Exodus 38 (BOGWICC)

1 Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229. 2 Anapanga nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo, kotero kuti nyangazo ndi guwalo zinali chinthu chimodzi, ndipo anakuta guwalo ndi mkuwa. 3 Anapanganso ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto. 4 Anapanga sefa yachitsulo chamkuwa ya guwa lansembelo kuti ikhale mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, kuchokera pansi mpaka pakati pa khoma la guwalo. 5 Anapanga mphete zamkuwa zinayi ndipo anazilumikiza ku ngodya zinayi za sefa ija kuti zigwire nsichi zonyamulira. 6 Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndipo anazikuta ndi mkuwa. 7 Iwo analowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo kuti azinyamulira. Guwalo linali lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. 8 Anapanga beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso kuchokera ku magalasi oyangʼanira nkhope a amayi amene ankatumikira pa chipata cha tenti ya msonkhano. 9 Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. 10 Anapanganso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 11 Mbali yakumpoto inalinso yotalika mamita 46 ndipo inali ndi mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 12 Mbali yakumadzulo inali yotalika mamita 23 ndipo inali ndi nsalu yotchinga, mizati khumi ndi matsinde khumi. Inalinso ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 13 Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, inalinso yotalika mamita 23. 14 Mbali imodzi yachipata kunali nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu, 15 polowera mʼbwalo panali nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu. 16 Katani yonse yotchinga kuzungulira chihema inali yofewa, yosalala ndi yolukidwa bwino. 17 Matsinde amizati anali amkuwa. Ngowe ndi zingwe za mizati zinali zasiliva, ndipo pamwamba pa mizatiyo anakutapo siliva. Choncho mizati yonse ya bwalolo inalumikizidwa ndi zingwe zasiliva. 18 Nsalu yotchinga ya pa chipata inali yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira, yofewa yosalala ndi yopangidwa ndi anthu aluso. Nsaluyo inali yotalika mamita asanu ndi anayi, molingana ndi nsalu zotchinga bwalo. Msinkhu wake unali masentimita 229, 19 pamodzi ndi mizati yake inayi ndi matsinde amkuwa anayi. Ngowe ndi zingwe zake zinali za siliva, ndipo pamwamba pake pa mzati anakutapo ndi siliva. 20 Zikhomo za chihema ndi zina zonse zozungulira chihemacho zinali zamkuwa. 21 Chiwerengero cha zipangizo zimene anagwiritsa ntchito popanga chihema, chihema chaumboni, zimene Mose analamulira Alevi kuti alembe motsogozedwa ndi Itamara mwana wa Aaroni, wansembe, chinali ichi: 22 Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huzi wa fuko la Yuda anapanga chilichonse Yehova analamulira Mose, 23 pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, wa luso la zopangapanga ndi kulemba mapulani, ndi wopanga nsalu zolukidwa bwino za mtundu wa mtambo, yapepo ndi zofiira, zofewa ndi zosalala. 24 Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika. 25 Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika. 26 Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550. 27 Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi. 28 Makilogalamu otsalawo anagwiritsa ntchito popanga ngowe zamzati kukutira pamwamba pa mizati ndiponso kupanga zingwe zake. 29 Mkuwa ochokera ku nsembe yoweyula unali makilogalamu 2,425. 30 Iwo anawugwiritsa ntchito popanga matsinde a pa chipata cha tenti ya msonkhano, guwa la mkuwa pamodzi ndi sefa yake ndiponso ziwiya zonse, 31 matsinde ozungulira bwalo ndiponso a pa chipata pake, ndi zikhomo zonse za tentiyo ndi matsinde a malo wozungulirapo.

In Other Versions

Exodus 38 in the ANGEFD

Exodus 38 in the ANTPNG2D

Exodus 38 in the AS21

Exodus 38 in the BAGH

Exodus 38 in the BBPNG

Exodus 38 in the BBT1E

Exodus 38 in the BDS

Exodus 38 in the BEV

Exodus 38 in the BHAD

Exodus 38 in the BIB

Exodus 38 in the BLPT

Exodus 38 in the BNT

Exodus 38 in the BNTABOOT

Exodus 38 in the BNTLV

Exodus 38 in the BOATCB

Exodus 38 in the BOATCB2

Exodus 38 in the BOBCV

Exodus 38 in the BOCNT

Exodus 38 in the BOECS

Exodus 38 in the BOHCB

Exodus 38 in the BOHCV

Exodus 38 in the BOHLNT

Exodus 38 in the BOHNTLTAL

Exodus 38 in the BOICB

Exodus 38 in the BOILNTAP

Exodus 38 in the BOITCV

Exodus 38 in the BOKCV

Exodus 38 in the BOKCV2

Exodus 38 in the BOKHWOG

Exodus 38 in the BOKSSV

Exodus 38 in the BOLCB

Exodus 38 in the BOLCB2

Exodus 38 in the BOMCV

Exodus 38 in the BONAV

Exodus 38 in the BONCB

Exodus 38 in the BONLT

Exodus 38 in the BONUT2

Exodus 38 in the BOPLNT

Exodus 38 in the BOSCB

Exodus 38 in the BOSNC

Exodus 38 in the BOTLNT

Exodus 38 in the BOVCB

Exodus 38 in the BOYCB

Exodus 38 in the BPBB

Exodus 38 in the BPH

Exodus 38 in the BSB

Exodus 38 in the CCB

Exodus 38 in the CUV

Exodus 38 in the CUVS

Exodus 38 in the DBT

Exodus 38 in the DGDNT

Exodus 38 in the DHNT

Exodus 38 in the DNT

Exodus 38 in the ELBE

Exodus 38 in the EMTV

Exodus 38 in the ESV

Exodus 38 in the FBV

Exodus 38 in the FEB

Exodus 38 in the GGMNT

Exodus 38 in the GNT

Exodus 38 in the HARY

Exodus 38 in the HNT

Exodus 38 in the IRVA

Exodus 38 in the IRVB

Exodus 38 in the IRVG

Exodus 38 in the IRVH

Exodus 38 in the IRVK

Exodus 38 in the IRVM

Exodus 38 in the IRVM2

Exodus 38 in the IRVO

Exodus 38 in the IRVP

Exodus 38 in the IRVT

Exodus 38 in the IRVT2

Exodus 38 in the IRVU

Exodus 38 in the ISVN

Exodus 38 in the JSNT

Exodus 38 in the KAPI

Exodus 38 in the KBT1ETNIK

Exodus 38 in the KBV

Exodus 38 in the KJV

Exodus 38 in the KNFD

Exodus 38 in the LBA

Exodus 38 in the LBLA

Exodus 38 in the LNT

Exodus 38 in the LSV

Exodus 38 in the MAAL

Exodus 38 in the MBV

Exodus 38 in the MBV2

Exodus 38 in the MHNT

Exodus 38 in the MKNFD

Exodus 38 in the MNG

Exodus 38 in the MNT

Exodus 38 in the MNT2

Exodus 38 in the MRS1T

Exodus 38 in the NAA

Exodus 38 in the NASB

Exodus 38 in the NBLA

Exodus 38 in the NBS

Exodus 38 in the NBVTP

Exodus 38 in the NET2

Exodus 38 in the NIV11

Exodus 38 in the NNT

Exodus 38 in the NNT2

Exodus 38 in the NNT3

Exodus 38 in the PDDPT

Exodus 38 in the PFNT

Exodus 38 in the RMNT

Exodus 38 in the SBIAS

Exodus 38 in the SBIBS

Exodus 38 in the SBIBS2

Exodus 38 in the SBICS

Exodus 38 in the SBIDS

Exodus 38 in the SBIGS

Exodus 38 in the SBIHS

Exodus 38 in the SBIIS

Exodus 38 in the SBIIS2

Exodus 38 in the SBIIS3

Exodus 38 in the SBIKS

Exodus 38 in the SBIKS2

Exodus 38 in the SBIMS

Exodus 38 in the SBIOS

Exodus 38 in the SBIPS

Exodus 38 in the SBISS

Exodus 38 in the SBITS

Exodus 38 in the SBITS2

Exodus 38 in the SBITS3

Exodus 38 in the SBITS4

Exodus 38 in the SBIUS

Exodus 38 in the SBIVS

Exodus 38 in the SBT

Exodus 38 in the SBT1E

Exodus 38 in the SCHL

Exodus 38 in the SNT

Exodus 38 in the SUSU

Exodus 38 in the SUSU2

Exodus 38 in the SYNO

Exodus 38 in the TBIAOTANT

Exodus 38 in the TBT1E

Exodus 38 in the TBT1E2

Exodus 38 in the TFTIP

Exodus 38 in the TFTU

Exodus 38 in the TGNTATF3T

Exodus 38 in the THAI

Exodus 38 in the TNFD

Exodus 38 in the TNT

Exodus 38 in the TNTIK

Exodus 38 in the TNTIL

Exodus 38 in the TNTIN

Exodus 38 in the TNTIP

Exodus 38 in the TNTIZ

Exodus 38 in the TOMA

Exodus 38 in the TTENT

Exodus 38 in the UBG

Exodus 38 in the UGV

Exodus 38 in the UGV2

Exodus 38 in the UGV3

Exodus 38 in the VBL

Exodus 38 in the VDCC

Exodus 38 in the YALU

Exodus 38 in the YAPE

Exodus 38 in the YBVTP

Exodus 38 in the ZBP