Deuteronomy 16 (BOGWICC)

1 Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto. 2 Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake. 3 Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto. 4 Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa. 5 Musamangopereka nsembe ya Paska mu mzinda wina uliwonse umene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, 6 koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto. 7 Muyiwotche ndi kuyidya pa malo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Kenaka mmawa mubwerere ku matenti anu. 8 Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse. 9 Muziwerenga masabata asanu ndi awiri kuyambira pamene mwatenga chikwakwa ndi kuyamba kumweta tirigu wachilili. 10 Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani 11 Ndipo inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi a mʼmizinda mwanu, alendo, ana ndi akazi amasiye okhala pakati panu, mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku malo amene adzawasankhe kukhazikitsako dzina lake. 12 Kumbukirani kuti inunso munali akapolo ku Igupto, ndiye muzitsatira malangizo awa mosamalitsa. 13 Mukatha kukolola tirigu wanu ndi kupsinya vinyo wanu, muzikhala ndi Chikondwerero cha Misasa kwa masiku asanu ndi awiri. 14 Musangalale pa chikondwerero chanu, inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi, alendo, ana ndi akazi amasiye amene ali mʼmizinda yanu. 15 Kwa masiku asanu ndi awiri muzichita chikondwererochi kwa Yehova Mulungu wanu kumalo kumene Yehova adzasankhe. Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani inu pa zokolola zanu ndi pa ntchito za manja anu, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu. 16 Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake. 17 Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani. 18 Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo. 19 Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. 20 Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 21 Musazike mtengo wina uliwonse wa mafano a Asera pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, 22 ndipo musayimike mwala wachipembedzo pakuti Yehova Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.

In Other Versions

Deuteronomy 16 in the ANGEFD

Deuteronomy 16 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 16 in the AS21

Deuteronomy 16 in the BAGH

Deuteronomy 16 in the BBPNG

Deuteronomy 16 in the BBT1E

Deuteronomy 16 in the BDS

Deuteronomy 16 in the BEV

Deuteronomy 16 in the BHAD

Deuteronomy 16 in the BIB

Deuteronomy 16 in the BLPT

Deuteronomy 16 in the BNT

Deuteronomy 16 in the BNTABOOT

Deuteronomy 16 in the BNTLV

Deuteronomy 16 in the BOATCB

Deuteronomy 16 in the BOATCB2

Deuteronomy 16 in the BOBCV

Deuteronomy 16 in the BOCNT

Deuteronomy 16 in the BOECS

Deuteronomy 16 in the BOHCB

Deuteronomy 16 in the BOHCV

Deuteronomy 16 in the BOHLNT

Deuteronomy 16 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 16 in the BOICB

Deuteronomy 16 in the BOILNTAP

Deuteronomy 16 in the BOITCV

Deuteronomy 16 in the BOKCV

Deuteronomy 16 in the BOKCV2

Deuteronomy 16 in the BOKHWOG

Deuteronomy 16 in the BOKSSV

Deuteronomy 16 in the BOLCB

Deuteronomy 16 in the BOLCB2

Deuteronomy 16 in the BOMCV

Deuteronomy 16 in the BONAV

Deuteronomy 16 in the BONCB

Deuteronomy 16 in the BONLT

Deuteronomy 16 in the BONUT2

Deuteronomy 16 in the BOPLNT

Deuteronomy 16 in the BOSCB

Deuteronomy 16 in the BOSNC

Deuteronomy 16 in the BOTLNT

Deuteronomy 16 in the BOVCB

Deuteronomy 16 in the BOYCB

Deuteronomy 16 in the BPBB

Deuteronomy 16 in the BPH

Deuteronomy 16 in the BSB

Deuteronomy 16 in the CCB

Deuteronomy 16 in the CUV

Deuteronomy 16 in the CUVS

Deuteronomy 16 in the DBT

Deuteronomy 16 in the DGDNT

Deuteronomy 16 in the DHNT

Deuteronomy 16 in the DNT

Deuteronomy 16 in the ELBE

Deuteronomy 16 in the EMTV

Deuteronomy 16 in the ESV

Deuteronomy 16 in the FBV

Deuteronomy 16 in the FEB

Deuteronomy 16 in the GGMNT

Deuteronomy 16 in the GNT

Deuteronomy 16 in the HARY

Deuteronomy 16 in the HNT

Deuteronomy 16 in the IRVA

Deuteronomy 16 in the IRVB

Deuteronomy 16 in the IRVG

Deuteronomy 16 in the IRVH

Deuteronomy 16 in the IRVK

Deuteronomy 16 in the IRVM

Deuteronomy 16 in the IRVM2

Deuteronomy 16 in the IRVO

Deuteronomy 16 in the IRVP

Deuteronomy 16 in the IRVT

Deuteronomy 16 in the IRVT2

Deuteronomy 16 in the IRVU

Deuteronomy 16 in the ISVN

Deuteronomy 16 in the JSNT

Deuteronomy 16 in the KAPI

Deuteronomy 16 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 16 in the KBV

Deuteronomy 16 in the KJV

Deuteronomy 16 in the KNFD

Deuteronomy 16 in the LBA

Deuteronomy 16 in the LBLA

Deuteronomy 16 in the LNT

Deuteronomy 16 in the LSV

Deuteronomy 16 in the MAAL

Deuteronomy 16 in the MBV

Deuteronomy 16 in the MBV2

Deuteronomy 16 in the MHNT

Deuteronomy 16 in the MKNFD

Deuteronomy 16 in the MNG

Deuteronomy 16 in the MNT

Deuteronomy 16 in the MNT2

Deuteronomy 16 in the MRS1T

Deuteronomy 16 in the NAA

Deuteronomy 16 in the NASB

Deuteronomy 16 in the NBLA

Deuteronomy 16 in the NBS

Deuteronomy 16 in the NBVTP

Deuteronomy 16 in the NET2

Deuteronomy 16 in the NIV11

Deuteronomy 16 in the NNT

Deuteronomy 16 in the NNT2

Deuteronomy 16 in the NNT3

Deuteronomy 16 in the PDDPT

Deuteronomy 16 in the PFNT

Deuteronomy 16 in the RMNT

Deuteronomy 16 in the SBIAS

Deuteronomy 16 in the SBIBS

Deuteronomy 16 in the SBIBS2

Deuteronomy 16 in the SBICS

Deuteronomy 16 in the SBIDS

Deuteronomy 16 in the SBIGS

Deuteronomy 16 in the SBIHS

Deuteronomy 16 in the SBIIS

Deuteronomy 16 in the SBIIS2

Deuteronomy 16 in the SBIIS3

Deuteronomy 16 in the SBIKS

Deuteronomy 16 in the SBIKS2

Deuteronomy 16 in the SBIMS

Deuteronomy 16 in the SBIOS

Deuteronomy 16 in the SBIPS

Deuteronomy 16 in the SBISS

Deuteronomy 16 in the SBITS

Deuteronomy 16 in the SBITS2

Deuteronomy 16 in the SBITS3

Deuteronomy 16 in the SBITS4

Deuteronomy 16 in the SBIUS

Deuteronomy 16 in the SBIVS

Deuteronomy 16 in the SBT

Deuteronomy 16 in the SBT1E

Deuteronomy 16 in the SCHL

Deuteronomy 16 in the SNT

Deuteronomy 16 in the SUSU

Deuteronomy 16 in the SUSU2

Deuteronomy 16 in the SYNO

Deuteronomy 16 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 16 in the TBT1E

Deuteronomy 16 in the TBT1E2

Deuteronomy 16 in the TFTIP

Deuteronomy 16 in the TFTU

Deuteronomy 16 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 16 in the THAI

Deuteronomy 16 in the TNFD

Deuteronomy 16 in the TNT

Deuteronomy 16 in the TNTIK

Deuteronomy 16 in the TNTIL

Deuteronomy 16 in the TNTIN

Deuteronomy 16 in the TNTIP

Deuteronomy 16 in the TNTIZ

Deuteronomy 16 in the TOMA

Deuteronomy 16 in the TTENT

Deuteronomy 16 in the UBG

Deuteronomy 16 in the UGV

Deuteronomy 16 in the UGV2

Deuteronomy 16 in the UGV3

Deuteronomy 16 in the VBL

Deuteronomy 16 in the VDCC

Deuteronomy 16 in the YALU

Deuteronomy 16 in the YAPE

Deuteronomy 16 in the YBVTP

Deuteronomy 16 in the ZBP