Deuteronomy 17 (BOGWICC)
1 Musapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena cholakwika chilichonse, pakuti zimenezi zimamunyansa. 2 Ngati mwamuna kapena mkazi pakati panu, mʼmizinda imene Yehova akukupatsani apezeka akuchita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu pophwanya pangano lake, 3 ndipo ngati motsutsana ndi lamulo langa wapembedza milungu ina, kuyigwadira milunguyo, kaya ndi dzuwa kapena mwezi kapena nyenyezi zakumwamba, 4 ndipo inu nʼkuwuzidwa zimenezi, mufufuze bwinobwino. Ngati ndi zoona, ndipo ngati zatsimikizika kuti chonyansa choterechi chachitikadi mu Israeli, 5 mumutengere mwamuna kapena mkazi amene wachita chonyansa choterechi ku chipata cha mzinda wanu ndi kumupha pomugenda miyala. 6 Munthu aziphedwa pakakhala mboni ziwiri kapena zitatu koma osati mboni imodzi yokha ayi. 7 Wochitira umboniwo ndiwo aziyamba kumupha munthuyo, ndipo kenaka anthu onse. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu. 8 Ngati akubweretserani milandu mʼmabwalo anu imene ili yovuta kuweruza kaya ndi yokhetsa magazi, kaya ndi yophwanyirana ufulu, kaya ndi yovulazana, muyitengere kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. 9 Mudzapite kwa ansembe Alevi ndi kwa woweruza wa pa nthawi imeneyo. Kawafunseni ndipo iwowo adzakuwuzani zoyenera kuchita. 10 Kachiteni zimene adzakuwuzenizo kuchokera ku malo amene Yehova adzasankhe. Kaonetsetseni kuti mukutsatira zonse zimene akuwuzanizo. 11 Kachiteni motsatira malamulo ndi malangizo amene adzakuwuzeni; osawanyoza, potembenukira kumanja kapena kumanzere. 12 Munthu aliyense amene adzanyoza woweruza kapena wansembe amene akutumikira kumeneko mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu, aphedwe ndithu. Muzichotsa choyipa pakati pa Israeli. 13 Anthu onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha, choncho sadzadzikuzanso. 14 Mukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge, ndipo mukakakhazikika mʼmenemo nimunena kuti, “Tiyeni tisankhe mfumu yoti izitilamulira monga imachitira mitundu yonse yotizungulirayi,” 15 mudzakhazikitse mfumu yoti izikakulamulirani, mfumu imene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati panu. Mudzasankhe mfumuyo kuchokera pakati pa abale anu. Osasankha mlendo, munthu amene sachokera pakati pa abale anu Aisraeli. 16 Komatu mfumuyo isadzikundikire akavalo, kapena kutuma anthu kupita ku Igupto kukayipezera akavalo ena, pakuti Ambuye akuti, “Simuyenera kubweranso ku Igupto mʼnjira yomweyo.” 17 Asadziwunjikire akazi kuopa kuti mtima wake ungamusocheretse. Asadziwunjikirenso golide ndi siliva wambiri. 18 Akakhala pa mpando waufumuwo, ayenera kulemba za iye mwini mʼbuku la malamuloli, kuchokera kwa ansembe Alevi. 19 Asunge zimene walembazo ndipo ayenera kumaziwerenga masiku onse a moyo wake, kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake posunga mosamalitsa malamulo ndi malangizowa. 20 Asadzione kuti iyeyo ndi wopambana kuposa abale ake, nalekeratu kutsatira malamulo. Akasamala zimenezi iye ndi ana ake adzalamulira ufumu wa Israeli kwa nthawi yayitali.
In Other Versions
Deuteronomy 17 in the ANGEFD
Deuteronomy 17 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 17 in the AS21
Deuteronomy 17 in the BAGH
Deuteronomy 17 in the BBPNG
Deuteronomy 17 in the BBT1E
Deuteronomy 17 in the BDS
Deuteronomy 17 in the BEV
Deuteronomy 17 in the BHAD
Deuteronomy 17 in the BIB
Deuteronomy 17 in the BLPT
Deuteronomy 17 in the BNT
Deuteronomy 17 in the BNTABOOT
Deuteronomy 17 in the BNTLV
Deuteronomy 17 in the BOATCB
Deuteronomy 17 in the BOATCB2
Deuteronomy 17 in the BOBCV
Deuteronomy 17 in the BOCNT
Deuteronomy 17 in the BOECS
Deuteronomy 17 in the BOHCB
Deuteronomy 17 in the BOHCV
Deuteronomy 17 in the BOHLNT
Deuteronomy 17 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 17 in the BOICB
Deuteronomy 17 in the BOILNTAP
Deuteronomy 17 in the BOITCV
Deuteronomy 17 in the BOKCV
Deuteronomy 17 in the BOKCV2
Deuteronomy 17 in the BOKHWOG
Deuteronomy 17 in the BOKSSV
Deuteronomy 17 in the BOLCB
Deuteronomy 17 in the BOLCB2
Deuteronomy 17 in the BOMCV
Deuteronomy 17 in the BONAV
Deuteronomy 17 in the BONCB
Deuteronomy 17 in the BONLT
Deuteronomy 17 in the BONUT2
Deuteronomy 17 in the BOPLNT
Deuteronomy 17 in the BOSCB
Deuteronomy 17 in the BOSNC
Deuteronomy 17 in the BOTLNT
Deuteronomy 17 in the BOVCB
Deuteronomy 17 in the BOYCB
Deuteronomy 17 in the BPBB
Deuteronomy 17 in the BPH
Deuteronomy 17 in the BSB
Deuteronomy 17 in the CCB
Deuteronomy 17 in the CUV
Deuteronomy 17 in the CUVS
Deuteronomy 17 in the DBT
Deuteronomy 17 in the DGDNT
Deuteronomy 17 in the DHNT
Deuteronomy 17 in the DNT
Deuteronomy 17 in the ELBE
Deuteronomy 17 in the EMTV
Deuteronomy 17 in the ESV
Deuteronomy 17 in the FBV
Deuteronomy 17 in the FEB
Deuteronomy 17 in the GGMNT
Deuteronomy 17 in the GNT
Deuteronomy 17 in the HARY
Deuteronomy 17 in the HNT
Deuteronomy 17 in the IRVA
Deuteronomy 17 in the IRVB
Deuteronomy 17 in the IRVG
Deuteronomy 17 in the IRVH
Deuteronomy 17 in the IRVK
Deuteronomy 17 in the IRVM
Deuteronomy 17 in the IRVM2
Deuteronomy 17 in the IRVO
Deuteronomy 17 in the IRVP
Deuteronomy 17 in the IRVT
Deuteronomy 17 in the IRVT2
Deuteronomy 17 in the IRVU
Deuteronomy 17 in the ISVN
Deuteronomy 17 in the JSNT
Deuteronomy 17 in the KAPI
Deuteronomy 17 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 17 in the KBV
Deuteronomy 17 in the KJV
Deuteronomy 17 in the KNFD
Deuteronomy 17 in the LBA
Deuteronomy 17 in the LBLA
Deuteronomy 17 in the LNT
Deuteronomy 17 in the LSV
Deuteronomy 17 in the MAAL
Deuteronomy 17 in the MBV
Deuteronomy 17 in the MBV2
Deuteronomy 17 in the MHNT
Deuteronomy 17 in the MKNFD
Deuteronomy 17 in the MNG
Deuteronomy 17 in the MNT
Deuteronomy 17 in the MNT2
Deuteronomy 17 in the MRS1T
Deuteronomy 17 in the NAA
Deuteronomy 17 in the NASB
Deuteronomy 17 in the NBLA
Deuteronomy 17 in the NBS
Deuteronomy 17 in the NBVTP
Deuteronomy 17 in the NET2
Deuteronomy 17 in the NIV11
Deuteronomy 17 in the NNT
Deuteronomy 17 in the NNT2
Deuteronomy 17 in the NNT3
Deuteronomy 17 in the PDDPT
Deuteronomy 17 in the PFNT
Deuteronomy 17 in the RMNT
Deuteronomy 17 in the SBIAS
Deuteronomy 17 in the SBIBS
Deuteronomy 17 in the SBIBS2
Deuteronomy 17 in the SBICS
Deuteronomy 17 in the SBIDS
Deuteronomy 17 in the SBIGS
Deuteronomy 17 in the SBIHS
Deuteronomy 17 in the SBIIS
Deuteronomy 17 in the SBIIS2
Deuteronomy 17 in the SBIIS3
Deuteronomy 17 in the SBIKS
Deuteronomy 17 in the SBIKS2
Deuteronomy 17 in the SBIMS
Deuteronomy 17 in the SBIOS
Deuteronomy 17 in the SBIPS
Deuteronomy 17 in the SBISS
Deuteronomy 17 in the SBITS
Deuteronomy 17 in the SBITS2
Deuteronomy 17 in the SBITS3
Deuteronomy 17 in the SBITS4
Deuteronomy 17 in the SBIUS
Deuteronomy 17 in the SBIVS
Deuteronomy 17 in the SBT
Deuteronomy 17 in the SBT1E
Deuteronomy 17 in the SCHL
Deuteronomy 17 in the SNT
Deuteronomy 17 in the SUSU
Deuteronomy 17 in the SUSU2
Deuteronomy 17 in the SYNO
Deuteronomy 17 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 17 in the TBT1E
Deuteronomy 17 in the TBT1E2
Deuteronomy 17 in the TFTIP
Deuteronomy 17 in the TFTU
Deuteronomy 17 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 17 in the THAI
Deuteronomy 17 in the TNFD
Deuteronomy 17 in the TNT
Deuteronomy 17 in the TNTIK
Deuteronomy 17 in the TNTIL
Deuteronomy 17 in the TNTIN
Deuteronomy 17 in the TNTIP
Deuteronomy 17 in the TNTIZ
Deuteronomy 17 in the TOMA
Deuteronomy 17 in the TTENT
Deuteronomy 17 in the UBG
Deuteronomy 17 in the UGV
Deuteronomy 17 in the UGV2
Deuteronomy 17 in the UGV3
Deuteronomy 17 in the VBL
Deuteronomy 17 in the VDCC
Deuteronomy 17 in the YALU
Deuteronomy 17 in the YAPE
Deuteronomy 17 in the YBVTP
Deuteronomy 17 in the ZBP