Exodus 7 (BOGWICC)

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona ine ndakuyika kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mʼbale wako Aaroni adzakhala mneneri wako. 2 Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto. 3 Koma ndidzawumitsa mtima wa Farao, ndipo ngakhale nditachulukitsa zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa mu Igupto, 4 iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto. 5 Ndipo Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzatambasula dzanja langa kukantha Igupto ndi kutulutsa Aisraeli mʼdzikomo.” 6 Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova anawalamulira. 7 Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao. 8 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, 9 “Ngati Farao adzati kwa inu, ‘Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, ‘Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.” 10 Kotero Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kuchita monga momwe Yehova anawalamulira. Aaroni anaponya ndodo yake pansi patsogolo pa Farao ndi nduna zake ndipo inasanduka njoka. 11 Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. 12 Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo. 13 Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera. 14 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite. 15 Upite kwa Farao mmawa pamene azidzapita ku madzi. Ukamudikire mʼmbali mwa Nailo kuti ukakumane naye ndipo unyamule ndodo imene inasanduka njoka ija mʼdzanja lako. 16 Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere. 17 Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: 18 Nsomba za mu Nailo zidzafa, mtsinje udzanunkha ndipo Aigupto sadzatha kumwa madzi ake.’ ” 19 Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.” 20 Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi. 21 Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto. 22 Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu. 23 Mʼmalo mwake iye anatembenuka ndi kupita ku nyumba yake yaufumu ndipo zimenezi sanazilabadire. 24 Anthu onse a ku Igupto anayamba kukumba mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sanathe kumwa madzi a mu mtsinjemo. 25 Panapita masiku asanu ndi awiri Yehova atamenya madzi a mu mtsinje wa Nailo.

In Other Versions

Exodus 7 in the ANGEFD

Exodus 7 in the ANTPNG2D

Exodus 7 in the AS21

Exodus 7 in the BAGH

Exodus 7 in the BBPNG

Exodus 7 in the BBT1E

Exodus 7 in the BDS

Exodus 7 in the BEV

Exodus 7 in the BHAD

Exodus 7 in the BIB

Exodus 7 in the BLPT

Exodus 7 in the BNT

Exodus 7 in the BNTABOOT

Exodus 7 in the BNTLV

Exodus 7 in the BOATCB

Exodus 7 in the BOATCB2

Exodus 7 in the BOBCV

Exodus 7 in the BOCNT

Exodus 7 in the BOECS

Exodus 7 in the BOHCB

Exodus 7 in the BOHCV

Exodus 7 in the BOHLNT

Exodus 7 in the BOHNTLTAL

Exodus 7 in the BOICB

Exodus 7 in the BOILNTAP

Exodus 7 in the BOITCV

Exodus 7 in the BOKCV

Exodus 7 in the BOKCV2

Exodus 7 in the BOKHWOG

Exodus 7 in the BOKSSV

Exodus 7 in the BOLCB

Exodus 7 in the BOLCB2

Exodus 7 in the BOMCV

Exodus 7 in the BONAV

Exodus 7 in the BONCB

Exodus 7 in the BONLT

Exodus 7 in the BONUT2

Exodus 7 in the BOPLNT

Exodus 7 in the BOSCB

Exodus 7 in the BOSNC

Exodus 7 in the BOTLNT

Exodus 7 in the BOVCB

Exodus 7 in the BOYCB

Exodus 7 in the BPBB

Exodus 7 in the BPH

Exodus 7 in the BSB

Exodus 7 in the CCB

Exodus 7 in the CUV

Exodus 7 in the CUVS

Exodus 7 in the DBT

Exodus 7 in the DGDNT

Exodus 7 in the DHNT

Exodus 7 in the DNT

Exodus 7 in the ELBE

Exodus 7 in the EMTV

Exodus 7 in the ESV

Exodus 7 in the FBV

Exodus 7 in the FEB

Exodus 7 in the GGMNT

Exodus 7 in the GNT

Exodus 7 in the HARY

Exodus 7 in the HNT

Exodus 7 in the IRVA

Exodus 7 in the IRVB

Exodus 7 in the IRVG

Exodus 7 in the IRVH

Exodus 7 in the IRVK

Exodus 7 in the IRVM

Exodus 7 in the IRVM2

Exodus 7 in the IRVO

Exodus 7 in the IRVP

Exodus 7 in the IRVT

Exodus 7 in the IRVT2

Exodus 7 in the IRVU

Exodus 7 in the ISVN

Exodus 7 in the JSNT

Exodus 7 in the KAPI

Exodus 7 in the KBT1ETNIK

Exodus 7 in the KBV

Exodus 7 in the KJV

Exodus 7 in the KNFD

Exodus 7 in the LBA

Exodus 7 in the LBLA

Exodus 7 in the LNT

Exodus 7 in the LSV

Exodus 7 in the MAAL

Exodus 7 in the MBV

Exodus 7 in the MBV2

Exodus 7 in the MHNT

Exodus 7 in the MKNFD

Exodus 7 in the MNG

Exodus 7 in the MNT

Exodus 7 in the MNT2

Exodus 7 in the MRS1T

Exodus 7 in the NAA

Exodus 7 in the NASB

Exodus 7 in the NBLA

Exodus 7 in the NBS

Exodus 7 in the NBVTP

Exodus 7 in the NET2

Exodus 7 in the NIV11

Exodus 7 in the NNT

Exodus 7 in the NNT2

Exodus 7 in the NNT3

Exodus 7 in the PDDPT

Exodus 7 in the PFNT

Exodus 7 in the RMNT

Exodus 7 in the SBIAS

Exodus 7 in the SBIBS

Exodus 7 in the SBIBS2

Exodus 7 in the SBICS

Exodus 7 in the SBIDS

Exodus 7 in the SBIGS

Exodus 7 in the SBIHS

Exodus 7 in the SBIIS

Exodus 7 in the SBIIS2

Exodus 7 in the SBIIS3

Exodus 7 in the SBIKS

Exodus 7 in the SBIKS2

Exodus 7 in the SBIMS

Exodus 7 in the SBIOS

Exodus 7 in the SBIPS

Exodus 7 in the SBISS

Exodus 7 in the SBITS

Exodus 7 in the SBITS2

Exodus 7 in the SBITS3

Exodus 7 in the SBITS4

Exodus 7 in the SBIUS

Exodus 7 in the SBIVS

Exodus 7 in the SBT

Exodus 7 in the SBT1E

Exodus 7 in the SCHL

Exodus 7 in the SNT

Exodus 7 in the SUSU

Exodus 7 in the SUSU2

Exodus 7 in the SYNO

Exodus 7 in the TBIAOTANT

Exodus 7 in the TBT1E

Exodus 7 in the TBT1E2

Exodus 7 in the TFTIP

Exodus 7 in the TFTU

Exodus 7 in the TGNTATF3T

Exodus 7 in the THAI

Exodus 7 in the TNFD

Exodus 7 in the TNT

Exodus 7 in the TNTIK

Exodus 7 in the TNTIL

Exodus 7 in the TNTIN

Exodus 7 in the TNTIP

Exodus 7 in the TNTIZ

Exodus 7 in the TOMA

Exodus 7 in the TTENT

Exodus 7 in the UBG

Exodus 7 in the UGV

Exodus 7 in the UGV2

Exodus 7 in the UGV3

Exodus 7 in the VBL

Exodus 7 in the VDCC

Exodus 7 in the YALU

Exodus 7 in the YAPE

Exodus 7 in the YBVTP

Exodus 7 in the ZBP