Deuteronomy 27 (BOGWICC)

1 Mose ndi akuluakulu a Israeli analamula anthu kuti, “Sungani malamulo onse amene ndikukupatsani lero lino. 2 Mukawoloka mtsinje wa Yorodani kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muyimiritse miyala ingapo ikuluikulu ndi kuyikulungiza. 3 Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani. 4 Ndipo mukawoloka Yorodani muyimike miyala iyi pa Phiri la Ebala monga momwe ndikukulamulirani lero lino ndipo muyikulungize. 5 Pamenepo mumange guwa lansembe la miyala la Yehova Mulungu wanu. Musagwiritse ntchito chida chilichonse chachitsulo pa miyalapo. 6 Mumange guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu ndi miyala yakutchire ndi kuperekerapo nsembe yopsereza kwa Yehova Mulungu wanu. 7 Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 8 Ndipo pa miyalapo mudzalembepo mawu onse a malamulo ndi malemba akuluakulu.” 9 Kenaka Mose ndi ansembe, amene ndi Alevi anati kwa Aisraeli onse, “Khalani chete Aisraeli inu ndipo mumvetsere! Tsopano inu ndinu anthu a Yehova Mulungu wanu. 10 Muzimvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsata malamulo ake ndi malangizo ake omwe ndikukupatsani lero lino.” 11 Tsiku lomwelo Mose analamula anthu kuti: 12 Mukawoloka Yorodani, mafuko awa akayimirire pa Phiri la Gerizimu ndi kudalitsa anthu: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13 Ndipo mafuko awa akayimirire pa Phiri la Ebala ndi kutchula matemberero: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafutali. 14 Alevi adzayankhula mokweza kwa Aisraeli onse kuti: 15 “Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 16 “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 17 “Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 18 “Ndi wotembereredwa munthu amene amasocheretsa munthu wosaona pa msewu.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 19 “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 20 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 21 “Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 22 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 23 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 24 “Ndi wotembereredwa munthu amene apha mnzake mwachinsinsi.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 25 “Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” 26 “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.”Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

In Other Versions

Deuteronomy 27 in the ANGEFD

Deuteronomy 27 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 27 in the AS21

Deuteronomy 27 in the BAGH

Deuteronomy 27 in the BBPNG

Deuteronomy 27 in the BBT1E

Deuteronomy 27 in the BDS

Deuteronomy 27 in the BEV

Deuteronomy 27 in the BHAD

Deuteronomy 27 in the BIB

Deuteronomy 27 in the BLPT

Deuteronomy 27 in the BNT

Deuteronomy 27 in the BNTABOOT

Deuteronomy 27 in the BNTLV

Deuteronomy 27 in the BOATCB

Deuteronomy 27 in the BOATCB2

Deuteronomy 27 in the BOBCV

Deuteronomy 27 in the BOCNT

Deuteronomy 27 in the BOECS

Deuteronomy 27 in the BOHCB

Deuteronomy 27 in the BOHCV

Deuteronomy 27 in the BOHLNT

Deuteronomy 27 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 27 in the BOICB

Deuteronomy 27 in the BOILNTAP

Deuteronomy 27 in the BOITCV

Deuteronomy 27 in the BOKCV

Deuteronomy 27 in the BOKCV2

Deuteronomy 27 in the BOKHWOG

Deuteronomy 27 in the BOKSSV

Deuteronomy 27 in the BOLCB

Deuteronomy 27 in the BOLCB2

Deuteronomy 27 in the BOMCV

Deuteronomy 27 in the BONAV

Deuteronomy 27 in the BONCB

Deuteronomy 27 in the BONLT

Deuteronomy 27 in the BONUT2

Deuteronomy 27 in the BOPLNT

Deuteronomy 27 in the BOSCB

Deuteronomy 27 in the BOSNC

Deuteronomy 27 in the BOTLNT

Deuteronomy 27 in the BOVCB

Deuteronomy 27 in the BOYCB

Deuteronomy 27 in the BPBB

Deuteronomy 27 in the BPH

Deuteronomy 27 in the BSB

Deuteronomy 27 in the CCB

Deuteronomy 27 in the CUV

Deuteronomy 27 in the CUVS

Deuteronomy 27 in the DBT

Deuteronomy 27 in the DGDNT

Deuteronomy 27 in the DHNT

Deuteronomy 27 in the DNT

Deuteronomy 27 in the ELBE

Deuteronomy 27 in the EMTV

Deuteronomy 27 in the ESV

Deuteronomy 27 in the FBV

Deuteronomy 27 in the FEB

Deuteronomy 27 in the GGMNT

Deuteronomy 27 in the GNT

Deuteronomy 27 in the HARY

Deuteronomy 27 in the HNT

Deuteronomy 27 in the IRVA

Deuteronomy 27 in the IRVB

Deuteronomy 27 in the IRVG

Deuteronomy 27 in the IRVH

Deuteronomy 27 in the IRVK

Deuteronomy 27 in the IRVM

Deuteronomy 27 in the IRVM2

Deuteronomy 27 in the IRVO

Deuteronomy 27 in the IRVP

Deuteronomy 27 in the IRVT

Deuteronomy 27 in the IRVT2

Deuteronomy 27 in the IRVU

Deuteronomy 27 in the ISVN

Deuteronomy 27 in the JSNT

Deuteronomy 27 in the KAPI

Deuteronomy 27 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 27 in the KBV

Deuteronomy 27 in the KJV

Deuteronomy 27 in the KNFD

Deuteronomy 27 in the LBA

Deuteronomy 27 in the LBLA

Deuteronomy 27 in the LNT

Deuteronomy 27 in the LSV

Deuteronomy 27 in the MAAL

Deuteronomy 27 in the MBV

Deuteronomy 27 in the MBV2

Deuteronomy 27 in the MHNT

Deuteronomy 27 in the MKNFD

Deuteronomy 27 in the MNG

Deuteronomy 27 in the MNT

Deuteronomy 27 in the MNT2

Deuteronomy 27 in the MRS1T

Deuteronomy 27 in the NAA

Deuteronomy 27 in the NASB

Deuteronomy 27 in the NBLA

Deuteronomy 27 in the NBS

Deuteronomy 27 in the NBVTP

Deuteronomy 27 in the NET2

Deuteronomy 27 in the NIV11

Deuteronomy 27 in the NNT

Deuteronomy 27 in the NNT2

Deuteronomy 27 in the NNT3

Deuteronomy 27 in the PDDPT

Deuteronomy 27 in the PFNT

Deuteronomy 27 in the RMNT

Deuteronomy 27 in the SBIAS

Deuteronomy 27 in the SBIBS

Deuteronomy 27 in the SBIBS2

Deuteronomy 27 in the SBICS

Deuteronomy 27 in the SBIDS

Deuteronomy 27 in the SBIGS

Deuteronomy 27 in the SBIHS

Deuteronomy 27 in the SBIIS

Deuteronomy 27 in the SBIIS2

Deuteronomy 27 in the SBIIS3

Deuteronomy 27 in the SBIKS

Deuteronomy 27 in the SBIKS2

Deuteronomy 27 in the SBIMS

Deuteronomy 27 in the SBIOS

Deuteronomy 27 in the SBIPS

Deuteronomy 27 in the SBISS

Deuteronomy 27 in the SBITS

Deuteronomy 27 in the SBITS2

Deuteronomy 27 in the SBITS3

Deuteronomy 27 in the SBITS4

Deuteronomy 27 in the SBIUS

Deuteronomy 27 in the SBIVS

Deuteronomy 27 in the SBT

Deuteronomy 27 in the SBT1E

Deuteronomy 27 in the SCHL

Deuteronomy 27 in the SNT

Deuteronomy 27 in the SUSU

Deuteronomy 27 in the SUSU2

Deuteronomy 27 in the SYNO

Deuteronomy 27 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 27 in the TBT1E

Deuteronomy 27 in the TBT1E2

Deuteronomy 27 in the TFTIP

Deuteronomy 27 in the TFTU

Deuteronomy 27 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 27 in the THAI

Deuteronomy 27 in the TNFD

Deuteronomy 27 in the TNT

Deuteronomy 27 in the TNTIK

Deuteronomy 27 in the TNTIL

Deuteronomy 27 in the TNTIN

Deuteronomy 27 in the TNTIP

Deuteronomy 27 in the TNTIZ

Deuteronomy 27 in the TOMA

Deuteronomy 27 in the TTENT

Deuteronomy 27 in the UBG

Deuteronomy 27 in the UGV

Deuteronomy 27 in the UGV2

Deuteronomy 27 in the UGV3

Deuteronomy 27 in the VBL

Deuteronomy 27 in the VDCC

Deuteronomy 27 in the YALU

Deuteronomy 27 in the YAPE

Deuteronomy 27 in the YBVTP

Deuteronomy 27 in the ZBP