Deuteronomy 23 (BOGWICC)
1 Mwamuna aliyense wofulidwa kapena woduka chiwalo chachimuna asalowe nawo mu msonkhano wa Yehova. 2 Aliyense wobadwa mʼbanja losavomerezeka, kapena mdzukulu wake wina aliyense, ngakhale mibado khumi pambuyo pake, asalowe mu msonkhano wa Yehova. 3 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe mu msonkhano wa anthu a Yehova ngakhale mibado khumi yobwera pambuyo pake. 4 Pakuti iwowa sanabwere kudzakulonjerani ndi chakudya kapena madzi pamene mumadutsa pochokera ku Igupto, mʼmalo mwake anakalemba ganyu Balaamu mwana wa Beori wochokera ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni. 5 Komabe Yehova Mulungu wanu sanamvere Balaamu koma anatembenuza temberero kukhala dalitso kwa inu chifukwa Yehova Mulungu wanu amakukondani. 6 Musachite nawo mgwirizano uliwonse wa mtendere pa moyo wanu wonse. 7 Musapeputse Mwedomu pakuti ndi mʼbale wanu ndithu. Musapeputse Mwigupto chifukwa munali alendo mʼdziko lake. 8 Mʼbado wachitatu wa ana awo akhoza kulowa mu msonkhano wa anthu a Yehova. 9 Mukamakhala pa msasa pokonzekera adani anu, musayandikane ndi china chilichonse chodetsedwa. 10 Wina mwa asilikali anu akadziwonongera ndi umuna usiku, ayenera kuchoka pa msasapo ndipo akhale kunja kwa msasa. 11 Koma dzuwa likapendeka ayenera kusamba ndipo polowa dzuwa akhoza kubwerera ku msasa. 12 Mukonze malo kunja kwa msasa kumene mukhoza kukadzithandizirako. 13 Pakati pa zida zanu muzikhala ndi china chokumbira, ndipo pokadzithandiza muzikumba kadzenje ndi kukwirira chimbudzi chanu. 14 Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani. 15 Ngati kapolo wathawa mbuye wake nakabisala kwanu, musamuperekenso kwa mbuye wakeyo. 16 Mumulole akhale pakati panu, paliponse pamene angakonde, mʼmudzi umene angasankhe ndipo musamupondereze. 17 Pasapezeke Mwisraeli wamwamuna kapena wamkazi wochita chiwerewere ku Nyumba ya Mulungu. 18 Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi. 19 Musamalipitse mʼbale wanu chiwongoladzanja, kaya pa ndalama, kapena pa chakudya, kapena pa china chilichonse choti nʼkupereketsa chiwongoladzanja. 20 Mlendo mukhoza kumulipitsa chiwongoladzanja koma osati mʼbale wanu Mwisraeli, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochitika zanu zonse mʼdziko mukulowamoli. 21 Mukalumbira kupereka kanthu kwa Yehova Mulungu wanu, musamachedwetse kupereka, chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakufunsanibe kanthuko ndipo mudzapezeka wochimwa. 22 Koma ngati mupewa kupanga mapangano simudzapezeka ochimwa. 23 Zilizonse zimene mulumbira ndi pakamwa panu muzitsimikiza kuzichita, chifukwa mwalumbira mwaufulu pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi pakamwa panu. 24 Mukalowa mʼmunda wamphesa wa mnzanu mukhoza kudya mphesa mmene mungafunire koma musayike zina mʼdengu mwanu. 25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mʼbale wanu, mukhoza kutengako ngala mʼmanja mwanu, koma osasenga tirigu ndi chikwakwa.
In Other Versions
Deuteronomy 23 in the ANGEFD
Deuteronomy 23 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 23 in the AS21
Deuteronomy 23 in the BAGH
Deuteronomy 23 in the BBPNG
Deuteronomy 23 in the BBT1E
Deuteronomy 23 in the BDS
Deuteronomy 23 in the BEV
Deuteronomy 23 in the BHAD
Deuteronomy 23 in the BIB
Deuteronomy 23 in the BLPT
Deuteronomy 23 in the BNT
Deuteronomy 23 in the BNTABOOT
Deuteronomy 23 in the BNTLV
Deuteronomy 23 in the BOATCB
Deuteronomy 23 in the BOATCB2
Deuteronomy 23 in the BOBCV
Deuteronomy 23 in the BOCNT
Deuteronomy 23 in the BOECS
Deuteronomy 23 in the BOHCB
Deuteronomy 23 in the BOHCV
Deuteronomy 23 in the BOHLNT
Deuteronomy 23 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 23 in the BOICB
Deuteronomy 23 in the BOILNTAP
Deuteronomy 23 in the BOITCV
Deuteronomy 23 in the BOKCV
Deuteronomy 23 in the BOKCV2
Deuteronomy 23 in the BOKHWOG
Deuteronomy 23 in the BOKSSV
Deuteronomy 23 in the BOLCB
Deuteronomy 23 in the BOLCB2
Deuteronomy 23 in the BOMCV
Deuteronomy 23 in the BONAV
Deuteronomy 23 in the BONCB
Deuteronomy 23 in the BONLT
Deuteronomy 23 in the BONUT2
Deuteronomy 23 in the BOPLNT
Deuteronomy 23 in the BOSCB
Deuteronomy 23 in the BOSNC
Deuteronomy 23 in the BOTLNT
Deuteronomy 23 in the BOVCB
Deuteronomy 23 in the BOYCB
Deuteronomy 23 in the BPBB
Deuteronomy 23 in the BPH
Deuteronomy 23 in the BSB
Deuteronomy 23 in the CCB
Deuteronomy 23 in the CUV
Deuteronomy 23 in the CUVS
Deuteronomy 23 in the DBT
Deuteronomy 23 in the DGDNT
Deuteronomy 23 in the DHNT
Deuteronomy 23 in the DNT
Deuteronomy 23 in the ELBE
Deuteronomy 23 in the EMTV
Deuteronomy 23 in the ESV
Deuteronomy 23 in the FBV
Deuteronomy 23 in the FEB
Deuteronomy 23 in the GGMNT
Deuteronomy 23 in the GNT
Deuteronomy 23 in the HARY
Deuteronomy 23 in the HNT
Deuteronomy 23 in the IRVA
Deuteronomy 23 in the IRVB
Deuteronomy 23 in the IRVG
Deuteronomy 23 in the IRVH
Deuteronomy 23 in the IRVK
Deuteronomy 23 in the IRVM
Deuteronomy 23 in the IRVM2
Deuteronomy 23 in the IRVO
Deuteronomy 23 in the IRVP
Deuteronomy 23 in the IRVT
Deuteronomy 23 in the IRVT2
Deuteronomy 23 in the IRVU
Deuteronomy 23 in the ISVN
Deuteronomy 23 in the JSNT
Deuteronomy 23 in the KAPI
Deuteronomy 23 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 23 in the KBV
Deuteronomy 23 in the KJV
Deuteronomy 23 in the KNFD
Deuteronomy 23 in the LBA
Deuteronomy 23 in the LBLA
Deuteronomy 23 in the LNT
Deuteronomy 23 in the LSV
Deuteronomy 23 in the MAAL
Deuteronomy 23 in the MBV
Deuteronomy 23 in the MBV2
Deuteronomy 23 in the MHNT
Deuteronomy 23 in the MKNFD
Deuteronomy 23 in the MNG
Deuteronomy 23 in the MNT
Deuteronomy 23 in the MNT2
Deuteronomy 23 in the MRS1T
Deuteronomy 23 in the NAA
Deuteronomy 23 in the NASB
Deuteronomy 23 in the NBLA
Deuteronomy 23 in the NBS
Deuteronomy 23 in the NBVTP
Deuteronomy 23 in the NET2
Deuteronomy 23 in the NIV11
Deuteronomy 23 in the NNT
Deuteronomy 23 in the NNT2
Deuteronomy 23 in the NNT3
Deuteronomy 23 in the PDDPT
Deuteronomy 23 in the PFNT
Deuteronomy 23 in the RMNT
Deuteronomy 23 in the SBIAS
Deuteronomy 23 in the SBIBS
Deuteronomy 23 in the SBIBS2
Deuteronomy 23 in the SBICS
Deuteronomy 23 in the SBIDS
Deuteronomy 23 in the SBIGS
Deuteronomy 23 in the SBIHS
Deuteronomy 23 in the SBIIS
Deuteronomy 23 in the SBIIS2
Deuteronomy 23 in the SBIIS3
Deuteronomy 23 in the SBIKS
Deuteronomy 23 in the SBIKS2
Deuteronomy 23 in the SBIMS
Deuteronomy 23 in the SBIOS
Deuteronomy 23 in the SBIPS
Deuteronomy 23 in the SBISS
Deuteronomy 23 in the SBITS
Deuteronomy 23 in the SBITS2
Deuteronomy 23 in the SBITS3
Deuteronomy 23 in the SBITS4
Deuteronomy 23 in the SBIUS
Deuteronomy 23 in the SBIVS
Deuteronomy 23 in the SBT
Deuteronomy 23 in the SBT1E
Deuteronomy 23 in the SCHL
Deuteronomy 23 in the SNT
Deuteronomy 23 in the SUSU
Deuteronomy 23 in the SUSU2
Deuteronomy 23 in the SYNO
Deuteronomy 23 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 23 in the TBT1E
Deuteronomy 23 in the TBT1E2
Deuteronomy 23 in the TFTIP
Deuteronomy 23 in the TFTU
Deuteronomy 23 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 23 in the THAI
Deuteronomy 23 in the TNFD
Deuteronomy 23 in the TNT
Deuteronomy 23 in the TNTIK
Deuteronomy 23 in the TNTIL
Deuteronomy 23 in the TNTIN
Deuteronomy 23 in the TNTIP
Deuteronomy 23 in the TNTIZ
Deuteronomy 23 in the TOMA
Deuteronomy 23 in the TTENT
Deuteronomy 23 in the UBG
Deuteronomy 23 in the UGV
Deuteronomy 23 in the UGV2
Deuteronomy 23 in the UGV3
Deuteronomy 23 in the VBL
Deuteronomy 23 in the VDCC
Deuteronomy 23 in the YALU
Deuteronomy 23 in the YAPE
Deuteronomy 23 in the YBVTP
Deuteronomy 23 in the ZBP