Ezekiel 3 (BOGWICC)

1 Tsono Mulungu anandiwuza kuti, “Mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya kenaka upite ukayankhule ndi Aisraeli.” 2 Choncho ndinayasama ndipo anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye. 3 Kenaka Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsa kuti ukhute.” Choncho ndinadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi mʼkamwa mwanga. 4 Pamenepo Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita tsopano kwa Aisraeli ndipo ukawawuze mawu anga. 5 Sindikukutuma kwa anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, koma kwa Aisraeli. 6 Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, amene mawu ake sungawamvetse. Ndithu ndikanakutuma kwa iwowa, bwenzi iwo atakumvera. 7 Koma Aisraeli sadzakumvera chifukwa iwo sakufuna kumvera Ine. Paja Aisraeli onse ndi okanika ndiponso a mtima wowuma. 8 Tsono ine ndakhwimitsa nkhope yako mofanana ndi nkhope zawo. Ndalimbitsanso mutu wako mofanana ndi mitu yawo. 9 Ine ndidzakusandutsa wolimba ngati mwala wa dayimondi umene uposa thanthwe lina lililonse kulimba kwake. Usachite nawo mantha kapena kuopsedwa nawo. Paja anthuwa ndi awupandu.” 10 Anatinso, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetse bwino zimene ndikukuwuzazi ndipo mawu angawa uwasunge bwino mu mtima mwako. 11 Tsopano upite kwa Aisraeli anzako amene ali ku ukapolo ndipo ukayankhule nawo. ‘Kaya akamvera kaya sakamvera,’ koma uzikawawuza kuti, Ambuye Wamphamvuzonse akuti zakutizakuti.” 12 Pamenepo Mzimu unandinyamula ndipo kumbuyo kwanga ndinamva liwu lamphamvu ngati chivomerezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Yehova kumene Iye amakhala!” 13 Phokoso ndinkalimvalo linali la kugundana kwa mapiko a zamoyo ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, limene linkamveka ngati chivomerezi chachikulu. 14 Mzimu wa Yehova unandikweza ndi kundinyamula ndipo ndinachokapo ndili wowawidwa ndi wonyuka mu mtima. Ndipo dzanja la Yehova linali pa ine mwa mphamvu. 15 Choncho ndinafika kwa amene anali mu ukapolo ku Telabibu pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndinakhala pansi pakati pawo masiku asanu ndi awiri, ndili wothedwa nzeru kwambiri. 16 Atatha masiku asanu ndi awiriwo, Yehova anandiwuza kuti, 17 “Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza. 18 Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 19 Koma ukamuchenjeza munthu woyipa koma iye osatembenuka mtima kuleka zoyipa zake kapena kusiya njira zake zoyipa, munthuyo adzafa chifukwa cha uchimo wake koma iwe udzapulumutsa moyo wako. 20 “Ngati munthu wolungama asiya chilungamo chake ndi kuchita uchimo ndipo Ine nʼkumuyika mʼzoopsa, munthuyo adzafa ndithu. Popeza iwe sunamuchenjeze, adzafadi chifukwa cha tchimo ndipo chilungamo chake sichidzakumbukiridwa, koma ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 21 Koma ngati umuchenjeza munthu wolungama kuti asachimwe ndipo iye nʼkuleka kuchimwa adzakhala ndi moyo ndithu chifukwa anamvera chenjezo, ndipo iwe udzapulumutsa moyo wako.” 22 Nthawi ina dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandiwuza kuti, “Nyamuka upite ku chigwa, kumeneko ndikayankhula nawe.” 23 Choncho ndinanyamuka kupita ku chigwa. Ndipo ndinaona ulemerero wa Yehova kumeneko, ngati ulemerero umene ndinaona mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara ndipo ndinagwa pansi chafufumimba. 24 Koma Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa. Tsono Yehova anandiyankhula nati: “Pita, kadzitsekere mʼnyumba mwako. 25 Ndipo iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe motero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu. 26 Ndidzamatirira lilime lako kukhosi, kotero kuti udzakhala chete wosatha kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu aupandu. 27 Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.’ Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka.”

In Other Versions

Ezekiel 3 in the ANGEFD

Ezekiel 3 in the ANTPNG2D

Ezekiel 3 in the AS21

Ezekiel 3 in the BAGH

Ezekiel 3 in the BBPNG

Ezekiel 3 in the BBT1E

Ezekiel 3 in the BDS

Ezekiel 3 in the BEV

Ezekiel 3 in the BHAD

Ezekiel 3 in the BIB

Ezekiel 3 in the BLPT

Ezekiel 3 in the BNT

Ezekiel 3 in the BNTABOOT

Ezekiel 3 in the BNTLV

Ezekiel 3 in the BOATCB

Ezekiel 3 in the BOATCB2

Ezekiel 3 in the BOBCV

Ezekiel 3 in the BOCNT

Ezekiel 3 in the BOECS

Ezekiel 3 in the BOHCB

Ezekiel 3 in the BOHCV

Ezekiel 3 in the BOHLNT

Ezekiel 3 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 3 in the BOICB

Ezekiel 3 in the BOILNTAP

Ezekiel 3 in the BOITCV

Ezekiel 3 in the BOKCV

Ezekiel 3 in the BOKCV2

Ezekiel 3 in the BOKHWOG

Ezekiel 3 in the BOKSSV

Ezekiel 3 in the BOLCB

Ezekiel 3 in the BOLCB2

Ezekiel 3 in the BOMCV

Ezekiel 3 in the BONAV

Ezekiel 3 in the BONCB

Ezekiel 3 in the BONLT

Ezekiel 3 in the BONUT2

Ezekiel 3 in the BOPLNT

Ezekiel 3 in the BOSCB

Ezekiel 3 in the BOSNC

Ezekiel 3 in the BOTLNT

Ezekiel 3 in the BOVCB

Ezekiel 3 in the BOYCB

Ezekiel 3 in the BPBB

Ezekiel 3 in the BPH

Ezekiel 3 in the BSB

Ezekiel 3 in the CCB

Ezekiel 3 in the CUV

Ezekiel 3 in the CUVS

Ezekiel 3 in the DBT

Ezekiel 3 in the DGDNT

Ezekiel 3 in the DHNT

Ezekiel 3 in the DNT

Ezekiel 3 in the ELBE

Ezekiel 3 in the EMTV

Ezekiel 3 in the ESV

Ezekiel 3 in the FBV

Ezekiel 3 in the FEB

Ezekiel 3 in the GGMNT

Ezekiel 3 in the GNT

Ezekiel 3 in the HARY

Ezekiel 3 in the HNT

Ezekiel 3 in the IRVA

Ezekiel 3 in the IRVB

Ezekiel 3 in the IRVG

Ezekiel 3 in the IRVH

Ezekiel 3 in the IRVK

Ezekiel 3 in the IRVM

Ezekiel 3 in the IRVM2

Ezekiel 3 in the IRVO

Ezekiel 3 in the IRVP

Ezekiel 3 in the IRVT

Ezekiel 3 in the IRVT2

Ezekiel 3 in the IRVU

Ezekiel 3 in the ISVN

Ezekiel 3 in the JSNT

Ezekiel 3 in the KAPI

Ezekiel 3 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 3 in the KBV

Ezekiel 3 in the KJV

Ezekiel 3 in the KNFD

Ezekiel 3 in the LBA

Ezekiel 3 in the LBLA

Ezekiel 3 in the LNT

Ezekiel 3 in the LSV

Ezekiel 3 in the MAAL

Ezekiel 3 in the MBV

Ezekiel 3 in the MBV2

Ezekiel 3 in the MHNT

Ezekiel 3 in the MKNFD

Ezekiel 3 in the MNG

Ezekiel 3 in the MNT

Ezekiel 3 in the MNT2

Ezekiel 3 in the MRS1T

Ezekiel 3 in the NAA

Ezekiel 3 in the NASB

Ezekiel 3 in the NBLA

Ezekiel 3 in the NBS

Ezekiel 3 in the NBVTP

Ezekiel 3 in the NET2

Ezekiel 3 in the NIV11

Ezekiel 3 in the NNT

Ezekiel 3 in the NNT2

Ezekiel 3 in the NNT3

Ezekiel 3 in the PDDPT

Ezekiel 3 in the PFNT

Ezekiel 3 in the RMNT

Ezekiel 3 in the SBIAS

Ezekiel 3 in the SBIBS

Ezekiel 3 in the SBIBS2

Ezekiel 3 in the SBICS

Ezekiel 3 in the SBIDS

Ezekiel 3 in the SBIGS

Ezekiel 3 in the SBIHS

Ezekiel 3 in the SBIIS

Ezekiel 3 in the SBIIS2

Ezekiel 3 in the SBIIS3

Ezekiel 3 in the SBIKS

Ezekiel 3 in the SBIKS2

Ezekiel 3 in the SBIMS

Ezekiel 3 in the SBIOS

Ezekiel 3 in the SBIPS

Ezekiel 3 in the SBISS

Ezekiel 3 in the SBITS

Ezekiel 3 in the SBITS2

Ezekiel 3 in the SBITS3

Ezekiel 3 in the SBITS4

Ezekiel 3 in the SBIUS

Ezekiel 3 in the SBIVS

Ezekiel 3 in the SBT

Ezekiel 3 in the SBT1E

Ezekiel 3 in the SCHL

Ezekiel 3 in the SNT

Ezekiel 3 in the SUSU

Ezekiel 3 in the SUSU2

Ezekiel 3 in the SYNO

Ezekiel 3 in the TBIAOTANT

Ezekiel 3 in the TBT1E

Ezekiel 3 in the TBT1E2

Ezekiel 3 in the TFTIP

Ezekiel 3 in the TFTU

Ezekiel 3 in the TGNTATF3T

Ezekiel 3 in the THAI

Ezekiel 3 in the TNFD

Ezekiel 3 in the TNT

Ezekiel 3 in the TNTIK

Ezekiel 3 in the TNTIL

Ezekiel 3 in the TNTIN

Ezekiel 3 in the TNTIP

Ezekiel 3 in the TNTIZ

Ezekiel 3 in the TOMA

Ezekiel 3 in the TTENT

Ezekiel 3 in the UBG

Ezekiel 3 in the UGV

Ezekiel 3 in the UGV2

Ezekiel 3 in the UGV3

Ezekiel 3 in the VBL

Ezekiel 3 in the VDCC

Ezekiel 3 in the YALU

Ezekiel 3 in the YAPE

Ezekiel 3 in the YBVTP

Ezekiel 3 in the ZBP