Isaiah 33 (BOGWICC)
1 Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,amene sunawonongedwepo!Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,iwe amene sunanyengedwepo!Iwe ukadzaleka kuwononga,udzawonongedwa,ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga. 2 Inu Yehova, mutikomere mtima ife;tikulakalaka Inu.Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso. 3 Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika. 4 Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe. 5 Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonseadzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso. 6 Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;kuopa Yehova ngati madalitso. 7 Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu;akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri. 8 Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.Mdaniyo ndi wosasunga pangano.Iye amanyoza mboni.Palibe kulemekezana. 9 Dziko likulira ndipo likunka likutha.Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka. 10 Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatukandipo ndidzaonetsa mphamvu zanga,ndipo ndidzakwezedwa. 11 Zolingalira zanu nʼzachabechabengati udzu wamanyowa.Mpweya wamoto udzakupserezani. 12 Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza;ndi ngati minga yodulidwa.” 13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita;inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga 14 Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha;anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera:Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa?Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?” 15 Angathe kuti ndi amene amachita zolungamandi kuyankhula zoona,amene amakana phindu lolipeza monyengandipo salola manja ake kulandira ziphuphu,amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawondipo amatsinzina kuti angaone zoyipa. 16 Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja,kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri.Azidzalandira chakudya chakendipo madzi sadzamusowa. 17 Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongolandi kuona dziko lotambasukira kutali. 18 Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:“Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?Ali kuti wokhometsa misonkho uja?Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?” 19 Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,anthu aja achiyankhulo chosadziwika,chachilendo ndi chosamveka. 20 Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;maso anu adzaona Yerusalemu,mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,zikhomo zake sizidzazulidwa,kapena zingwe zake kuduka. 21 Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wakendipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo. 22 Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,Yehova ndiye wotilamulira,Yehova ndiye mfumu yathu;ndipo ndiye amene adzatipulumutse. 23 Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka,sizikutha kulimbitsa mlongoti wake,matanga ake sakutheka kutambasuka.Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambirindipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo. 24 Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala”ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.
In Other Versions
Isaiah 33 in the ANGEFD
Isaiah 33 in the ANTPNG2D
Isaiah 33 in the AS21
Isaiah 33 in the BAGH
Isaiah 33 in the BBPNG
Isaiah 33 in the BBT1E
Isaiah 33 in the BDS
Isaiah 33 in the BEV
Isaiah 33 in the BHAD
Isaiah 33 in the BIB
Isaiah 33 in the BLPT
Isaiah 33 in the BNT
Isaiah 33 in the BNTABOOT
Isaiah 33 in the BNTLV
Isaiah 33 in the BOATCB
Isaiah 33 in the BOATCB2
Isaiah 33 in the BOBCV
Isaiah 33 in the BOCNT
Isaiah 33 in the BOECS
Isaiah 33 in the BOHCB
Isaiah 33 in the BOHCV
Isaiah 33 in the BOHLNT
Isaiah 33 in the BOHNTLTAL
Isaiah 33 in the BOICB
Isaiah 33 in the BOILNTAP
Isaiah 33 in the BOITCV
Isaiah 33 in the BOKCV
Isaiah 33 in the BOKCV2
Isaiah 33 in the BOKHWOG
Isaiah 33 in the BOKSSV
Isaiah 33 in the BOLCB
Isaiah 33 in the BOLCB2
Isaiah 33 in the BOMCV
Isaiah 33 in the BONAV
Isaiah 33 in the BONCB
Isaiah 33 in the BONLT
Isaiah 33 in the BONUT2
Isaiah 33 in the BOPLNT
Isaiah 33 in the BOSCB
Isaiah 33 in the BOSNC
Isaiah 33 in the BOTLNT
Isaiah 33 in the BOVCB
Isaiah 33 in the BOYCB
Isaiah 33 in the BPBB
Isaiah 33 in the BPH
Isaiah 33 in the BSB
Isaiah 33 in the CCB
Isaiah 33 in the CUV
Isaiah 33 in the CUVS
Isaiah 33 in the DBT
Isaiah 33 in the DGDNT
Isaiah 33 in the DHNT
Isaiah 33 in the DNT
Isaiah 33 in the ELBE
Isaiah 33 in the EMTV
Isaiah 33 in the ESV
Isaiah 33 in the FBV
Isaiah 33 in the FEB
Isaiah 33 in the GGMNT
Isaiah 33 in the GNT
Isaiah 33 in the HARY
Isaiah 33 in the HNT
Isaiah 33 in the IRVA
Isaiah 33 in the IRVB
Isaiah 33 in the IRVG
Isaiah 33 in the IRVH
Isaiah 33 in the IRVK
Isaiah 33 in the IRVM
Isaiah 33 in the IRVM2
Isaiah 33 in the IRVO
Isaiah 33 in the IRVP
Isaiah 33 in the IRVT
Isaiah 33 in the IRVT2
Isaiah 33 in the IRVU
Isaiah 33 in the ISVN
Isaiah 33 in the JSNT
Isaiah 33 in the KAPI
Isaiah 33 in the KBT1ETNIK
Isaiah 33 in the KBV
Isaiah 33 in the KJV
Isaiah 33 in the KNFD
Isaiah 33 in the LBA
Isaiah 33 in the LBLA
Isaiah 33 in the LNT
Isaiah 33 in the LSV
Isaiah 33 in the MAAL
Isaiah 33 in the MBV
Isaiah 33 in the MBV2
Isaiah 33 in the MHNT
Isaiah 33 in the MKNFD
Isaiah 33 in the MNG
Isaiah 33 in the MNT
Isaiah 33 in the MNT2
Isaiah 33 in the MRS1T
Isaiah 33 in the NAA
Isaiah 33 in the NASB
Isaiah 33 in the NBLA
Isaiah 33 in the NBS
Isaiah 33 in the NBVTP
Isaiah 33 in the NET2
Isaiah 33 in the NIV11
Isaiah 33 in the NNT
Isaiah 33 in the NNT2
Isaiah 33 in the NNT3
Isaiah 33 in the PDDPT
Isaiah 33 in the PFNT
Isaiah 33 in the RMNT
Isaiah 33 in the SBIAS
Isaiah 33 in the SBIBS
Isaiah 33 in the SBIBS2
Isaiah 33 in the SBICS
Isaiah 33 in the SBIDS
Isaiah 33 in the SBIGS
Isaiah 33 in the SBIHS
Isaiah 33 in the SBIIS
Isaiah 33 in the SBIIS2
Isaiah 33 in the SBIIS3
Isaiah 33 in the SBIKS
Isaiah 33 in the SBIKS2
Isaiah 33 in the SBIMS
Isaiah 33 in the SBIOS
Isaiah 33 in the SBIPS
Isaiah 33 in the SBISS
Isaiah 33 in the SBITS
Isaiah 33 in the SBITS2
Isaiah 33 in the SBITS3
Isaiah 33 in the SBITS4
Isaiah 33 in the SBIUS
Isaiah 33 in the SBIVS
Isaiah 33 in the SBT
Isaiah 33 in the SBT1E
Isaiah 33 in the SCHL
Isaiah 33 in the SNT
Isaiah 33 in the SUSU
Isaiah 33 in the SUSU2
Isaiah 33 in the SYNO
Isaiah 33 in the TBIAOTANT
Isaiah 33 in the TBT1E
Isaiah 33 in the TBT1E2
Isaiah 33 in the TFTIP
Isaiah 33 in the TFTU
Isaiah 33 in the TGNTATF3T
Isaiah 33 in the THAI
Isaiah 33 in the TNFD
Isaiah 33 in the TNT
Isaiah 33 in the TNTIK
Isaiah 33 in the TNTIL
Isaiah 33 in the TNTIN
Isaiah 33 in the TNTIP
Isaiah 33 in the TNTIZ
Isaiah 33 in the TOMA
Isaiah 33 in the TTENT
Isaiah 33 in the UBG
Isaiah 33 in the UGV
Isaiah 33 in the UGV2
Isaiah 33 in the UGV3
Isaiah 33 in the VBL
Isaiah 33 in the VDCC
Isaiah 33 in the YALU
Isaiah 33 in the YAPE
Isaiah 33 in the YBVTP
Isaiah 33 in the ZBP