Ezekiel 32 (BOGWICC)

1 Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,“Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu.Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja.Umakhuvula mʼmitsinje yako,kuvundula madzi ndi mapazi akondi kudetsa madzi mʼmitsinje. 3 “Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,“ ‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri,ndidzakuponyera khoka langandi kukugwira mu ukonde wanga. 4 Ndidzakuponya ku mtundandi kukutayira pansi.Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe,ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya. 5 Ndidzayanika mnofu wako pa mapirindipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako. 6 Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,mpaka kumapiri komwe,ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako. 7 Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyambandikudetsa nyenyezi zake.Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo,ndipo mwezi sudzawala. 8 Zowala zonse zamumlengalengandidzazizimitsa;ndidzachititsa mdima pa dziko lako,akutero Ambuye Yehova. 9 Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiripamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,ku mayiko amene iwe sunawadziwe. 10 Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwepamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo.Pa nthawi ya kugwa kwako,aliyense wa iwo adzanjenjemeramoyo wake wonse. 11 “ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,“ ‘Lupanga la mfumu ya ku Babulonilidzabwera kudzalimbana nawe. 12 Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwendi lupanga la anthu amphamvu,anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu.Adzathetsa kunyada kwa Igupto,ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa. 13 Ndidzawononga ziweto zake zonsezokhala mʼmbali mwa madzi ambiri.Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthukapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto. 14 Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi akendipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta,akutero Ambuye Yehova. 15 Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;ndikadzawononga dziko lonsendi kukantha onse okhala kumeneko,adzadziwa kuti ndine Yehova.’ 16 “Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.” 17 Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa. 19 Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’ 20 Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo. 21 Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’ 22 “Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo. 23 Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga. 24 “Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. 25 Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa. 26 “Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. 27 Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo. 28 “Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga. 29 “Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje. 30 “Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda. 31 “Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 32 Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

In Other Versions

Ezekiel 32 in the ANGEFD

Ezekiel 32 in the ANTPNG2D

Ezekiel 32 in the AS21

Ezekiel 32 in the BAGH

Ezekiel 32 in the BBPNG

Ezekiel 32 in the BBT1E

Ezekiel 32 in the BDS

Ezekiel 32 in the BEV

Ezekiel 32 in the BHAD

Ezekiel 32 in the BIB

Ezekiel 32 in the BLPT

Ezekiel 32 in the BNT

Ezekiel 32 in the BNTABOOT

Ezekiel 32 in the BNTLV

Ezekiel 32 in the BOATCB

Ezekiel 32 in the BOATCB2

Ezekiel 32 in the BOBCV

Ezekiel 32 in the BOCNT

Ezekiel 32 in the BOECS

Ezekiel 32 in the BOHCB

Ezekiel 32 in the BOHCV

Ezekiel 32 in the BOHLNT

Ezekiel 32 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 32 in the BOICB

Ezekiel 32 in the BOILNTAP

Ezekiel 32 in the BOITCV

Ezekiel 32 in the BOKCV

Ezekiel 32 in the BOKCV2

Ezekiel 32 in the BOKHWOG

Ezekiel 32 in the BOKSSV

Ezekiel 32 in the BOLCB

Ezekiel 32 in the BOLCB2

Ezekiel 32 in the BOMCV

Ezekiel 32 in the BONAV

Ezekiel 32 in the BONCB

Ezekiel 32 in the BONLT

Ezekiel 32 in the BONUT2

Ezekiel 32 in the BOPLNT

Ezekiel 32 in the BOSCB

Ezekiel 32 in the BOSNC

Ezekiel 32 in the BOTLNT

Ezekiel 32 in the BOVCB

Ezekiel 32 in the BOYCB

Ezekiel 32 in the BPBB

Ezekiel 32 in the BPH

Ezekiel 32 in the BSB

Ezekiel 32 in the CCB

Ezekiel 32 in the CUV

Ezekiel 32 in the CUVS

Ezekiel 32 in the DBT

Ezekiel 32 in the DGDNT

Ezekiel 32 in the DHNT

Ezekiel 32 in the DNT

Ezekiel 32 in the ELBE

Ezekiel 32 in the EMTV

Ezekiel 32 in the ESV

Ezekiel 32 in the FBV

Ezekiel 32 in the FEB

Ezekiel 32 in the GGMNT

Ezekiel 32 in the GNT

Ezekiel 32 in the HARY

Ezekiel 32 in the HNT

Ezekiel 32 in the IRVA

Ezekiel 32 in the IRVB

Ezekiel 32 in the IRVG

Ezekiel 32 in the IRVH

Ezekiel 32 in the IRVK

Ezekiel 32 in the IRVM

Ezekiel 32 in the IRVM2

Ezekiel 32 in the IRVO

Ezekiel 32 in the IRVP

Ezekiel 32 in the IRVT

Ezekiel 32 in the IRVT2

Ezekiel 32 in the IRVU

Ezekiel 32 in the ISVN

Ezekiel 32 in the JSNT

Ezekiel 32 in the KAPI

Ezekiel 32 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 32 in the KBV

Ezekiel 32 in the KJV

Ezekiel 32 in the KNFD

Ezekiel 32 in the LBA

Ezekiel 32 in the LBLA

Ezekiel 32 in the LNT

Ezekiel 32 in the LSV

Ezekiel 32 in the MAAL

Ezekiel 32 in the MBV

Ezekiel 32 in the MBV2

Ezekiel 32 in the MHNT

Ezekiel 32 in the MKNFD

Ezekiel 32 in the MNG

Ezekiel 32 in the MNT

Ezekiel 32 in the MNT2

Ezekiel 32 in the MRS1T

Ezekiel 32 in the NAA

Ezekiel 32 in the NASB

Ezekiel 32 in the NBLA

Ezekiel 32 in the NBS

Ezekiel 32 in the NBVTP

Ezekiel 32 in the NET2

Ezekiel 32 in the NIV11

Ezekiel 32 in the NNT

Ezekiel 32 in the NNT2

Ezekiel 32 in the NNT3

Ezekiel 32 in the PDDPT

Ezekiel 32 in the PFNT

Ezekiel 32 in the RMNT

Ezekiel 32 in the SBIAS

Ezekiel 32 in the SBIBS

Ezekiel 32 in the SBIBS2

Ezekiel 32 in the SBICS

Ezekiel 32 in the SBIDS

Ezekiel 32 in the SBIGS

Ezekiel 32 in the SBIHS

Ezekiel 32 in the SBIIS

Ezekiel 32 in the SBIIS2

Ezekiel 32 in the SBIIS3

Ezekiel 32 in the SBIKS

Ezekiel 32 in the SBIKS2

Ezekiel 32 in the SBIMS

Ezekiel 32 in the SBIOS

Ezekiel 32 in the SBIPS

Ezekiel 32 in the SBISS

Ezekiel 32 in the SBITS

Ezekiel 32 in the SBITS2

Ezekiel 32 in the SBITS3

Ezekiel 32 in the SBITS4

Ezekiel 32 in the SBIUS

Ezekiel 32 in the SBIVS

Ezekiel 32 in the SBT

Ezekiel 32 in the SBT1E

Ezekiel 32 in the SCHL

Ezekiel 32 in the SNT

Ezekiel 32 in the SUSU

Ezekiel 32 in the SUSU2

Ezekiel 32 in the SYNO

Ezekiel 32 in the TBIAOTANT

Ezekiel 32 in the TBT1E

Ezekiel 32 in the TBT1E2

Ezekiel 32 in the TFTIP

Ezekiel 32 in the TFTU

Ezekiel 32 in the TGNTATF3T

Ezekiel 32 in the THAI

Ezekiel 32 in the TNFD

Ezekiel 32 in the TNT

Ezekiel 32 in the TNTIK

Ezekiel 32 in the TNTIL

Ezekiel 32 in the TNTIN

Ezekiel 32 in the TNTIP

Ezekiel 32 in the TNTIZ

Ezekiel 32 in the TOMA

Ezekiel 32 in the TTENT

Ezekiel 32 in the UBG

Ezekiel 32 in the UGV

Ezekiel 32 in the UGV2

Ezekiel 32 in the UGV3

Ezekiel 32 in the VBL

Ezekiel 32 in the VDCC

Ezekiel 32 in the YALU

Ezekiel 32 in the YAPE

Ezekiel 32 in the YBVTP

Ezekiel 32 in the ZBP