Deuteronomy 8 (BOGWICC)
1 Samalani potsata lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mukhale ndi moyo ndi kuchulukana kuti mulande ndi kulowa mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu. 2 Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi. 3 Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova. 4 Mʼzaka makumi anayi zimenezi, zovala zanu sizinangʼambike ndipo mapazi anu sanatupe. 5 Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani. 6 Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye. 7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino, dziko lokhala ndi mitsinje ndi mathawale a madzi, akasupe oyenderera mu zigwa ndi mʼmapiri, 8 dziko lokhala ndi tirigu ndi barele, mpesa ndi mitengo ya mkuyu, makangadza, mafuta a olivi ndi uchi; 9 dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa. 10 Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani. 11 Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, 12 kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo, 13 ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka, 14 mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo. 15 Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma. 16 Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino. 17 Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.” 18 Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino. 19 Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu. 20 Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.
In Other Versions
Deuteronomy 8 in the ANGEFD
Deuteronomy 8 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 8 in the AS21
Deuteronomy 8 in the BAGH
Deuteronomy 8 in the BBPNG
Deuteronomy 8 in the BBT1E
Deuteronomy 8 in the BDS
Deuteronomy 8 in the BEV
Deuteronomy 8 in the BHAD
Deuteronomy 8 in the BIB
Deuteronomy 8 in the BLPT
Deuteronomy 8 in the BNT
Deuteronomy 8 in the BNTABOOT
Deuteronomy 8 in the BNTLV
Deuteronomy 8 in the BOATCB
Deuteronomy 8 in the BOATCB2
Deuteronomy 8 in the BOBCV
Deuteronomy 8 in the BOCNT
Deuteronomy 8 in the BOECS
Deuteronomy 8 in the BOHCB
Deuteronomy 8 in the BOHCV
Deuteronomy 8 in the BOHLNT
Deuteronomy 8 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 8 in the BOICB
Deuteronomy 8 in the BOILNTAP
Deuteronomy 8 in the BOITCV
Deuteronomy 8 in the BOKCV
Deuteronomy 8 in the BOKCV2
Deuteronomy 8 in the BOKHWOG
Deuteronomy 8 in the BOKSSV
Deuteronomy 8 in the BOLCB
Deuteronomy 8 in the BOLCB2
Deuteronomy 8 in the BOMCV
Deuteronomy 8 in the BONAV
Deuteronomy 8 in the BONCB
Deuteronomy 8 in the BONLT
Deuteronomy 8 in the BONUT2
Deuteronomy 8 in the BOPLNT
Deuteronomy 8 in the BOSCB
Deuteronomy 8 in the BOSNC
Deuteronomy 8 in the BOTLNT
Deuteronomy 8 in the BOVCB
Deuteronomy 8 in the BOYCB
Deuteronomy 8 in the BPBB
Deuteronomy 8 in the BPH
Deuteronomy 8 in the BSB
Deuteronomy 8 in the CCB
Deuteronomy 8 in the CUV
Deuteronomy 8 in the CUVS
Deuteronomy 8 in the DBT
Deuteronomy 8 in the DGDNT
Deuteronomy 8 in the DHNT
Deuteronomy 8 in the DNT
Deuteronomy 8 in the ELBE
Deuteronomy 8 in the EMTV
Deuteronomy 8 in the ESV
Deuteronomy 8 in the FBV
Deuteronomy 8 in the FEB
Deuteronomy 8 in the GGMNT
Deuteronomy 8 in the GNT
Deuteronomy 8 in the HARY
Deuteronomy 8 in the HNT
Deuteronomy 8 in the IRVA
Deuteronomy 8 in the IRVB
Deuteronomy 8 in the IRVG
Deuteronomy 8 in the IRVH
Deuteronomy 8 in the IRVK
Deuteronomy 8 in the IRVM
Deuteronomy 8 in the IRVM2
Deuteronomy 8 in the IRVO
Deuteronomy 8 in the IRVP
Deuteronomy 8 in the IRVT
Deuteronomy 8 in the IRVT2
Deuteronomy 8 in the IRVU
Deuteronomy 8 in the ISVN
Deuteronomy 8 in the JSNT
Deuteronomy 8 in the KAPI
Deuteronomy 8 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 8 in the KBV
Deuteronomy 8 in the KJV
Deuteronomy 8 in the KNFD
Deuteronomy 8 in the LBA
Deuteronomy 8 in the LBLA
Deuteronomy 8 in the LNT
Deuteronomy 8 in the LSV
Deuteronomy 8 in the MAAL
Deuteronomy 8 in the MBV
Deuteronomy 8 in the MBV2
Deuteronomy 8 in the MHNT
Deuteronomy 8 in the MKNFD
Deuteronomy 8 in the MNG
Deuteronomy 8 in the MNT
Deuteronomy 8 in the MNT2
Deuteronomy 8 in the MRS1T
Deuteronomy 8 in the NAA
Deuteronomy 8 in the NASB
Deuteronomy 8 in the NBLA
Deuteronomy 8 in the NBS
Deuteronomy 8 in the NBVTP
Deuteronomy 8 in the NET2
Deuteronomy 8 in the NIV11
Deuteronomy 8 in the NNT
Deuteronomy 8 in the NNT2
Deuteronomy 8 in the NNT3
Deuteronomy 8 in the PDDPT
Deuteronomy 8 in the PFNT
Deuteronomy 8 in the RMNT
Deuteronomy 8 in the SBIAS
Deuteronomy 8 in the SBIBS
Deuteronomy 8 in the SBIBS2
Deuteronomy 8 in the SBICS
Deuteronomy 8 in the SBIDS
Deuteronomy 8 in the SBIGS
Deuteronomy 8 in the SBIHS
Deuteronomy 8 in the SBIIS
Deuteronomy 8 in the SBIIS2
Deuteronomy 8 in the SBIIS3
Deuteronomy 8 in the SBIKS
Deuteronomy 8 in the SBIKS2
Deuteronomy 8 in the SBIMS
Deuteronomy 8 in the SBIOS
Deuteronomy 8 in the SBIPS
Deuteronomy 8 in the SBISS
Deuteronomy 8 in the SBITS
Deuteronomy 8 in the SBITS2
Deuteronomy 8 in the SBITS3
Deuteronomy 8 in the SBITS4
Deuteronomy 8 in the SBIUS
Deuteronomy 8 in the SBIVS
Deuteronomy 8 in the SBT
Deuteronomy 8 in the SBT1E
Deuteronomy 8 in the SCHL
Deuteronomy 8 in the SNT
Deuteronomy 8 in the SUSU
Deuteronomy 8 in the SUSU2
Deuteronomy 8 in the SYNO
Deuteronomy 8 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 8 in the TBT1E
Deuteronomy 8 in the TBT1E2
Deuteronomy 8 in the TFTIP
Deuteronomy 8 in the TFTU
Deuteronomy 8 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 8 in the THAI
Deuteronomy 8 in the TNFD
Deuteronomy 8 in the TNT
Deuteronomy 8 in the TNTIK
Deuteronomy 8 in the TNTIL
Deuteronomy 8 in the TNTIN
Deuteronomy 8 in the TNTIP
Deuteronomy 8 in the TNTIZ
Deuteronomy 8 in the TOMA
Deuteronomy 8 in the TTENT
Deuteronomy 8 in the UBG
Deuteronomy 8 in the UGV
Deuteronomy 8 in the UGV2
Deuteronomy 8 in the UGV3
Deuteronomy 8 in the VBL
Deuteronomy 8 in the VDCC
Deuteronomy 8 in the YALU
Deuteronomy 8 in the YAPE
Deuteronomy 8 in the YBVTP
Deuteronomy 8 in the ZBP