Deuteronomy 30 (BOGWICC)

1 Madalitso ndi matemberero awa onse amene ndawayika pamaso panu akadzafika pa inu, inu nʼkukumbukira kulikonse kumene Yehova Mulungu wanu wakubalalitsirani pakati pa mitundu ya anthu, 2 ndipo inu pamodzi ndi ana anu nʼkudzatembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse molingana ndi chilichonse chimene ndakulamulani lero lino, 3 pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakukhalitsani monga kale ndi kukuchitirani chifundo, ndipo adzakusonkhanitsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu kumene anakubalalitsirani. 4 Ngakhale atakupirikitsirani ku malekezero a dziko lapansi, adzakusonkhanitsani kuchokera kumeneko ndi kukubweretsaninso. 5 Adzakubweretsani ku dziko limene linali la makolo anu, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzakulemeretsani ndi kukuchulukitsani kupambana makolo anu. 6 Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo. 7 Yehova Mulungu wanu adzayika matemberero awa onse pa adani anu amene amadana nanu ndi kukuzunzani. 8 Inu mudzamveranso Yehova ndi kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino. 9 Pamenepo Yehova Mulungu wanu adzakulemeretsani pa zochita zanu zonse ndipo adzakupatsani ana ambiri, zoweta zambiri, ndiponso mudzakhala ndi zokolola zambiri za mʼdziko lanu. Yehova adzakondwera nanunso ndi kukulemeretsani monga momwe anakondwera ndi makolo anu, 10 ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 11 Tsopano zimene ndikukulamulirani leroli sizovuta kapena zapatali. 12 Sizili kumwamba, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene akwere kumwamba kuti akazitenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 13 Komanso sizili pa tsidya la nyanja, kuti muzichita kufunsa kuti, “Kodi ndani amene adzawoloke nyanja kuti akatenge ndi kudzatilalikira kuti timvere?” 14 Ayi, mawu ali pafupi ndi inu; ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu kuti muwamvere. 15 Taonani, lero ine ndayika pamaso panu moyo ndi zokoma, imfa ndi chiwonongeko. 16 Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo. 17 Koma ngati mtima wanu udzatembenuka, inu nʼkukhala osandimvera, ndipo ngati mudzatengeka ndi kupita kukagwadira milungu ina ndi kuyipembedza, 18 lero ndikulengeza kwa inu kuti mudzawonongeka ndithu. Simudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukulowamo pamene mukuwoloka Yorodani kuti mulitenge. 19 Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo. 20 Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.

In Other Versions

Deuteronomy 30 in the ANGEFD

Deuteronomy 30 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 30 in the AS21

Deuteronomy 30 in the BAGH

Deuteronomy 30 in the BBPNG

Deuteronomy 30 in the BBT1E

Deuteronomy 30 in the BDS

Deuteronomy 30 in the BEV

Deuteronomy 30 in the BHAD

Deuteronomy 30 in the BIB

Deuteronomy 30 in the BLPT

Deuteronomy 30 in the BNT

Deuteronomy 30 in the BNTABOOT

Deuteronomy 30 in the BNTLV

Deuteronomy 30 in the BOATCB

Deuteronomy 30 in the BOATCB2

Deuteronomy 30 in the BOBCV

Deuteronomy 30 in the BOCNT

Deuteronomy 30 in the BOECS

Deuteronomy 30 in the BOHCB

Deuteronomy 30 in the BOHCV

Deuteronomy 30 in the BOHLNT

Deuteronomy 30 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 30 in the BOICB

Deuteronomy 30 in the BOILNTAP

Deuteronomy 30 in the BOITCV

Deuteronomy 30 in the BOKCV

Deuteronomy 30 in the BOKCV2

Deuteronomy 30 in the BOKHWOG

Deuteronomy 30 in the BOKSSV

Deuteronomy 30 in the BOLCB

Deuteronomy 30 in the BOLCB2

Deuteronomy 30 in the BOMCV

Deuteronomy 30 in the BONAV

Deuteronomy 30 in the BONCB

Deuteronomy 30 in the BONLT

Deuteronomy 30 in the BONUT2

Deuteronomy 30 in the BOPLNT

Deuteronomy 30 in the BOSCB

Deuteronomy 30 in the BOSNC

Deuteronomy 30 in the BOTLNT

Deuteronomy 30 in the BOVCB

Deuteronomy 30 in the BOYCB

Deuteronomy 30 in the BPBB

Deuteronomy 30 in the BPH

Deuteronomy 30 in the BSB

Deuteronomy 30 in the CCB

Deuteronomy 30 in the CUV

Deuteronomy 30 in the CUVS

Deuteronomy 30 in the DBT

Deuteronomy 30 in the DGDNT

Deuteronomy 30 in the DHNT

Deuteronomy 30 in the DNT

Deuteronomy 30 in the ELBE

Deuteronomy 30 in the EMTV

Deuteronomy 30 in the ESV

Deuteronomy 30 in the FBV

Deuteronomy 30 in the FEB

Deuteronomy 30 in the GGMNT

Deuteronomy 30 in the GNT

Deuteronomy 30 in the HARY

Deuteronomy 30 in the HNT

Deuteronomy 30 in the IRVA

Deuteronomy 30 in the IRVB

Deuteronomy 30 in the IRVG

Deuteronomy 30 in the IRVH

Deuteronomy 30 in the IRVK

Deuteronomy 30 in the IRVM

Deuteronomy 30 in the IRVM2

Deuteronomy 30 in the IRVO

Deuteronomy 30 in the IRVP

Deuteronomy 30 in the IRVT

Deuteronomy 30 in the IRVT2

Deuteronomy 30 in the IRVU

Deuteronomy 30 in the ISVN

Deuteronomy 30 in the JSNT

Deuteronomy 30 in the KAPI

Deuteronomy 30 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 30 in the KBV

Deuteronomy 30 in the KJV

Deuteronomy 30 in the KNFD

Deuteronomy 30 in the LBA

Deuteronomy 30 in the LBLA

Deuteronomy 30 in the LNT

Deuteronomy 30 in the LSV

Deuteronomy 30 in the MAAL

Deuteronomy 30 in the MBV

Deuteronomy 30 in the MBV2

Deuteronomy 30 in the MHNT

Deuteronomy 30 in the MKNFD

Deuteronomy 30 in the MNG

Deuteronomy 30 in the MNT

Deuteronomy 30 in the MNT2

Deuteronomy 30 in the MRS1T

Deuteronomy 30 in the NAA

Deuteronomy 30 in the NASB

Deuteronomy 30 in the NBLA

Deuteronomy 30 in the NBS

Deuteronomy 30 in the NBVTP

Deuteronomy 30 in the NET2

Deuteronomy 30 in the NIV11

Deuteronomy 30 in the NNT

Deuteronomy 30 in the NNT2

Deuteronomy 30 in the NNT3

Deuteronomy 30 in the PDDPT

Deuteronomy 30 in the PFNT

Deuteronomy 30 in the RMNT

Deuteronomy 30 in the SBIAS

Deuteronomy 30 in the SBIBS

Deuteronomy 30 in the SBIBS2

Deuteronomy 30 in the SBICS

Deuteronomy 30 in the SBIDS

Deuteronomy 30 in the SBIGS

Deuteronomy 30 in the SBIHS

Deuteronomy 30 in the SBIIS

Deuteronomy 30 in the SBIIS2

Deuteronomy 30 in the SBIIS3

Deuteronomy 30 in the SBIKS

Deuteronomy 30 in the SBIKS2

Deuteronomy 30 in the SBIMS

Deuteronomy 30 in the SBIOS

Deuteronomy 30 in the SBIPS

Deuteronomy 30 in the SBISS

Deuteronomy 30 in the SBITS

Deuteronomy 30 in the SBITS2

Deuteronomy 30 in the SBITS3

Deuteronomy 30 in the SBITS4

Deuteronomy 30 in the SBIUS

Deuteronomy 30 in the SBIVS

Deuteronomy 30 in the SBT

Deuteronomy 30 in the SBT1E

Deuteronomy 30 in the SCHL

Deuteronomy 30 in the SNT

Deuteronomy 30 in the SUSU

Deuteronomy 30 in the SUSU2

Deuteronomy 30 in the SYNO

Deuteronomy 30 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 30 in the TBT1E

Deuteronomy 30 in the TBT1E2

Deuteronomy 30 in the TFTIP

Deuteronomy 30 in the TFTU

Deuteronomy 30 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 30 in the THAI

Deuteronomy 30 in the TNFD

Deuteronomy 30 in the TNT

Deuteronomy 30 in the TNTIK

Deuteronomy 30 in the TNTIL

Deuteronomy 30 in the TNTIN

Deuteronomy 30 in the TNTIP

Deuteronomy 30 in the TNTIZ

Deuteronomy 30 in the TOMA

Deuteronomy 30 in the TTENT

Deuteronomy 30 in the UBG

Deuteronomy 30 in the UGV

Deuteronomy 30 in the UGV2

Deuteronomy 30 in the UGV3

Deuteronomy 30 in the VBL

Deuteronomy 30 in the VDCC

Deuteronomy 30 in the YALU

Deuteronomy 30 in the YAPE

Deuteronomy 30 in the YBVTP

Deuteronomy 30 in the ZBP