Ecclesiastes 9 (BOGWICC)
1 Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani. 2 Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe.Zomwe zimachitikira munthu wabwino,zimachitikiranso munthu wochimwa,zomwe zimachitikira amene amalumbira,zimachitikiranso amene amaopa kulumbira. 3 Choyipa chimene chili mʼzonse zochitika pansi ndi ichi: Mathero a zonse ndi amodzi. Ndithu, mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoyipa, ndipo mʼmitima mwawo muli zamisala pamene ali ndi moyo, potsiriza pake iwo amakakhala pamodzi ndi anthu akufa. 4 Aliyense amene ali ndi moyo amakhala ndi chiyembekezo, pajatu galu wamoyo aposa mkango wakufa! 5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,koma akufa sadziwa kanthu;alibe mphotho ina yowonjezera,ndipo palibe amene amawakumbukira. 6 Chikondi chawo, chidani chawondiponso nsanje yawo, zonse zinatha kalekale;sadzakhalanso ndi gawopa zonse zochitika pansi pano. 7 Pita, kadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti tsopano Mulungu akukondwera ndi zochita zako. 8 Uzivala zovala zoyera nthawi zonse, uzidzola mafuta mʼmutu mwako nthawi zonse. 9 Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano. 10 Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru. 11 Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano:opambana pa kuthamanga si aliwiro,kapena opambana pa nkhondo si amphamvu,ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru,kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri,kapena okomeredwa mtima si ophunzira;koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake. 12 Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti:monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde,kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha,chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa,pamene tsoka limawagwera mosayembekezera. 13 Ine ndinaonanso pansi pano chitsanzo ichi cha nzeru chimene chinandikhudza kwambiri: 14 Panali mzinda waungʼono umene unali ndi anthu owerengeka. Ndipo mfumu yamphamvu inabwera kudzawuthira nkhondo, inawuzungulira ndi kumanga mitumbira yankhondo. 15 Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo. 16 Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake. 17 Mawu oyankhula mofatsa a munthu wanzeru, anthu amawasamalira kwambirikupambana kufuwula kwa mfumu ya zitsiru. 18 Nzeru ndi yabwino kupambana zida zankhondo,koma wochimwa mmodzi amawononga zinthu zambiri zabwino.
In Other Versions
Ecclesiastes 9 in the ANGEFD
Ecclesiastes 9 in the ANTPNG2D
Ecclesiastes 9 in the AS21
Ecclesiastes 9 in the BAGH
Ecclesiastes 9 in the BBPNG
Ecclesiastes 9 in the BBT1E
Ecclesiastes 9 in the BDS
Ecclesiastes 9 in the BEV
Ecclesiastes 9 in the BHAD
Ecclesiastes 9 in the BIB
Ecclesiastes 9 in the BLPT
Ecclesiastes 9 in the BNT
Ecclesiastes 9 in the BNTABOOT
Ecclesiastes 9 in the BNTLV
Ecclesiastes 9 in the BOATCB
Ecclesiastes 9 in the BOATCB2
Ecclesiastes 9 in the BOBCV
Ecclesiastes 9 in the BOCNT
Ecclesiastes 9 in the BOECS
Ecclesiastes 9 in the BOHCB
Ecclesiastes 9 in the BOHCV
Ecclesiastes 9 in the BOHLNT
Ecclesiastes 9 in the BOHNTLTAL
Ecclesiastes 9 in the BOICB
Ecclesiastes 9 in the BOILNTAP
Ecclesiastes 9 in the BOITCV
Ecclesiastes 9 in the BOKCV
Ecclesiastes 9 in the BOKCV2
Ecclesiastes 9 in the BOKHWOG
Ecclesiastes 9 in the BOKSSV
Ecclesiastes 9 in the BOLCB
Ecclesiastes 9 in the BOLCB2
Ecclesiastes 9 in the BOMCV
Ecclesiastes 9 in the BONAV
Ecclesiastes 9 in the BONCB
Ecclesiastes 9 in the BONLT
Ecclesiastes 9 in the BONUT2
Ecclesiastes 9 in the BOPLNT
Ecclesiastes 9 in the BOSCB
Ecclesiastes 9 in the BOSNC
Ecclesiastes 9 in the BOTLNT
Ecclesiastes 9 in the BOVCB
Ecclesiastes 9 in the BOYCB
Ecclesiastes 9 in the BPBB
Ecclesiastes 9 in the BPH
Ecclesiastes 9 in the BSB
Ecclesiastes 9 in the CCB
Ecclesiastes 9 in the CUV
Ecclesiastes 9 in the CUVS
Ecclesiastes 9 in the DBT
Ecclesiastes 9 in the DGDNT
Ecclesiastes 9 in the DHNT
Ecclesiastes 9 in the DNT
Ecclesiastes 9 in the ELBE
Ecclesiastes 9 in the EMTV
Ecclesiastes 9 in the ESV
Ecclesiastes 9 in the FBV
Ecclesiastes 9 in the FEB
Ecclesiastes 9 in the GGMNT
Ecclesiastes 9 in the GNT
Ecclesiastes 9 in the HARY
Ecclesiastes 9 in the HNT
Ecclesiastes 9 in the IRVA
Ecclesiastes 9 in the IRVB
Ecclesiastes 9 in the IRVG
Ecclesiastes 9 in the IRVH
Ecclesiastes 9 in the IRVK
Ecclesiastes 9 in the IRVM
Ecclesiastes 9 in the IRVM2
Ecclesiastes 9 in the IRVO
Ecclesiastes 9 in the IRVP
Ecclesiastes 9 in the IRVT
Ecclesiastes 9 in the IRVT2
Ecclesiastes 9 in the IRVU
Ecclesiastes 9 in the ISVN
Ecclesiastes 9 in the JSNT
Ecclesiastes 9 in the KAPI
Ecclesiastes 9 in the KBT1ETNIK
Ecclesiastes 9 in the KBV
Ecclesiastes 9 in the KJV
Ecclesiastes 9 in the KNFD
Ecclesiastes 9 in the LBA
Ecclesiastes 9 in the LBLA
Ecclesiastes 9 in the LNT
Ecclesiastes 9 in the LSV
Ecclesiastes 9 in the MAAL
Ecclesiastes 9 in the MBV
Ecclesiastes 9 in the MBV2
Ecclesiastes 9 in the MHNT
Ecclesiastes 9 in the MKNFD
Ecclesiastes 9 in the MNG
Ecclesiastes 9 in the MNT
Ecclesiastes 9 in the MNT2
Ecclesiastes 9 in the MRS1T
Ecclesiastes 9 in the NAA
Ecclesiastes 9 in the NASB
Ecclesiastes 9 in the NBLA
Ecclesiastes 9 in the NBS
Ecclesiastes 9 in the NBVTP
Ecclesiastes 9 in the NET2
Ecclesiastes 9 in the NIV11
Ecclesiastes 9 in the NNT
Ecclesiastes 9 in the NNT2
Ecclesiastes 9 in the NNT3
Ecclesiastes 9 in the PDDPT
Ecclesiastes 9 in the PFNT
Ecclesiastes 9 in the RMNT
Ecclesiastes 9 in the SBIAS
Ecclesiastes 9 in the SBIBS
Ecclesiastes 9 in the SBIBS2
Ecclesiastes 9 in the SBICS
Ecclesiastes 9 in the SBIDS
Ecclesiastes 9 in the SBIGS
Ecclesiastes 9 in the SBIHS
Ecclesiastes 9 in the SBIIS
Ecclesiastes 9 in the SBIIS2
Ecclesiastes 9 in the SBIIS3
Ecclesiastes 9 in the SBIKS
Ecclesiastes 9 in the SBIKS2
Ecclesiastes 9 in the SBIMS
Ecclesiastes 9 in the SBIOS
Ecclesiastes 9 in the SBIPS
Ecclesiastes 9 in the SBISS
Ecclesiastes 9 in the SBITS
Ecclesiastes 9 in the SBITS2
Ecclesiastes 9 in the SBITS3
Ecclesiastes 9 in the SBITS4
Ecclesiastes 9 in the SBIUS
Ecclesiastes 9 in the SBIVS
Ecclesiastes 9 in the SBT
Ecclesiastes 9 in the SBT1E
Ecclesiastes 9 in the SCHL
Ecclesiastes 9 in the SNT
Ecclesiastes 9 in the SUSU
Ecclesiastes 9 in the SUSU2
Ecclesiastes 9 in the SYNO
Ecclesiastes 9 in the TBIAOTANT
Ecclesiastes 9 in the TBT1E
Ecclesiastes 9 in the TBT1E2
Ecclesiastes 9 in the TFTIP
Ecclesiastes 9 in the TFTU
Ecclesiastes 9 in the TGNTATF3T
Ecclesiastes 9 in the THAI
Ecclesiastes 9 in the TNFD
Ecclesiastes 9 in the TNT
Ecclesiastes 9 in the TNTIK
Ecclesiastes 9 in the TNTIL
Ecclesiastes 9 in the TNTIN
Ecclesiastes 9 in the TNTIP
Ecclesiastes 9 in the TNTIZ
Ecclesiastes 9 in the TOMA
Ecclesiastes 9 in the TTENT
Ecclesiastes 9 in the UBG
Ecclesiastes 9 in the UGV
Ecclesiastes 9 in the UGV2
Ecclesiastes 9 in the UGV3
Ecclesiastes 9 in the VBL
Ecclesiastes 9 in the VDCC
Ecclesiastes 9 in the YALU
Ecclesiastes 9 in the YAPE
Ecclesiastes 9 in the YBVTP
Ecclesiastes 9 in the ZBP