomy 11 in the MHNT

Deuteronomy 11 in the MKNFD

Deuteronomy 11 in the MNG

Deuteronomy 11 in the MNT

Deuteronomy 11 in the MNT2

Deuteronomy 11 in the MRS1T

Deuteronomy 11 in the NAA

Deuteronomy 11 in the NASB

Deuteronomy 11 in the NBLA

Deuteronomy 11 in the NBS

Deuteronomy 11 in the NBVTP

Deuteronomy 11 in the NET2

Deuteronomy 11 in the NIV11

Deuteronomy 11 in the NNT

Deuteronomy 11 in the NNT2

Deuteronomy 11 in the NNT3

Deuteronomy 11 in the PDDPT

Deuteronomy 11 in the PFNT

Deuteronomy 11 in the RMNT

Deuteronomy 11 in the SBIAS

Deuteronomy 11 in the SBIBS

Deuteronomy 11 in the SBIBS2

Deuteronomy 11 in the SBICS

Deuteronomy 11 in the SBIDS

Deuteronomy 11 in the SBIGS

Deuteronomy 11 in the SBIHS

Deuteronomy 11 in the SBIIS

Deuteronomy 11 in the SBIIS2

Deuteronomy 11 in the SBIIS3

Deuteronomy 11 in the SBIKS

Deuteronomy 11 in the SBIKS2

Deuteronomy 11 in the SBIMS

Deuteronomy 11 in the SBIOS

Deuteronomy 11 in the SBIPS

Deuteronomy 11 in the SBISS

Deuteronomy 11 in the SBITS

Deuteronomy 11 in the SBITS2

Deuteronomy 11 in the SBITS3

Deuteronomy 11 in the SBITS4

Deuteronomy 11 in the SBIUS

Deuteronomy 11 in the SBIVS

Deuteronomy 11 in the SBT

Deuteronomy 11 in the SBT1E

Deuteronomy 11 in the SCHL

Deuteronomy 11 in the SNT

Deuteronomy 11 in the SUSU

Deuteronomy 11 in the SUSU2

Deuteronomy 11 in the SYNO

Deuteronomy 11 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 11 in the TBT1E

Deuteronomy 11 in the TBT1E2

Deuteronomy 11 in the TFTIP

Deuteronomy 11 in the TFTU

Deuteronomy 11 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 11 in the THAI

Deuteronomy 11 in the TNFD

Deuteronomy 11 in the TNT

Deuteronomy 11 in the TNTIK

Deuteronomy 11 in the TNTIL

Deuteronomy 11 in the TNTIN

Deuteronomy 11 in the TNTIP

Deuteronomy 11 in the TNTIZ

Deuteronomy 11 in the TOMA

Deuteronomy 11 in the TTENT

Deuteronomy 11 in the UBG

Deuteronomy 11 in the UGV

Deuteronomy 11 in the UGV2

Deuteronomy 11 in the UGV3

Deuteronomy 11 in the VBL

Deuteronomy 11 in the VDCC

Deuteronomy 11 in the YALU

Deuteronomy 11 in the YAPE

Deuteronomy 11 in the YBVTP

Deuteronomy 11 in the ZBP