Genesis 11 (BOGWICC)
1 Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi. 2 Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako. 3 Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. 4 Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.” 5 Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. 6 Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. 7 Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.” 8 Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. 9 Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi. 10 Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. 11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 12 Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. 13 Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. 15 Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 16 Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. 17 Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 18 Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. 19 Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 20 Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21 Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 22 Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. 23 Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 24 Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. 25 Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi. 26 Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. 27 Nayi mibado yochokera mwa Tera. Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. 28 Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. 29 Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. 30 Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka. 31 Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko. 32 Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.
In Other Versions
Genesis 11 in the ANGEFD
Genesis 11 in the ANTPNG2D
Genesis 11 in the AS21
Genesis 11 in the BAGH
Genesis 11 in the BBPNG
Genesis 11 in the BBT1E
Genesis 11 in the BDS
Genesis 11 in the BEV
Genesis 11 in the BHAD
Genesis 11 in the BIB
Genesis 11 in the BLPT
Genesis 11 in the BNT
Genesis 11 in the BNTABOOT
Genesis 11 in the BNTLV
Genesis 11 in the BOATCB
Genesis 11 in the BOATCB2
Genesis 11 in the BOBCV
Genesis 11 in the BOCNT
Genesis 11 in the BOECS
Genesis 11 in the BOHCB
Genesis 11 in the BOHCV
Genesis 11 in the BOHLNT
Genesis 11 in the BOHNTLTAL
Genesis 11 in the BOICB
Genesis 11 in the BOILNTAP
Genesis 11 in the BOITCV
Genesis 11 in the BOKCV
Genesis 11 in the BOKCV2
Genesis 11 in the BOKHWOG
Genesis 11 in the BOKSSV
Genesis 11 in the BOLCB
Genesis 11 in the BOLCB2
Genesis 11 in the BOMCV
Genesis 11 in the BONAV
Genesis 11 in the BONCB
Genesis 11 in the BONLT
Genesis 11 in the BONUT2
Genesis 11 in the BOPLNT
Genesis 11 in the BOSCB
Genesis 11 in the BOSNC
Genesis 11 in the BOTLNT
Genesis 11 in the BOVCB
Genesis 11 in the BOYCB
Genesis 11 in the BPBB
Genesis 11 in the BPH
Genesis 11 in the BSB
Genesis 11 in the CCB
Genesis 11 in the CUV
Genesis 11 in the CUVS
Genesis 11 in the DBT
Genesis 11 in the DGDNT
Genesis 11 in the DHNT
Genesis 11 in the DNT
Genesis 11 in the ELBE
Genesis 11 in the EMTV
Genesis 11 in the ESV
Genesis 11 in the FBV
Genesis 11 in the FEB
Genesis 11 in the GGMNT
Genesis 11 in the GNT
Genesis 11 in the HARY
Genesis 11 in the HNT
Genesis 11 in the IRVA
Genesis 11 in the IRVB
Genesis 11 in the IRVG
Genesis 11 in the IRVH
Genesis 11 in the IRVK
Genesis 11 in the IRVM
Genesis 11 in the IRVM2
Genesis 11 in the IRVO
Genesis 11 in the IRVP
Genesis 11 in the IRVT
Genesis 11 in the IRVT2
Genesis 11 in the IRVU
Genesis 11 in the ISVN
Genesis 11 in the JSNT
Genesis 11 in the KAPI
Genesis 11 in the KBT1ETNIK
Genesis 11 in the KBV
Genesis 11 in the KJV
Genesis 11 in the KNFD
Genesis 11 in the LBA
Genesis 11 in the LBLA
Genesis 11 in the LNT
Genesis 11 in the LSV
Genesis 11 in the MAAL
Genesis 11 in the MBV
Genesis 11 in the MBV2
Genesis 11 in the MHNT
Genesis 11 in the MKNFD
Genesis 11 in the MNG
Genesis 11 in the MNT
Genesis 11 in the MNT2
Genesis 11 in the MRS1T
Genesis 11 in the NAA
Genesis 11 in the NASB
Genesis 11 in the NBLA
Genesis 11 in the NBS
Genesis 11 in the NBVTP
Genesis 11 in the NET2
Genesis 11 in the NIV11
Genesis 11 in the NNT
Genesis 11 in the NNT2
Genesis 11 in the NNT3
Genesis 11 in the PDDPT
Genesis 11 in the PFNT
Genesis 11 in the RMNT
Genesis 11 in the SBIAS
Genesis 11 in the SBIBS
Genesis 11 in the SBIBS2
Genesis 11 in the SBICS
Genesis 11 in the SBIDS
Genesis 11 in the SBIGS
Genesis 11 in the SBIHS
Genesis 11 in the SBIIS
Genesis 11 in the SBIIS2
Genesis 11 in the SBIIS3
Genesis 11 in the SBIKS
Genesis 11 in the SBIKS2
Genesis 11 in the SBIMS
Genesis 11 in the SBIOS
Genesis 11 in the SBIPS
Genesis 11 in the SBISS
Genesis 11 in the SBITS
Genesis 11 in the SBITS2
Genesis 11 in the SBITS3
Genesis 11 in the SBITS4
Genesis 11 in the SBIUS
Genesis 11 in the SBIVS
Genesis 11 in the SBT
Genesis 11 in the SBT1E
Genesis 11 in the SCHL
Genesis 11 in the SNT
Genesis 11 in the SUSU
Genesis 11 in the SUSU2
Genesis 11 in the SYNO
Genesis 11 in the TBIAOTANT
Genesis 11 in the TBT1E
Genesis 11 in the TBT1E2
Genesis 11 in the TFTIP
Genesis 11 in the TFTU
Genesis 11 in the TGNTATF3T
Genesis 11 in the THAI
Genesis 11 in the TNFD
Genesis 11 in the TNT
Genesis 11 in the TNTIK
Genesis 11 in the TNTIL
Genesis 11 in the TNTIN
Genesis 11 in the TNTIP
Genesis 11 in the TNTIZ
Genesis 11 in the TOMA
Genesis 11 in the TTENT
Genesis 11 in the UBG
Genesis 11 in the UGV
Genesis 11 in the UGV2
Genesis 11 in the UGV3
Genesis 11 in the VBL
Genesis 11 in the VDCC
Genesis 11 in the YALU
Genesis 11 in the YAPE
Genesis 11 in the YBVTP
Genesis 11 in the ZBP