Hebrews 3 (BOGWICC)
1 Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza. 2 Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu. 3 Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo. 4 Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu. 5 Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo. 6 Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo. 7 Tsono monga Mzimu Woyera akuti,“Lero mukamva mawu ake, 8 musawumitse mitima yanungati munachitira pamene munawukira,pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu. 9 Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa,ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita. 10 Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo,ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera,ndipo iwo sadziwa njira zanga.’ 11 Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti,‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ” 12 Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo. 13 Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo. 14 Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi. 15 Monga kunanenedwa kuti,“Lero ngati mumva mawu ake,musawumitse mitima yanungati momwe munachitira pamene munawukira.” 16 Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto? 17 Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja? 18 Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja. 19 Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.
In Other Versions
Hebrews 3 in the ANGEFD
Hebrews 3 in the ANTPNG2D
Hebrews 3 in the AS21
Hebrews 3 in the BAGH
Hebrews 3 in the BBPNG
Hebrews 3 in the BBT1E
Hebrews 3 in the BDS
Hebrews 3 in the BEV
Hebrews 3 in the BHAD
Hebrews 3 in the BIB
Hebrews 3 in the BLPT
Hebrews 3 in the BNT
Hebrews 3 in the BNTABOOT
Hebrews 3 in the BNTLV
Hebrews 3 in the BOATCB
Hebrews 3 in the BOATCB2
Hebrews 3 in the BOBCV
Hebrews 3 in the BOCNT
Hebrews 3 in the BOECS
Hebrews 3 in the BOHCB
Hebrews 3 in the BOHCV
Hebrews 3 in the BOHLNT
Hebrews 3 in the BOHNTLTAL
Hebrews 3 in the BOICB
Hebrews 3 in the BOILNTAP
Hebrews 3 in the BOITCV
Hebrews 3 in the BOKCV
Hebrews 3 in the BOKCV2
Hebrews 3 in the BOKHWOG
Hebrews 3 in the BOKSSV
Hebrews 3 in the BOLCB
Hebrews 3 in the BOLCB2
Hebrews 3 in the BOMCV
Hebrews 3 in the BONAV
Hebrews 3 in the BONCB
Hebrews 3 in the BONLT
Hebrews 3 in the BONUT2
Hebrews 3 in the BOPLNT
Hebrews 3 in the BOSCB
Hebrews 3 in the BOSNC
Hebrews 3 in the BOTLNT
Hebrews 3 in the BOVCB
Hebrews 3 in the BOYCB
Hebrews 3 in the BPBB
Hebrews 3 in the BPH
Hebrews 3 in the BSB
Hebrews 3 in the CCB
Hebrews 3 in the CUV
Hebrews 3 in the CUVS
Hebrews 3 in the DBT
Hebrews 3 in the DGDNT
Hebrews 3 in the DHNT
Hebrews 3 in the DNT
Hebrews 3 in the ELBE
Hebrews 3 in the EMTV
Hebrews 3 in the ESV
Hebrews 3 in the FBV
Hebrews 3 in the FEB
Hebrews 3 in the GGMNT
Hebrews 3 in the GNT
Hebrews 3 in the HARY
Hebrews 3 in the HNT
Hebrews 3 in the IRVA
Hebrews 3 in the IRVB
Hebrews 3 in the IRVG
Hebrews 3 in the IRVH
Hebrews 3 in the IRVK
Hebrews 3 in the IRVM
Hebrews 3 in the IRVM2
Hebrews 3 in the IRVO
Hebrews 3 in the IRVP
Hebrews 3 in the IRVT
Hebrews 3 in the IRVT2
Hebrews 3 in the IRVU
Hebrews 3 in the ISVN
Hebrews 3 in the JSNT
Hebrews 3 in the KAPI
Hebrews 3 in the KBT1ETNIK
Hebrews 3 in the KBV
Hebrews 3 in the KJV
Hebrews 3 in the KNFD
Hebrews 3 in the LBA
Hebrews 3 in the LBLA
Hebrews 3 in the LNT
Hebrews 3 in the LSV
Hebrews 3 in the MAAL
Hebrews 3 in the MBV
Hebrews 3 in the MBV2
Hebrews 3 in the MHNT
Hebrews 3 in the MKNFD
Hebrews 3 in the MNG
Hebrews 3 in the MNT
Hebrews 3 in the MNT2
Hebrews 3 in the MRS1T
Hebrews 3 in the NAA
Hebrews 3 in the NASB
Hebrews 3 in the NBLA
Hebrews 3 in the NBS
Hebrews 3 in the NBVTP
Hebrews 3 in the NET2
Hebrews 3 in the NIV11
Hebrews 3 in the NNT
Hebrews 3 in the NNT2
Hebrews 3 in the NNT3
Hebrews 3 in the PDDPT
Hebrews 3 in the PFNT
Hebrews 3 in the RMNT
Hebrews 3 in the SBIAS
Hebrews 3 in the SBIBS
Hebrews 3 in the SBIBS2
Hebrews 3 in the SBICS
Hebrews 3 in the SBIDS
Hebrews 3 in the SBIGS
Hebrews 3 in the SBIHS
Hebrews 3 in the SBIIS
Hebrews 3 in the SBIIS2
Hebrews 3 in the SBIIS3
Hebrews 3 in the SBIKS
Hebrews 3 in the SBIKS2
Hebrews 3 in the SBIMS
Hebrews 3 in the SBIOS
Hebrews 3 in the SBIPS
Hebrews 3 in the SBISS
Hebrews 3 in the SBITS
Hebrews 3 in the SBITS2
Hebrews 3 in the SBITS3
Hebrews 3 in the SBITS4
Hebrews 3 in the SBIUS
Hebrews 3 in the SBIVS
Hebrews 3 in the SBT
Hebrews 3 in the SBT1E
Hebrews 3 in the SCHL
Hebrews 3 in the SNT
Hebrews 3 in the SUSU
Hebrews 3 in the SUSU2
Hebrews 3 in the SYNO
Hebrews 3 in the TBIAOTANT
Hebrews 3 in the TBT1E
Hebrews 3 in the TBT1E2
Hebrews 3 in the TFTIP
Hebrews 3 in the TFTU
Hebrews 3 in the TGNTATF3T
Hebrews 3 in the THAI
Hebrews 3 in the TNFD
Hebrews 3 in the TNT
Hebrews 3 in the TNTIK
Hebrews 3 in the TNTIL
Hebrews 3 in the TNTIN
Hebrews 3 in the TNTIP
Hebrews 3 in the TNTIZ
Hebrews 3 in the TOMA
Hebrews 3 in the TTENT
Hebrews 3 in the UBG
Hebrews 3 in the UGV
Hebrews 3 in the UGV2
Hebrews 3 in the UGV3
Hebrews 3 in the VBL
Hebrews 3 in the VDCC
Hebrews 3 in the YALU
Hebrews 3 in the YAPE
Hebrews 3 in the YBVTP
Hebrews 3 in the ZBP