Genesis 14 (BOGWICC)
1 Pa nthawi imeneyi Amarafeli mfumu ya Sinara, Arioki mfumu ya Elasara, Kedorilaomere mfumu ya Elamu ndi Tidala mfumu ya Goimu 2 anathira nkhondo Bera mfumu ya ku Sodomu, Birisa mfumu ya Gomora, Sinabi mfumu ya Adima, Semeberi mfumu ya Ziboimu ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). 3 Mafumu onse anathiridwa nkhondowa anagwirizana pamodzi kupita ku Chigwa cha Sidimu (Nyanja ya Mchere). 4 Kwa zaka khumi ndi ziwiri anali pansi pa ulamuliro wa Kedorilaomere, koma mʼchaka cha khumi ndi chitatu anamuwukira. 5 Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu 6 amene ankakhala ku Ahori, ku dziko la mapiri la Seiri mpaka ku Eli Parani kufupi ndi chipululu. 7 Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara. 8 Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo 9 Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu. 10 Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri. 11 Mafumu anayi aja anatenga katundu yense ndi chakudya chonse cha ku Sodomu ndi Gomora napita nazo. 12 Anatenganso Loti, mwana wa mʼbale wake wa Abramu pamodzi ndi katundu wake popeza ankakhala mu Sodomu. 13 Koma munthu wina amene anathawa, anabwera kudzamufotokozera Abramu Mhebri. Tsono Abramu ankakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya Mamre wa fuko la Aamori, mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri. Onsewa anali pa mgwirizano ndi Abramu. 14 Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani. 15 Pa nthawi ya usiku Abramu anawagawa asilikali ake kuti athire nkhondo mafumu aja, ndipo anawakantha nawapirikitsa mpaka ku Hoba, cha kumpoto kwa Damasiko. 16 Ndipo anawalanda katundu wawo yense nabwera naye Loti, katundu wake yense, pamodzi ndi akazi ndi anthu ena. 17 Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu). 18 Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba, 19 ndipo anadalitsa Abramu nati,“Mulungu Wammwambamwamba,wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu. 20 Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwambaamene anapereka adani ako mʼdzanja lako.”Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo. 21 Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, “Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.” 22 Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, “Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira 23 kuti sindidzalandira kanthu kalikonse kako, ngakhale utakhala ulusi chabe kapena chingwe cha nsapato, kuopa kuti ungamanene kuti, ‘Ndamulemeretsa Abramu.’ 24 Sindidzalandira kanthu kalikonse kupatula zokhazo zimene anthu anga adya ndi gawo la katundu la anthu amene ndinapita nawo monga Aneri, Esikolo ndi Mamre. Iwowa atenge gawo lawo.”
In Other Versions
Genesis 14 in the ANGEFD
Genesis 14 in the ANTPNG2D
Genesis 14 in the AS21
Genesis 14 in the BAGH
Genesis 14 in the BBPNG
Genesis 14 in the BBT1E
Genesis 14 in the BDS
Genesis 14 in the BEV
Genesis 14 in the BHAD
Genesis 14 in the BIB
Genesis 14 in the BLPT
Genesis 14 in the BNT
Genesis 14 in the BNTABOOT
Genesis 14 in the BNTLV
Genesis 14 in the BOATCB
Genesis 14 in the BOATCB2
Genesis 14 in the BOBCV
Genesis 14 in the BOCNT
Genesis 14 in the BOECS
Genesis 14 in the BOHCB
Genesis 14 in the BOHCV
Genesis 14 in the BOHLNT
Genesis 14 in the BOHNTLTAL
Genesis 14 in the BOICB
Genesis 14 in the BOILNTAP
Genesis 14 in the BOITCV
Genesis 14 in the BOKCV
Genesis 14 in the BOKCV2
Genesis 14 in the BOKHWOG
Genesis 14 in the BOKSSV
Genesis 14 in the BOLCB
Genesis 14 in the BOLCB2
Genesis 14 in the BOMCV
Genesis 14 in the BONAV
Genesis 14 in the BONCB
Genesis 14 in the BONLT
Genesis 14 in the BONUT2
Genesis 14 in the BOPLNT
Genesis 14 in the BOSCB
Genesis 14 in the BOSNC
Genesis 14 in the BOTLNT
Genesis 14 in the BOVCB
Genesis 14 in the BOYCB
Genesis 14 in the BPBB
Genesis 14 in the BPH
Genesis 14 in the BSB
Genesis 14 in the CCB
Genesis 14 in the CUV
Genesis 14 in the CUVS
Genesis 14 in the DBT
Genesis 14 in the DGDNT
Genesis 14 in the DHNT
Genesis 14 in the DNT
Genesis 14 in the ELBE
Genesis 14 in the EMTV
Genesis 14 in the ESV
Genesis 14 in the FBV
Genesis 14 in the FEB
Genesis 14 in the GGMNT
Genesis 14 in the GNT
Genesis 14 in the HARY
Genesis 14 in the HNT
Genesis 14 in the IRVA
Genesis 14 in the IRVB
Genesis 14 in the IRVG
Genesis 14 in the IRVH
Genesis 14 in the IRVK
Genesis 14 in the IRVM
Genesis 14 in the IRVM2
Genesis 14 in the IRVO
Genesis 14 in the IRVP
Genesis 14 in the IRVT
Genesis 14 in the IRVT2
Genesis 14 in the IRVU
Genesis 14 in the ISVN
Genesis 14 in the JSNT
Genesis 14 in the KAPI
Genesis 14 in the KBT1ETNIK
Genesis 14 in the KBV
Genesis 14 in the KJV
Genesis 14 in the KNFD
Genesis 14 in the LBA
Genesis 14 in the LBLA
Genesis 14 in the LNT
Genesis 14 in the LSV
Genesis 14 in the MAAL
Genesis 14 in the MBV
Genesis 14 in the MBV2
Genesis 14 in the MHNT
Genesis 14 in the MKNFD
Genesis 14 in the MNG
Genesis 14 in the MNT
Genesis 14 in the MNT2
Genesis 14 in the MRS1T
Genesis 14 in the NAA
Genesis 14 in the NASB
Genesis 14 in the NBLA
Genesis 14 in the NBS
Genesis 14 in the NBVTP
Genesis 14 in the NET2
Genesis 14 in the NIV11
Genesis 14 in the NNT
Genesis 14 in the NNT2
Genesis 14 in the NNT3
Genesis 14 in the PDDPT
Genesis 14 in the PFNT
Genesis 14 in the RMNT
Genesis 14 in the SBIAS
Genesis 14 in the SBIBS
Genesis 14 in the SBIBS2
Genesis 14 in the SBICS
Genesis 14 in the SBIDS
Genesis 14 in the SBIGS
Genesis 14 in the SBIHS
Genesis 14 in the SBIIS
Genesis 14 in the SBIIS2
Genesis 14 in the SBIIS3
Genesis 14 in the SBIKS
Genesis 14 in the SBIKS2
Genesis 14 in the SBIMS
Genesis 14 in the SBIOS
Genesis 14 in the SBIPS
Genesis 14 in the SBISS
Genesis 14 in the SBITS
Genesis 14 in the SBITS2
Genesis 14 in the SBITS3
Genesis 14 in the SBITS4
Genesis 14 in the SBIUS
Genesis 14 in the SBIVS
Genesis 14 in the SBT
Genesis 14 in the SBT1E
Genesis 14 in the SCHL
Genesis 14 in the SNT
Genesis 14 in the SUSU
Genesis 14 in the SUSU2
Genesis 14 in the SYNO
Genesis 14 in the TBIAOTANT
Genesis 14 in the TBT1E
Genesis 14 in the TBT1E2
Genesis 14 in the TFTIP
Genesis 14 in the TFTU
Genesis 14 in the TGNTATF3T
Genesis 14 in the THAI
Genesis 14 in the TNFD
Genesis 14 in the TNT
Genesis 14 in the TNTIK
Genesis 14 in the TNTIL
Genesis 14 in the TNTIN
Genesis 14 in the TNTIP
Genesis 14 in the TNTIZ
Genesis 14 in the TOMA
Genesis 14 in the TTENT
Genesis 14 in the UBG
Genesis 14 in the UGV
Genesis 14 in the UGV2
Genesis 14 in the UGV3
Genesis 14 in the VBL
Genesis 14 in the VDCC
Genesis 14 in the YALU
Genesis 14 in the YAPE
Genesis 14 in the YBVTP
Genesis 14 in the ZBP