Isaiah 19 (BOGWICC)

1 Uthenga onena za Igupto:Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro,ndipo akupita ku Igupto.Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake,ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha. 2 “Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha;mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake,mnansi ndi mnansi wake,mzinda ndi mzinda unzake,ndiponso ufumu ndi ufumu unzake. 3 Aigupto adzataya mtimapopeza ndidzalepheretsa zolinga zawo;adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa,kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu. 4 Ndidzawapereka Aiguptokwa olamulira ankhanza,ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,”akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse. 5 Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa,ndipo mʼmbali mwa mtsinje mudzangʼaluka ndi kuwuma. 6 Ngalande zake zidzanunkha;ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma.Bango ndi dulu zidzafota, 7 ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailondi ku mathiriro a mtsinjewo.Zonse zodzalidwa mʼmbali mwa Nailozidzawuma, zidzawuluzika ndipo sizidzaonekanso. 8 Asodzi adzabuwula ndi kudandaula,onse amene amaponya mbedza mu Nailo;onse amene amaponya makoka mʼmadziadzalira. 9 Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima,anthu oluka nsalu zofewa zabafuta adzataya chiyembekezo. 10 Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi,ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu. 11 Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru;aphungu a nzeru a Farao amalangiza zopusa.Kodi mungathe kunena bwanji kwa Farao kuti,“Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru,wophunzira wa mafumu akale?” 12 Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti?Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsazimene Yehova Wamphamvuzonsewakonza kuchitira dziko la Igupto. 13 Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru,atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa;atsogoleri a dziko la Iguptoasocheretsa anthu a dzikolo. 14 Yehova wasocheretsaanthu a ku Igupto.Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita,ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake. 15 Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite,mtsogoleri kapena wotsatira, nthambi ya kanjedza kapena bango. 16 Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga. 17 Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto. 18 Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo. 19 Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso. 20 Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa. 21 Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo. 22 Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa. 23 Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi. 24 Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi. 25 Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”

In Other Versions

Isaiah 19 in the ANGEFD

Isaiah 19 in the ANTPNG2D

Isaiah 19 in the AS21

Isaiah 19 in the BAGH

Isaiah 19 in the BBPNG

Isaiah 19 in the BBT1E

Isaiah 19 in the BDS

Isaiah 19 in the BEV

Isaiah 19 in the BHAD

Isaiah 19 in the BIB

Isaiah 19 in the BLPT

Isaiah 19 in the BNT

Isaiah 19 in the BNTABOOT

Isaiah 19 in the BNTLV

Isaiah 19 in the BOATCB

Isaiah 19 in the BOATCB2

Isaiah 19 in the BOBCV

Isaiah 19 in the BOCNT

Isaiah 19 in the BOECS

Isaiah 19 in the BOHCB

Isaiah 19 in the BOHCV

Isaiah 19 in the BOHLNT

Isaiah 19 in the BOHNTLTAL

Isaiah 19 in the BOICB

Isaiah 19 in the BOILNTAP

Isaiah 19 in the BOITCV

Isaiah 19 in the BOKCV

Isaiah 19 in the BOKCV2

Isaiah 19 in the BOKHWOG

Isaiah 19 in the BOKSSV

Isaiah 19 in the BOLCB

Isaiah 19 in the BOLCB2

Isaiah 19 in the BOMCV

Isaiah 19 in the BONAV

Isaiah 19 in the BONCB

Isaiah 19 in the BONLT

Isaiah 19 in the BONUT2

Isaiah 19 in the BOPLNT

Isaiah 19 in the BOSCB

Isaiah 19 in the BOSNC

Isaiah 19 in the BOTLNT

Isaiah 19 in the BOVCB

Isaiah 19 in the BOYCB

Isaiah 19 in the BPBB

Isaiah 19 in the BPH

Isaiah 19 in the BSB

Isaiah 19 in the CCB

Isaiah 19 in the CUV

Isaiah 19 in the CUVS

Isaiah 19 in the DBT

Isaiah 19 in the DGDNT

Isaiah 19 in the DHNT

Isaiah 19 in the DNT

Isaiah 19 in the ELBE

Isaiah 19 in the EMTV

Isaiah 19 in the ESV

Isaiah 19 in the FBV

Isaiah 19 in the FEB

Isaiah 19 in the GGMNT

Isaiah 19 in the GNT

Isaiah 19 in the HARY

Isaiah 19 in the HNT

Isaiah 19 in the IRVA

Isaiah 19 in the IRVB

Isaiah 19 in the IRVG

Isaiah 19 in the IRVH

Isaiah 19 in the IRVK

Isaiah 19 in the IRVM

Isaiah 19 in the IRVM2

Isaiah 19 in the IRVO

Isaiah 19 in the IRVP

Isaiah 19 in the IRVT

Isaiah 19 in the IRVT2

Isaiah 19 in the IRVU

Isaiah 19 in the ISVN

Isaiah 19 in the JSNT

Isaiah 19 in the KAPI

Isaiah 19 in the KBT1ETNIK

Isaiah 19 in the KBV

Isaiah 19 in the KJV

Isaiah 19 in the KNFD

Isaiah 19 in the LBA

Isaiah 19 in the LBLA

Isaiah 19 in the LNT

Isaiah 19 in the LSV

Isaiah 19 in the MAAL

Isaiah 19 in the MBV

Isaiah 19 in the MBV2

Isaiah 19 in the MHNT

Isaiah 19 in the MKNFD

Isaiah 19 in the MNG

Isaiah 19 in the MNT

Isaiah 19 in the MNT2

Isaiah 19 in the MRS1T

Isaiah 19 in the NAA

Isaiah 19 in the NASB

Isaiah 19 in the NBLA

Isaiah 19 in the NBS

Isaiah 19 in the NBVTP

Isaiah 19 in the NET2

Isaiah 19 in the NIV11

Isaiah 19 in the NNT

Isaiah 19 in the NNT2

Isaiah 19 in the NNT3

Isaiah 19 in the PDDPT

Isaiah 19 in the PFNT

Isaiah 19 in the RMNT

Isaiah 19 in the SBIAS

Isaiah 19 in the SBIBS

Isaiah 19 in the SBIBS2

Isaiah 19 in the SBICS

Isaiah 19 in the SBIDS

Isaiah 19 in the SBIGS

Isaiah 19 in the SBIHS

Isaiah 19 in the SBIIS

Isaiah 19 in the SBIIS2

Isaiah 19 in the SBIIS3

Isaiah 19 in the SBIKS

Isaiah 19 in the SBIKS2

Isaiah 19 in the SBIMS

Isaiah 19 in the SBIOS

Isaiah 19 in the SBIPS

Isaiah 19 in the SBISS

Isaiah 19 in the SBITS

Isaiah 19 in the SBITS2

Isaiah 19 in the SBITS3

Isaiah 19 in the SBITS4

Isaiah 19 in the SBIUS

Isaiah 19 in the SBIVS

Isaiah 19 in the SBT

Isaiah 19 in the SBT1E

Isaiah 19 in the SCHL

Isaiah 19 in the SNT

Isaiah 19 in the SUSU

Isaiah 19 in the SUSU2

Isaiah 19 in the SYNO

Isaiah 19 in the TBIAOTANT

Isaiah 19 in the TBT1E

Isaiah 19 in the TBT1E2

Isaiah 19 in the TFTIP

Isaiah 19 in the TFTU

Isaiah 19 in the TGNTATF3T

Isaiah 19 in the THAI

Isaiah 19 in the TNFD

Isaiah 19 in the TNT

Isaiah 19 in the TNTIK

Isaiah 19 in the TNTIL

Isaiah 19 in the TNTIN

Isaiah 19 in the TNTIP

Isaiah 19 in the TNTIZ

Isaiah 19 in the TOMA

Isaiah 19 in the TTENT

Isaiah 19 in the UBG

Isaiah 19 in the UGV

Isaiah 19 in the UGV2

Isaiah 19 in the UGV3

Isaiah 19 in the VBL

Isaiah 19 in the VDCC

Isaiah 19 in the YALU

Isaiah 19 in the YAPE

Isaiah 19 in the YBVTP

Isaiah 19 in the ZBP